Tsono Isaki, bambo wakeyo, adamuuza kuti,
“Pa malo ako okhalapo sipadzakhala konse chonde,
mvula siidzagwa pa minda yako.
Ntchito yako idzakhala yomenya nkhondo,
ndipo udzakhala wotumikira mbale wako.
Koma ukadzatha kudzimasula,
udzachokeratu m'goli la ulamuliro wake.”