YouVersion Logo
Search Icon

NYIMBO YA SOLOMONI 4

4
Mkwati alemekeza mkwatibwi
1Taona, wakongola, bwenzi langa,
namwaliwe, taona, wakongola;
maso ako akunga a nkhunda patseri pa chophimba chako.
Tsitsi lako likunga gulu la mbuzi,
zooneka pa phiri la Giliyadi.
2Mano ako akunga gulu la nkhosa zosengasenga,
zokwera kuchokera kosamba;
yonse ili ndi ana awiri,
palibe imodzi yopoloza.
3Milomo yako ikunga mbota yofiira,
m'kamwa mwako ndi kukoma:
Palitsipa pako pakunga phande la khangaza
paseli pa chophimba chako.
4 # Neh. 3.19 Khosi lako likunga nsanja ya Davide anaimangira zida,
apachikapo zikopa zikwi,
ngakhale zikopa zonse za amuna amphamvu.
5Mawere ako awiri akunga ana awiri a nswala obadwa limodzi,
akudya pakati pa akakombo.
6Mpaka dzuwa litapepa, mithunzi ndi kutanimpha,
ndikamuka kuphiri la mure,
ndi kuchitunda cha lubani.
7 # Aef. 5.27 Wakongola monsemonse, wokondedwa wanga, namwaliwe,
mulibe chilema mwa iwe.
8Idza nane kuchokera ku Lebanoni, mkwatibwi,
kuchokera nane ku Lebanoni:
Unguza pamwamba pa Amana,
pa nsonga ya Seniri ndi Heremoni,
pa ngaka za mikango,
pa mapiri a anyalugwe.
9Walanda mtima wanga, mlongo wanga, mkwatibwi;
walanda mtima wanga ndi diso lako limodzi,
ndi chinganga chimodzi cha pakhosi pako.
10Ha, chikondi chako nchokongola, mlongo wanga, mkwatibwi!
Kodi chikondi chako sichiposa vinyo?
Kununkhira kwa mphoka yako
ndi kuposa zonunkhiritsa za mitundumitundu!
11 # Hos. 14.6-7 M'milomo yako, mkwatibwi, mukukha uchi,
uchi ndi mkaka zili pansi pa lilime lako;
kununkhira kwa zovala zako
ndi kunga kununkhira kwa Lebanoni.
12Mlongo wanga, mkwatibwi ndiye munda wotsekedwa;
ngati kasupe wotsekedwa, ndi chitsime chopikiza.
13Mphukira zako ndi munda wamakangaza,
ndi zipatso zofunika, bonongwe ndi narido.
14Narido ndi chikasu,
nzimbe ndi sinamoni, ndi mitengo yonse ya lubani;
mure ndi khonje, ndi zonunkhiritsa zonse zomveka.
15 # Yes. 49.10; Yoh. 4.10 Ndiwe kasupe wa m'minda,
chitsime cha madzi amoyo,
ndi mitsinje yoyenda yochokera ku Lebanoni.
Ayankha mkwatibwi
16Galamuka, mphepo ya kumpoto iwe,
nudze, mphepo iwe ya kumwera;
nuombe pamunda panga, kuti zonunkhiritsa zake zitulukemo.
Bwenzi langa mnyamatayo, alowe m'munda mwake,
nadye zipatso zake zofunika.

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in