Gen. 28
28
1Pamenepo Isaki adaitana Yakobe namdalitsa, ndipo adamlamula kuti, “Usakwatire mkazi wa kuno ku Kanani. 2Konzeka, upite ku Mesopotamiya, kwao kwa Betuele, bambo wa mai wakoyu. Kumeneko ukakwatire mmodzi mwa ana aakazi a Labani, mlongo wa mai wako. 3Mulungu Mphambe adalitse ukwati wako, ndipo akupatse ana ochuluka, kuti udzakhale gulu lalikulu la mitundu yambiri ya anthu. 4#Gen. 17.4-8Akudalitse iwe pamodzi ndi zidzukulu zako monga momwe adadalitsira Abrahamu, kuti lidzakhale lakodi dziko limene ukakhalemolo, dziko limene adapatsa Abrahamu.” 5Atatero Isaki adatumiza Yakobe ku Mesopotamiya kwa Labani, mwana wa Betuele Mwaramu. Labani anali mlongo wa Rebeka mai wa Yakobe ndi Esau.
Esau akwatiranso mkazi wina
6Esau adamva kuti Isaki wadalitsa Yakobe, ndipo kuti Yakobeyo watumizidwa ku Mesopotamiya kuti akakwatire kumeneko. Adamvanso kuti pomudalitsapo, adamlamula kuti asadzakwatire mkazi wa ku Kanani. 7Adamva kuti Yakobe wamvera bambo wake ndi mai wake, ndipo kuti wapita ku Mesopotamiya. 8Pamenepo Esau adadziŵa kuti bambo wake Isaki sankaŵakonda akazi a ku Kanani. 9Motero adapita kwa Ismaele mwana wa Abrahamu, nakwatira Maharati mwana wa Ismaele, mlongo wa Nebayoti.
Maloto a Yakobe ku Betele
10 #
Lun. 10.10
Yakobe adanyamuka ulendo kuchoka ku Beereseba, kupita ku Harani. 11Atafika pamalo pena, adaima pamenepo chifukwa dzuŵa linali litaloŵa. Adagona pompo atatsamira mwala. 12#Yoh. 1.51 Ndipo adalota akuwona makwerero ochoka pansi mpaka kukafika kumwamba. Angelo a Mulungu ankatsika ndi kumakwera pa makwererowo. 13#Gen. 13.14, 15 Chauta adaimirira pambali pake namuuza kuti, “Ine ndine Chauta, Mulungu wa Abrahamu ndi wa Isaki. Dziko ukugonapoli ndidzakupatsa iwe pamodzi ndi zidzukulu zako. 14#Gen. 12.3; 22.18 Zidzukulu zakozo zidzachuluka ngati fumbi la pa dziko lapansi. Zidzabalalikira ku mbali zonse: kuzambwe, kuvuma, kumpoto ndi kumwera. Ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadalitsidwa kudzera mwa iwe ndi zidzukulu zako. 15Ndili nawe, ndidzakutchinjiriza kulikonse kumene udzapite, ndipo ndidzakubwezanso ku dziko lino. Sindidzakusiya mpaka nditachita zonse ndakuuzazi.” 16Yakobe atadzuka adati, “Ndithudi Chauta ali pano, ndipo ine sindimadziŵa.” 17Tsono adachita mantha, nanena kuti, “Hi, malo ano ndi oopsa! Zoonadi pano mpa nyumba ya Mulungu ndiponso khomo la kumwamba.” 18Yakobeyo adadzuka m'maŵa kwambiri, natenga mwala uja adaatsamirawu, nauimiritsa kuti ukhale mwala wachikumbutso. Tsono adauthira mafuta mwalawo. 19Ndipo malowo adaŵatchula Betele. Poyamba mudziwo unkatchedwa Luzi. 20Pomwepo Yakobe adalumbira kwa Mulungu, adati, “Mukakhala nane ndi kunditchinjiriza pa ulendo wangawu, ndipo mukandipatsa chakudya ndi zovala, 21ndi kundibwezera bwino kwathu kwa atate anga, mudzakhala Mulungu wanga. 22Mwala wachikumbutso ndauimiritsawu udzakhala nyumba yanu, ndipo ine ndidzakupatsani gawo lachikhumi la zonse zimene mudzandipatse.”
Currently Selected:
Gen. 28: BLY-DC
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi