YouVersion Logo
Search Icon

NYIMBO YA SOLOMONI 5

5
1 # Mas. 36.8 Ndalowa m'munda mwanga, mlongo wanga, mkwatibwi:
Ndatchera mure wanga ndi zonunkhiritsa zanga;
ndadya uchi wanga ndi chisa chake;
ndamwa vinyo wanga ndi mkaka wanga.
Idyani, atsamwalinu,
imwani, mwetsani chikondi.
Alekana nthawi
2 # Chiv. 3.20; Yoh. 3.29 Ndinagona tulo, koma mtima wanga unali maso:
Ndi mau a bwenzi langa mnyamatayo agogoda, nati,
nditsegulire, mlongo wanga, wokondedwa wanga,
nkhunda yanga, wangwiro wanga:
Pakuti pamtu panga padzala mame,
patsitsi panga pali madontho a usiku.
3Ndinayankha kuti, Ndavula malaya anga, ndiwavalenso bwanji?
Ndasuka mapazi anga; ndiwadetserenji?
4Bwenzi langa analonga dzanja lake pazenera,
mtima wanga ndi kuguguda chifukwa cha iye.
5Ndinauka ndikatsegulire bwenzi langa;
pamanja panga panakha mure.
Ndi pa zala zanga madzi a mure,
pa zogwirira za mpikizo.
6Ndinamtsegulira bwenzi langalo;
koma ndinampeza, bwenzi langa atachoka.
Moyo wanga unalefuka polankhula iye:
Ndinamfunafuna, osampeza;
ndinamuitana, koma sanandivomere.
7Alonda akuyenda m'mudzi anandipeza,
nandikantha, nanditema;
osunga makoma nandichotsera chophimba changa.
8Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu,
mukapeza bwenzi langa, mudzamuuza chiyani?
Kuti ndadwala ndi chikondi.
9Bwenzi lako aposa abwenzi ena bwanji,
mkaziwe woposa kukongola?
Bwenzi lako aposa abwenzi ena bwanji,
kuti utilumbirira motero?
10 # Mas. 45.2; Yoh. 1.14 Wokondedwa wanga ali woyera ndi wofiira,
womveka mwa zikwi khumi.
11Mutu wake ukunga golide, woyengetsa,
tsitsi lake lopotana, ndi lakuda ngati khungubwi.
12Ana a maso ake akunga nkhunda
pambali pa mitsinje ya madzi;
otsukidwa ndi mkaka, okhala pa mitsinje yodzala.
13Masaya ake akunga chitipula chobzalamo ndiwo,
ngati mitumbira yoyangapo masamba onunkhira:
Milomo yake ikunga akakombo, pakukhapo madzi a mure.
14Manja ake akunga zing'anda zagolide
zoikamo zonyezimira zoti biriwiri.
Thupi lake likunga chopanga cha minyanga
cholemberapo masafiro.
15Miyendo yake ikunga zoimiritsa za mwala wonyezimira,
zogwirika m'kamwa mwa golide:
Maonekedwe ake akunga Lebanoni,
okometsetsa ngati mikungudza.
16M'kamwa mwake muli mokoma; inde,
ndiye wokondweretsa ndithu.
Ameneyu ndi wokondedwa wanga,
ameneyu ndi bwenzi langa,
ana akazi inu a ku Yerusalemu.

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in