YouVersion Logo
Search Icon

Gen. 27

27
Yakobe alandira madalitso a Esau
1Isaki atakalamba, adachita khungu, mwakuti sankatha kupenya. Tsono adatumiza mau kuti Esau mwana wake wamkulu abwere. Atabwera, Isaki adamuitana kuti, “Mwana wanga!” Iye adavomera kuti, “Ŵaŵa.” 2Tsono Isakiyo adati, “Ona, ine nkukalamba kuno, ndipo sindidziŵa tsiku loti ndidzafe. 3Tenga zida zako, uta ndi mivi yomwe, upite ku thengo ukandiphere nyama. 4Undiphikire chakudya chokoma chija ndimakondachi, ubwere nacho kuno. Nditadya, ndidzakudalitsa ndisanafe.”
5Rebeka ankangomvetsera pamene Isaki ankalankhula ndi mwana wake Esau. Tsono Esauyo atapita ku thengo kukasaka nyama yoti akapatse bambo wake, 6Rebeka adauza Yakobe kuti, “Ine ndamva bambo wako akuuza Esau kuti, 7‘Ubwere ndi nyama kuno, undiphikire. Nditadya, ndidzakudalitsa pamaso pa Chauta ndisanafe.’ 8Ndiye iwe mwana wanga, undimvere ndipo uchite zonse zimene ndikuuze. 9Pita ku khola, ukanditengere timbuzi tiŵiri tonenepa bwino, kuti ndiphike, ndi kukonza chakudya chimene bambo wako amachikonda. 10Ukapereke chakudyacho kwa bambo wako kuti akadye, ndipo akudalitse asanafe.” 11Koma Yakobe adauza mai wake kuti, “Mukudziŵa kuti Esau ndi wacheya, koma ine khungu langa ndi losalala. 12Mwina mwake bambo wanga adzandikhudza, ndipo adzadziŵa kuti ndikumunyenga. Motero m'malo mondidalitsa, adzanditemberera.” 13Mai wake adayankha kuti, “Mwana wanga, temberero lakelo lidzagwere ine, osati iwe. Iweyo ungochita zimene ndakuuza, kanditengere timbuzito.” 14Choncho Yakobe adapita kukatenga timbuzito nakapatsa mai wake, ndipo Rebeka adaphika chakudya chimene bamboyo ankachikonda. 15Pambuyo pake Rebeka adatenga zovala zabwino za Esau zimene ankazisunga m'nyumba, naveka mng'ono wake Yakobe. 16Adamuvekanso zikopa za tianatambuzi pamikono pake ndiponso pakhosi pake posalala popanda cheya. 17Ndipo adatenga buledi ndi chakudya chokonza bwino chija, napatsira Yakobe.
18Yakobe adapita kwa bambo wake, namuitana kuti, “Bambo!” Isaki adafunsa kuti, “Kodi ndiwe mwana wanga uti?” 19Yakobe adayankha kuti, “Ndine Esau mwana wanu wamkulu, ndipo zija mudaandiwuzazi ndachita. Chonde dzukani, khalani tsonga, mudye nyama ndakutengeraniyi, ndipo mundidalitse.” 20Apo Isaki adafunsa kuti, “Kodi nyama imeneyi waipeza bwanji msanga chotere, mwana wanga?” Yakobe adayankha kuti, “Chauta, Mulungu wanu, adandithandiza kuti ndiipeze.” 21Isaki adauza Yakobe kuti, “Tasendera pafupi kuti ndikukhudze, kuti ndidziŵe ngati ndiwedi mwana wanga Esau, kapena ai.” 22Yakobe adasendera pafupi ndi bambo wake, ndipo bambo wakeyo adamukhudza nati, “Liwuli ndi la Yakobe, koma mikonoyi ndi ya Esau.” 23Sadamzindikire Yakobe popeza kuti mikono yake inali yacheya ngati ya Esau. Motero adayambapo kumdalitsa. 24Koma adafunsanso kuti, “Kodi ndiwedi mwana wanga Esau?” Yakobe adayankhanso kuti, “Ndine amene.” 25Apo Isaki adati, “Bwera nayo kuno nyama yako, kuti ndidye ndipo ndikudalitse.” Yakobe adabwera ndi nyamayo, Isaki nkudya. Yakobe adampatsanso vinyo woti amwe. 26Tsono bambo wakeyo adati, “Bwera pafupi, udzandimpsompsone, mwana wanga.” 27#Ahe. 11.20 Atabwera pafupi kudzampsompsona Isaki adanunkhiza zovala zimene Yakobe adaavala, ndipo pompo adamdalitsa, adati,
“Fungo lokoma la mwana wanga
