Gen. 37
37
Yosefe ndi abale ake
1Yakobe adakhalabe ku dziko la Kanani kumene bambo wake ankakhala. 2Mbiri ya banja la Yakobe ndi iyi: Pamene Yosefe anali mnyamata wa zaka 17, ankaŵeta nkhosa ndi mbuzi pamodzi ndi abale ake, ana a Biliha aja ndi a Zilipa, akazi aang'ono a bambo wake. Tsono Yosefeyo ankauza bambo wake zoipa zimene ankachita abale akewo.
3Israele ankakonda Yosefe kupambana ana ake ena onse, popeza kuti anali mwana wake wapaukalamba. Adamsokera mkanjo wautali wamanja.
4Abale ake ataona kuti bambo wao ankakonda Yosefe kupambana iwowo, adayamba kudana naye Yosefeyo, ndipo sankalankhula naye mokondwa.
5Tsiku lina Yosefe adalota maloto, nafotokozera abale ake malotowo. Zitatero, adadana naye kopambana kale. 6Iye adaŵauza kuti “Mverani maloto omwe ndalota. 7Tonsefe tinali m'munda, ndipo tinalikumanga mitolo yatirigu. Tilikumanga chomwecho, mtolo wanga unaimirira. Tsono mitolo yanu inauzungulira mtolo wangawo ndi kumauŵeramira.” 8Apo abale akewo adamufunsa kuti, “Kodi ukuganiza kuti udzakhala mfumu yathu? Kodi ndiye kuti iweyo nkudzatilamula ife?” Motero adadana naye koposa kale chifukwa cha malotowo ndi mau akewo. 9Tsono Yosefe adalotanso ena maloto, nauzanso abale akewo kuti, “Ndalotanso, ndipo ndaona dzuŵa, mwezi ndi nyenyezi khumi ndi imodzi zikundiŵeramira.” 10Maloto ameneŵa adauzanso bambo wake pamodzi ndi abale ake omwe aja. Atate ake adamdzudzula, adati, “Kodi maloto ameneŵa ngotani? Kodi ukuganiza kuti ine, mai wakoyu pamodzi ndi abale akoŵa, tidzakugwadira iwe?” 11#Ntc. 7.9Tsono abale ake aja adachita naye kaduka kwambiri. Koma atate ake ankakhala akuziganiza zimenezi.
Yosefe agulitsidwa ku Ejipito
12Tsiku lina abale ake a Yosefe adapita ku Sekemu kukaŵeta nkhosa za bambo wao. 13Israele adauza Yosefe kuti, “Abale ako akuŵeta nkhosa ku Sekemu. Ndikufuna kuti upite kwa iwowo.” Yosefe adayankha kuti, “Chabwino, atate.” 14Tsono bambo wakeyo adamuuza kuti, “Pita ukaŵaone abale ako m'mene aliri, ndiponso ngati zoŵeta zili bwino, kenaka udzandiwuze.” Choncho bambo wake adatuma Yosefe kuchokera ku chigwa cha Hebroni.
Yosefe atafika ku Sekemu, 15munthu wina adampeza akungoyendayenda m'deralo namufunsa kuti, “Kodi ukufunafuna chiyani?” Yosefe adayankha kuti, 16“Ndikufunafuna abale anga. Chonde tandiwuzani kumene akuŵeta nkhosa.” 17Munthuyo adati, “Adachoka kale kuno. Ndidaŵamva akunena kuti akupita ku Dotani.” Apo Yosefe adaŵalondola abale akewo, nakaŵapeza ku Dotani. 18Abale ake aja adamuwonera kutali, iye asanayandikire nkomwe pamene panali iwopo. Adayamba kumpangira chiwembu natsimikiza zoti amuphe. 19Onsewo ankauzana kuti, “Uyotu kamaloto uja, akudza apoyo! 20Tiyeni timuphe, mtembo wake tiwuponye m'chitsime china mwa zitsime zili apazi. Tizikanena kuti wajiwa ndi chilombo, ndipo tidzaone tanthauzo lake la maloto ake aja.” 21Tsono Rubeni adamva zimene enawo ankanena, ndipo adayesetsa kumpulumutsa Yosefe. Adati, “Ai tisamuphe, tisakhetse magazi ake. 22Tingomuponya m'chitsime chopanda madzichi kuchipululu konkuno. Tisampweteke konse.” Ankanena zimenezi akuganiza zomupulumutsa m'manja mwao, kuti amtumize kwa bambo wake. 23Yosefe atafika kumene kunali abale akewo, iwowo adamuvula mkanjo wake, uja wautali wamanjawu umene adaavala, 24namtenga, nkumuponya m'chitsime chopanda madzi.
25Pamene iwo ankadya, adaona gulu la Aismaele akuchokera ku Giliyadi. Ngamira zao zinali zitasenza nzonono ndi zonunkhira zimene ankapita nazo ku Ejipito. 26Tsono Yuda adafunsa abale ake kuti, “Kodi tipindulanji tikamupha mbale wathuyu ndi kubisa, osaulula kuti tamupha? 27Tiyeni timgulitse kwa Aismaeleŵa. Nanga iyeyu si mbale wathu, thupi limodzi ndiponso magazi amodzi?” Abale akewo adavomereza zimenezo. 28#Lun. 10.13; Ntc. 7.9Tsono Amidiyani ena amalonda adafika pomwepo. Abale akewo adamtulutsa Yosefeyo m'chitsime muja, namgulitsa kwa Aismaelewo pamtengo wokwana masekeli a siliva makumi aŵiri, ndipo iwowo adapita naye ku Ejipito.
29Rubeni atabwerera kuchitsime kuja, adapeza muli ng'waa! Pomwepo adang'amba zovala zake chifukwa cha chisoni. 30Ndipo adabwerera kwa abale ake aja naŵauza kuti, “Mnyamata ujatu palibe! Tsono ine ndichite chiyani?” 31Pomwepo iwo adapha mbuzi, naviika mkanjo wa Yosefe uja m'magazi ake. 32Adatenga mkanjowo napita nawo kwa bambo wao, nati, “Tayang'anani, kapena nkukhala mkanjo wa mwana wanu uja.” 33Yakobe adauzindikira mkanjowo, nati, “Ha, ndi wakedi! Chilombo chamupha mwana wanga. Kalanga ine, Yosefe wakadzulidwa!” 34Yakobe adang'amba zovala zake, navala chiguduli m'chiwuno, chifukwa cha chisoni. Adalira maliro a mwana wakeyo nthaŵi yaitali. 35Ana ake onse aamuna ndi aakazi, adabwera kuti amtonthoze koma iye adakana, adati, “Ndidzakhala ndikulira mwana wanga mpaka kumanda komwe kuli iyeko.” Choncho adapitirirabe kulira chifukwa cha Yosefe mwana wake. 36Nthaŵi imeneyo nkuti Amidiyani aja atamgulitsa Yosefe kwa Potifara ku Ejipito. Potifarayo anali mmodzi mwa nduna za Farao, ndipo anali mkulu wa asilikali olonda kunyumba kwa Farao.
Currently Selected:
Gen. 37: BLY-DC
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi