Gen. 16
16
1Sarai mkazi wa Abramu, sadam'balire ana Abramuyo. Koma Sarai anali ndi mdzakazi wake wa ku Ejipito dzina lake Hagara. 2Tsono Sarai adauza Abramu kuti, “Chauta sadandipatse ana. Bwanji osati muloŵane ndi mdzakazi wangayu kuti kapena nkundibalira mwana?” Abramu adavomereza zimenezo. 3Motero Sarai adapereka Hagara uja kwa Abramu, kuti akhale mkazi wake wamng'ono. (Zimenezi zidachitika Abramu atakhala ku Kanani zaka khumi). 4Abramu ataloŵana ndi Hagara, Hagarayo adatenga pathupi ndipo pompo Hagara adayamba kudzitama, namanyoza Sarai. 5Tsiku lina Sarai adauza Abramu kuti, “Cholakwa chimenechi chakuti Hagara akundinyoza, chili pa inu. Ine ndidakupatsani mdzakazi ameneyu, ndipo kuyambira paja adatenga pathupipa, wakhala akundinyoza. Chauta ndiye aweruze kuti tiwone wolakwa ndani pakati pathu.” 6Abramu adayankha kuti, “Iyeyu ndi mdzakazi wako, ndipo ali mu ulamuliro wako. Chita naye chilichonse chomwe ufuna.” Choncho Sarai adayamba kuzunza Hagara, mpaka Hagarayo adathaŵa.
7Mngelo wa Chauta adakumana naye pa chitsime m'chipululu, pa mseu wopita ku Suri. 8Ndipo adati, “Iwe Hagara, mdzakazi wa Sarai, kodi ukuchokera kuti, nanga ukupita kuti?” Iye adayankha kuti “Ndikuthaŵa mbuyanga Sarai.” 9Mngelo wa Chautayo adati, “Iyai, bwerera kwa Sarai, ukamgonjere. 10Ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka, zosaŵerengeka.” 11Popitiriza mau mngeloyo adati,
“Tsopano uli pafupi kukhala ndi mwana wamwamuna,
udzamutche Ismaele,
ndiye kuti Chauta wamva kulira kwako pa zovuta zako.
12Koma mwana wako adzakhala ndi mtima wa chilombo,
adzadana ndi aliyense,
ndipo anthu onse adzadana naye.
Adzakhala akudana ndi abale ake onse.”
13Tsono Hagara adatcha Chauta amene adalankhula naye kuti, “Inu ndinu Mulungu wondipenya,” poti adati, “Pano ndamuwona Iye amene amandipenya.” 14Nchifukwa chake anthu amachitchula chitsime cha pakati pa Kadesi ndi Beredi kuti Chitsime cha Wamoyo-Wondipenya.
15 #
Aga. 4.22
Tsono Hagara adamubalira Abramu mwana wamwamuna, namutcha dzina loti Ismaele. 16Abramu anali wa zake 86 pa nthaŵi imeneyo.
Jelenleg kiválasztva:
Gen. 16: BLY-DC
Kiemelés
Megosztás
Másolás
Szeretnéd, hogy a kiemeléseid minden eszközödön megjelenjenek? Regisztrálj vagy jelentkezz be
Bible Society of Malawi