Gen. 38
38
Yuda ndi Tamara
1Nthaŵi imeneyo Yuda adachoka nakakhala kwa munthu wina wa fuko la Adulamu dzina lake Hira. 2Kumeneko Yuda adaonako mtsikana Wachikanani, mwana wa Suwa, namkwatira. 3Mkaziyo adatenga pathupi nabala mwana wamwamuna, nkumutcha Ere. 4Adatenganso pena pathupi nabala mwana wamwamuna, nkumutcha Onani. 5Adabalanso mwana wina wamwamuna, namutcha Sela. Pamene Sela ankabadwa, nkuti Yuda ali ku Kezibu. 6Yuda adampezera mkazi mwana wake wachisamba uja Ere, dzina lake Tamara. 7Koma makhalidwe oipa a Ere adaipira Chauta, mwakuti Chauta adamlanga ndi imfa. 8Motero Yuda adauza Onani kuti, “Loŵana naye mkazi wamasiye wa mbale wakoyu. Uloŵe chokolo ndithu, kuti mbale wakoyo akhale ndi ana.” 9Koma Onani adaadziŵa kuti anawo sadzakhala ake. Motero nthaŵi zonse akamakhala naye mkaziyo, ankangotayira pansi mbeu yake, kuti asamubalire ana mbale wakeyo. 10Tsono zimene ankachitazo zidaipira Chauta ndipo Chauta adamlanganso ndi imfa. 11Apo Yuda adauza mpongozi wake uja Tamara kuti, “Bwererani kunyumba kwa bambo wanu, mukakhale wamasiye kumeneko mpaka mwana wanga Sela atakula.” Adanena zimenezi chifukwa ankaopa kuti Sela angafenso monga abale akewo. Motero Tamara adabwerera kunyumba kwa bambo wake.
12Patapita nthaŵi, mkazi wa Yuda uja, mwana wa Suwa, adamwalira. Tsono Yuda atatha kulira malirowo, iyeyo pamodzi ndi bwenzi lake Hira Mwadulamu, adapita ku Timna kumene ankameta nkhosa zake. 13Munthu wina adauza Tamara kuti, “Apongozi ako akupita ku Timna kukameta nkhosa.” 14Tsono Tamarayo adasintha zovala zake zaumasiye zija navala zina. Adadziphimba kumaso ndi nsalu, nakakhala pansi pa chipata cha ku Enaimu. Mudzi wa Enaimu unali pa mseu wopita ku Timna. Adaadziŵa kuti pa nthaŵiyo nkuti Sela atakula, komabe Tamara anali asanamloŵe chokolo Sela uja. 15Yuda atamuwona, adaamuyesa mkazi wadama, chifukwa anali atadziphimba kumaso. 16Adapita ku mbali ya mseu komwe kunali iyeyo namuuza kuti, “Kodi mungandilole kuti ndigone nanu?” Yuda sankadziŵa kuti ndi mpongozi wake. Mkaziyo adati, “Mudzandipatsa chiyani?” 17Yuda adayankha kuti, “Ndidzakutumizira mbuzi yaing'ono ya m'khola mwanga.” Tsono Tamarayo adati, “Chabwino, ndivomera mukandipatsa chikole choti mpaka mudzanditumizire.” 18Yuda adamufunsa kuti, “Kodi ukufuna chikole chotani?” Tamara adayankha kuti, “Mundipatse mphete yanu pamodzi ndi chingwe chanu chomwecho, ndi ndodo yanu yoyendera imene ili m'manja mwanuyi.” Yuda adapereka zonsezo kwa Tamara. Atatero Yuda adagona naye mkaziyo, ndipo adatenga pathupi. 19Tsono Tamara adanyamuka nachokapo. Adachotsa nsalu imene adaadziphimba nayo kumaso ija, navalanso zovala zake zaumasiye zija.
20Pambuyo pake Yuda adatuma bwenzi lake kukapereka mbuzi ija, kuti mkazi uja amubwezere zikole zija. Koma bwenzi lakeyo sadakampeze mkaziyo. 21Adafunsa anthu akomweko kuti, “Kodi mkazi wadama amene ankakhala pambali pa mseu wopita ku Enaimu uja ali kuti?” Anthuwo adayankha kuti, “Chikhalire sipadakhale mkazi wadama pa malo amenewo.” 22Adabwerera kwa Yuda nakamuuza kuti, “Sindidampeze mkazi uja, ndipo anthu akumeneko andiwuza kuti, ‘Chikhalire sipadakhale mkazi wadama pa malo amenewo.’ ” 23Yuda adati, “Zinthu zimenezo atenge zikhale zake, kuwopa kuti anthu angadzatiseke. Ngakhale sudampeze mkaziyo, komabe ine ndidaamtumizira ndithu mbuziyi.”
24Patapita miyezi itatu, munthu wina adauza Yuda kuti, “Mpongozi wanu uja Tamara adachita chigololo, ndipo ali ndi pathupi.” Pomwepo Yuda adalamula kuti, “Kamtengeni ndipo mukamtenthe kuti afe.” 25Akutengedwa kumene, Tamarayo adatumiza mau kwa Yuda mpongozi wake kuti, “Ine ndili ndi pathupi pa mwiniwake zinthu izi. Taziyang'anani, muwone mwina inu nkumudziŵa mwiniwakeyo kuti ndani: mpheteyi ndi chingwechi ndiponso ndodo yoyenderayi.” 26Yuda atazizindikira zinthuzo adati, “Akunenetsadi. Ndine amene ndidalakwa. Bwenzi nditampereka kwa mwana wanga Sela kuti amkwatire.” Choncho Yuda sadagone nayenso mkaziyo.
27Itakwana nthaŵi yakuti Tamara achire, m'mimba mwake munali mapasa. 28Pa nthaŵi yochira, mmodzi mwa anawo adatulutsa dzanja. Mzamba adaligwira, nalimanga ndi chingwe chofiira nati, “Ameneyu ndiye woyamba kubadwa.” 29Koma mwanayo adalibweza dzanja lake, mwakuti mbale wake ndiye adayambira kubadwa. Tsono mzamba uja adati, “Uchita kudziphothyolera wekha chotere!” Motero mwanayo adatchedwa Perezi. 30Pambuyo pake mbale wake adabadwa chingwe chofiira chija chili lende ku dzanja. Tsono iyeyu adatchedwa Zera.
Currently Selected:
Gen. 38: BLY-DC
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi