Gen. 27:28-29
Gen. 27:28-29 BLY-DC
Mulungu akugwetsere mvula, ndipo minda yako ikhale yobala bwino. Akupatse zakudya ndi zakumwa zambiri. Anthu azikutumikira, mitundu ya anthu izikugwadira. Ukhale wolamulira pakati pa abale ako, zidzukulu za mai wako zizikugwadira. Atembereredwe onse okutemberera, ndipo adalitsidwe onse okudalitsa.”