NYIMBO YA SOLOMONI 3
3
Mkwatibwi apeza mkwati
1 #
Yes. 26.9
Usiku pamphasa panga ndinamfunafuna amene moyo wanga umkonda:
Ndinamfunafuna, koma osampeza.
2Ndinati, Ndiuketu, ndiyendeyende m'mudzi,
m'makwalala ndi m'mabwalo ake,
ndimfunefune amene moyo wanga umkonda:
Ndimfunafuna, koma osampeza.
3Alonda akuyendayenda m'mudzi anandipeza:
Ndinati, Kodi munamuona amene moyo wanga umkonda?
4Nditawapitirira pang'ono,
ndinampeza amene moyo wanga umkonda:
Ndinamgwiriziza, osamfumbatula,
mpaka nditamlowetsa m'nyumba ya amai,
ngakhale m'chipinda cha wondibala.
5Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu,
pali mphoyo, ndi mbawala ya kuthengo,
kuti musautse, ngakhale kugalamutsa chikondi,
mpaka chikafuna mwini.
Ulendo wa ukwati
6 #
Yes. 60.8
Ndaniyu akwera kutuluka m'chipululu ngati utsi wa tolo,
wonunkhira ndi mure ndi lubani,
ndi zonunkhiritsa zonse za wogulitsa?
7Taonani, ndi machila a Solomoni;
pazingapo amuna amphamvu makumi asanu ndi limodzi,
a mwa ngwazi za Israele.
8Onsewo agwira lupanga, nazolowera nkhondo:
Yense ali ndi lupanga lake pantchafu pake,
chifukwa cha upandu wa usiku.
9Solomoni mfumu anadzipangira machila okhalamo tsonga
ndi matabwa a ku Lebanoni.
10Anapanga timilongoti take ndi siliva,
cha pansi pake ndi golide, mpando wake ndi nsalu yofiirira,
pakati pake panayalidwa za chikondi
cha ana akazi a ku Yerusalemu.
11Tulukani, ana akazi inu a Ziyoni,
mupenye Solomoni mfumu,
ndi korona amake amamveka naye tsiku la ukwati wake,
ngakhale tsiku lakukondwera mtima wake.
Currently Selected:
NYIMBO YA SOLOMONI 3: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi