Gen. 17:12-13

Gen. 17:12-13 BLY-DC

Muziwumbala mwana wamwamuna aliyense akakwanitsa masiku asanu ndi atatu. Muziwumbala mwamuna aliyense pa mibadwo yanu yonse, mbadwa kapena kapolo amene mudamgula kwa mlendo wosakhala wa mbumba yanu. Inde aliyense aumbalidwe, ndipo chimenechi chidzakhala chizindikiro pa matupi anu, choonetsa kuti chipangano changa ndi inu nchamuyaya.