Gen. 29
29
Yakobe afika kwa Labani
1Tsono Yakobe adapitirira ulendo wake, kupita ku dziko la anthu akuvuma. 2Atafikako adaona chitsime ku busa, ndiponso magulu atatu a nkhosa zitagona pambali pa chitsimecho. Nkhosazo zinkamwa m'chitsime chimenechi chomwe pamwamba pake panali mwala waukulu. 3Nkhosa zonsezo zitasonkhana pamodzi kumeneko, abusa oŵeta nkhosazo ndiwo ankachotsa mwalawo pachitsimepo, kuti nkhosa zaozo zimwe. Zitatha kumwako, ankakunkhunizanso mwalawo kutseka pachitsimepo.
4Yakobe adaŵafunsa abusawo kuti, “Kodi abale anga mukuchokera kuti?” Iwowo adayankha kuti, “Tikuchokera ku Harani.” 5Yakobe adafunsanso kuti, “Kodi Labani mwana wa Nahori mumamdziŵa?” Iwowo adayankha kuti, “Ee, timamdziŵa.” 6Adaŵafunsanso kuti, “Kodi ali bwino?” Iwowo adayankha kuti, “Ee, ali bwino. Suuyu Rakele, mwana wake, akubwera ndi nkhosayu.” 7Tsono Yakobe adati, “Popeza kuti kukali masana, ndipo nthaŵi yokazilonga sinakwane, bwanji osati muzimwetse madzi, muzitengenso kukazidyetsa?” 8Iwo aja adayankha kuti, “Sitingathe kutero mpaka nkhosa zonse zitasonkhana pamodzi, ndipo mwala wa pamwamba pa chitsimewo titaukunkhuniza. Apo tingathe kuzipatsa madzi nkhosazo.”
9Yakobe akulankhulabe ndi iwowo, Rakele adafika ndi nkhosa za atate ake. Iyeyo ndiye ankaŵeta nkhosazo. 10Yakobe ataona Rakele ali ndi nkhosa za bambo wake Labani, adapita kuchitsimeko, nakunkhuniza mwalawo, nkuzimwetsa madzi nkhosa za Labanizo. 11Tsono Yakobe adamumpsompsona Rakeleyo, nalira mokweza. 12Ndipo adamuuza kuti, “Ine ndine mwana wa Rebeka, mlongo wa atate ako.” Pomwepo Rakele adathamanga kukauza atate ake.
13Labani atamva za Yakobe mwana wa mlongo wake, adathamanga kukakumana naye. Adamkumbatira, namumpsompsona, nkupita naye kunyumba. Tsono Yakobe adafotokozera Labani zonse zimene zidachitika. 14Apo Labani adamuuza kuti, “Inde, zoonadi, iwe ndiwe mbale wanga weniweni.” Yakobe adakhala kumeneko mwezi wathunthu.
Yakobe atumikira Labani kuti akwatire Rakele ndi Leya
15Tsono Labani adauza Yakobe kuti, “Suyenera kundigwirira ntchito popanda malipiro, chifukwa choti ndife abale. Undiwuze zimene ukufuna kuti ndikulipire.” 16Labani anali ndi ana aakazi aŵiri, wamkulu Leya, wamng'ono Rakele. 17Leya anali ndi maso ofooka, koma Rakele anali chiphadzuŵa. 18Yakobe ankakonda Rakele, ndipo adati, “Ndidzakugwirirani ntchito zaka zisanu ndi ziŵiri chifukwa cha mwana wanu Rakele.” 19Choncho Labani adati, “Ndi bwino kwambiri kuti Rakeleyu ndipatse iwe, osati munthu wina aliyense. Khala ndi ine.” 20Motero Yakobe adagwira ntchito zaka zisanu ndi ziŵiri kuti akwatire Rakele, ndipo nthaŵi imeneyo idangooneka kwa iye ngati masiku oŵerengeka chabe, chifukwa choti adaamkonda kwambiri mkaziyo.
21Yakobe adauza Labani kuti, “Tsopano nthaŵi yatha. Patseni mwana wanuyu kuti ndimkwatire.” 22Motero Labani adakonza phwando laukwati, naitana anthu onse akumeneko. 23Koma usiku umenewo Labani adatenga Leya m'malo mwa Rakele nampatsa Yakobe, ndipo Yakobe adaloŵana ndi Leya. 24(Nthaŵi yomweyo Labani adaperekanso mdzakazi wake Zilipa kwa Leya.) 25M'maŵa mwake kutacha, Yakobe adaona kuti mkaziyo ndi Leya. Tsono adafunsa Labani kuti, “Chifukwa chiyani mwandichita zotere? Kodi suja ndidakugwirirani ntchito kuti ndikwatire Rakele? Chifukwa chiyani tsono mwandinyenga?” 26Labani adayankha kuti, “Si mwambo wathu kuno kukwatitsa wamng'ono, mkulu wake asanakwatiwe. 27Dikira, yamba watsiriza mlungu uno wa chikondwerero chaukwati, kenaka ndidzakupatsa Rakele, komatu udzandigwiriranso ntchito zaka zina zisanu ndi ziŵiri.” 28Yakobe adavomera, ndipo mlungu wa chikondwerero chaukwati utapita, Labani adapereka Rakele kwa Yakobe kuti akhale mkazi wake. 29(Nthaŵi yomweyo Labani adaperekanso mdzakazi wake Biliha kwa Rakele.) 30Motero Yakobe adaloŵana ndi Rakele, ndipo adamkonda kupambana Leya. Tsono adamgwiriranso ntchito Labani zaka zina zisanu ndi ziŵiri.
Ana a Yakobe
31Chauta ataona kuti Yakobe sankakonda kwambiri Leya, adalola kuti Leyayo abale ana, koma Rakele ai. 32Leya adatenga pathupi, ndipo adabala mwana wamwamuna. Tsono adati, “Chauta waona zovuta zanga. Ndithu tsopano mwamuna wanga adzayamba kundikonda.” Motero mwanayo adamutcha Rubeni. 33Adatenganso pena pathupi, nabala mwana wina wamwamuna, ndipo adati, “Chauta wandipatsanso mwana wamwamunayu, chifukwa choti adamva kuti mwamuna wanga ine sandikonda.” Motero mwanayo adamutcha Simeoni. 34Adatenganso pena pathupi, nabalanso mwana wina wamwamuna, ndipo adati, “Tsopano mwamuna wanga azindikonda kwambiri, popeza kuti ndamubalira ana aamuna atatu.” Motero mwanayo adamutcha Levi. 35Adatenganso pena pathupi, nabala mwana winanso wamwamuna, ndipo adati, “Tsopano ndidzatamanda Chauta.” Motero mwanayo adamutcha Yuda. Apo adayamba walekeza kubala.
Currently Selected:
Gen. 29: BLY-DC
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi