YouVersion Logo
Search Icon

Gen. 36

36
Zidzukulu za Esau
(1 Mbi. 1.34-37)
1Nazi zidzukulu za Esau, amene ankatchedwanso Edomu. 2#Gen. 26.34 Esau adaakwatira akazi Achikanani aŵa: Ada mwana wa Eloni Muhiti, Oholibama mwana wa Ana, mwana wa Zibiyoni Muhivi, 3#Gen. 28.9 ndi Basemati mwana wa Ismaele, mlongo wa Nebayoti. 4Ada adamubalira Esau Elifazi. Basemati adabala Reuele 5ndipo Oholibama adabala Yeusi, Yalamu ndi Kora. Ameneŵa ndi ana amene adabereka Esau m'dziko la Kanani.
6Tsono Esau adatenga akazi ake, ana ake aamuna, ana ake aakazi ndi anthu onse a m'nyumba mwake, pamodzi ndi zoŵeta zake zonse, ndi katundu wake yense amene adampeza ku dziko la Kanani, ndipo adasiyana ndi mbale wake uja Yakobe, napita kukakhala ku dziko lina. 7Chimene adachokera ndi chakuti dziko limene ankakhalako iye pamodzi ndi Yakobe, silinkaŵakwanira aŵiriwo. Anali ndi zoŵeta zochuluka zedi, mwakuti sikudatheke kuti iwo akhale pa malo amodzi. 8Motero Esau adakakhala m'dziko lamapiri ku Edomu.
9Nazi zidzukulu za Esau, kholo la Aedomu, okhala m'dziko lamapiri la Seiri. 10Maina a ana aamuna a Esau naŵa: Elifazi mwana wa Ada mkazi wa Esau, ndi Reuele mwana wa Basemati mkazi wa Esau. 11Ana a Elifazi ndi Temani, Omara, Zefo, Gatamu ndi Kenazi. 12(Timna anali mzikazi wa Elifazi mwana wa Esau, ndipo mwa Timnayo Elifazi adaberekamo Amaleke.) Ameneŵa ndiwo ana a Ada mkazi wa Esau. 13Ana a Reuele ndi aŵa: Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Ameneŵa ndiwo ana a Basemati mkazi wa Esau. 14Ana a Oholibama mkazi wa Esau ndi aŵa: Yeusi, Yalamu ndi Kora. Oholibamayo anali mwana wa Ana mwana wa Zibiyoni. 15Naŵa mafumu a zidzukulu za Esau. Mwa ana a Elifazi, mwana woyamba wa Esau, panali mafumu aŵa: Temani, Omara, Zefo, Kenazi, 16Gatamu ndi Amaleke. Ameneŵa ndi mafumu mwa ana a Elifazi m'dziko la Edomu. Onseŵa anali ana a Ada. 17Mwa ana a Reuele, mwana wa Esau, panali mafumu aŵa: Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Ameneŵa ndiwo mafumu mwa ana a Ruwele m'dziko la Edomu, ndiponso ndiwo ana a Basemati mkazi wa Esau. 18Mwa ana a Oholibama, mkazi wa Esau, panali mafumu aŵa: Yeusi, Yalamu ndi Kora. Ameneŵa ndiwo mafumu amene mkazi wa Esau, Oholibama mwana wa Ana, adabala. 19Ameneŵa ndi zidzukulu zake za Esau, ndiponso ndiwo mafumu ao.
Zidzukulu za Seiri
(1 Mbi. 1.38-42)
20Aŵa ndi ana aamuna a Seiri Muhori, nzika za dzikolo: Lotani, Sobali, Zibiyoni ndi Ana, 21Disoni, Ezere ndi Disani. Aŵa ndiwo mafumu a Ahori ana a Seiri m'dziko la Edomu. 22Ana a Lotani anali Hori ndi Hemani, ndipo Timna anali mlongo wa Lotani. 23Ana a Sobali ndi aŵa: Alivani, Manahati, Ebala, Sefo ndi Onamu. 24Ana a Zibiyoni ndi aŵa: Aya ndi Ana. (Ameneyu ndiye Ana amene adapeza akasupe otentha m'chipululu, pamene ankadyetsa abulu a Zibiyoni bambo wake.) 25Ana a Ana ndi aŵa: Disoni mwana wake wamwamuna, ndi Oholibama mwana wake wamkazi, 26Ana aamuna a Disoni ndi aŵa: Hemudani, Esibani, Itirani ndi Kerani. 27Ana a Ezere ndi aŵa: Bilihani, Zaavani ndi Akani. 28Ana a Disani ndi aŵa: Uzi ndi Arani. 29Mafumu a Ahori ndi aŵa: Lotani, Sobali, Zibiyoni, Ana, 30Disoni, Ezere ndi Disani. Ameneŵa ndiwo mafumu a Ahori m'dziko la Seiri malinga ndi mafuko ao.
Mafumu a ku Edomu
(1 Mbi. 1.43-54)
31Naŵa mafumu amene ankalamulira dziko la Edomu, mafumu a Aisraele asanayambe kulamulira kumeneko: 32Bela mwana wa Beori, ankalamulira dziko la Edomu, ndipo dzina la mzinda wake linali Dinihaba. 33Bela atafa, Yobabu mwana wa Zera wa ku Bozira ndiye amene adaloŵa ufumu m'malo mwake. 34Yobabu atafa, Husamu wa ku dziko la Atemani adaloŵa ufumu m'malo mwake. 35Atafa Husamu, Hadadi mwana wa Bedadi adaloŵa ufumu m'malo mwake. Iyeyu ndiye amene adagonjetsa Amidiyani m'dziko la Mowabu, ndipo dzina la mzinda wake linali Aviti. 36Atafa Hadadi, Samila wa ku Masireka ndiye adaloŵa ufumu m'malo mwake. 37Atafa Samila, Shaulo wa ku Rehoboti, mzinda wa pa mtsinje wa Yufurate, ndiye amene adaloŵa ufumu m'malo mwake. 38Atafa Shaulo, Baala-Hanani mwana wa Akibori, ndiye adaloŵa ufumu m'malo mwake. 39Baala-Hanani mwana wa Akibori atafa, Hadari ndiye adaloŵa ufumu m'malo mwake. Dzina la mzinda wake linali Pau, ndipo dzina la mkazi wake linali Mehetabele, mwana wa Matiredi mwana wa Mezahabu.
40Aŵa ndiwo mafumu a kubanja kwa Esau mwatsatanetsatane, malinga ndi mafuko ao ndi malo a fuko lililonse: Timna, Aliva, Yeteti, 41Oholibama, Ela, Pinoni, 42Kenazi, Temani Mibizara, 43Magadiele ndi Iramu. Ameneŵa ndiwo mafumu a Edomu (ndiye kuti Esau kholo la Aedomu potsatana ndi malo omwe ankakhala m'dziko laolo.)

Currently Selected:

Gen. 36: BLY-DC

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in