lili ngati fungo la zokolola za m'munda
umene Chauta adaudalitsa.
28Mulungu akugwetsere mvula,
ndipo minda yako ikhale yobala bwino.
Akupatse zakudya ndi zakumwa zambiri.
29 # Gen. 12.3 Anthu azikutumikira,
mitundu ya anthu izikugwadira.
Ukhale wolamulira pakati pa abale ako,
zidzukulu za mai wako zizikugwadira.
Atembereredwe onse okutemberera,
ndipo adalitsidwe onse okudalitsa.”
Esau apempha Isaki kuti amdalitse
30Isaki atamaliza kudalitsako, Yakobe adachokapo. Nthaŵi yomweyo wafika Esau kuchokera kuuzimba kuja. 31Iyenso adaphika chakudya chabwino kwambiri, nakapereka kwa bambo wake. Esauyo adati, “Chonde bambo dzukani, khalani tsonga, mudye nyama imene ine mwana wanu ndakutengerani, ndipo mundidalitse.” 32Isaki adamufunsa kuti, “Kodi iwenso ndiwe yani?” Iye adayankha kuti, “Ndine mwana wanu wamkulu Esau.” 33Pompo Isaki adayamba kunjenjemera thupi lonse, nafunsa kuti, “Nanga uja adapha nyama nkubwera nayo kwa ineyu ndani? Ndadya kale imeneyo, iwe usanabwere. Ndamudalitsa kale, ndipo madalitso amenewo ndi ake mpaka muyaya.” 34Esau atamva zimenezi, adalira kwambiri ndi mtima woŵaŵa, ndipo adati, “Bambo, pepani inenso mundidalitseko.” 35Koma Isaki adayankha kuti, “Mng'ono wako anabwera, ndipo wandinyenga. Iyeyo ndiye amene watenga madalitso ako onse.” 36#Gen. 25.29-34 Pamenepo Esau adati, “Kameneka nkachiŵiri kundichenjeretsa iye uja. Nchosadodometsa kuti dzina lake ndi Yakobe. Ukulu wanga wauchisamba adandilanda, ndipo tsopano wandilandanso madalitso anga. Kodi monga madalitsowo simudandisungireko ndi pang'ono pomwe?” 37Isaki adayankha Esauyo kuti, “Ndamudalitsa kale iyeyo kuti akhale mbuyako, ndipo abale ake onse ndaŵasandutsa atumiki ake. Ndampatsa chakudya ndi chomwera chake. Nanga tsopano chatsalanso nchiyani choti ndikuchitire iwe mwana wanga?” 38#Ahe. 12.17Esau adapitirirabe kumpempha bambo wakeyo kuti, “Kodi bambo, dalitso muli nalo limodzi lokhali? Tandidalitsaniko nanenso bambo.” Ndipo atatero adayambanso kulira.
39 # Ahe. 11.20 Tsono Isaki, bambo wakeyo, adamuuza kuti,
“Pa malo ako okhalapo sipadzakhala konse chonde,
mvula siidzagwa pa minda yako.
40 # Gen. 36.8; 2Maf. 8.20 Ntchito yako idzakhala yomenya nkhondo,
ndipo udzakhala wotumikira mbale wako.
Koma ukadzatha kudzimasula,
udzachokeratu m'goli la ulamuliro wake.”
41Motero Esau adadana naye Yakobe chifukwa choti m'malo modalitsa iyeyo, bambo wake adadalitsa Yakobe. Ndipo adati, “Nthaŵi yakuti ndilire maliro a bambo wanga ili pafupi, pamenepo ndidzamupha Yakobeyu.” 42#Lun. 10.10Koma Rebeka atamva za maganizo onse a Esau, adaitana Yakobe namuuza kuti, “Taona, mbale wako Esau akuganiza zoti akuphe kuti akulipsire. 43Tsopano mwana wanga, uchite zimene ndikuuze. Konzeka, thaŵira kwa mlongo wanga Labani ku Harani. 44Bakakhala kwa iyeyo kanthaŵi ndithu, 45mpaka mtima wa mbale wako utatsika ndi kuiŵala zonse zimene wamchitazi. Pa nthaŵiyo, ine ndidzatuma munthu kudzakutenga. Nanga nditayirenji inu ana anga aŵiri pa tsiku limodzi?”
Isaki atumiza Yakobe kwa Labani
46Rebeka adauza Isaki kuti, “Akazi Achihitiŵa, ine ndatopa nawo! Yakobenso akakwatira wina mwa a Ahiti akunoŵa, ine kodi moyo wanga nkukomanso?”

Currently Selected:

Gen. 27: BLY-DC

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in