NYIMBO YA SOLOMONI 2
2
1Ndine duwa lofiira la ku Saroni,
ngakhale kakombo wa kuzigwa.
2Ngati kakombo pakati pa minga
momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana akazi.
3Ngati maula pakati pa mitengo ya m'nkhalango,
momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana amuna.
Ndinakondwa pakukhala pa mthunzi wake,
zipatso zake zinatsekemera m'kamwa mwanga.
4 #
Yes. 25
Anandifikitsa kunyumba ya vinyo,
mbendera yake yondizolimira inali chikondi.
5Mundilimbikitse ndi mphesa zouma,
munditonthoze mtima ndi maula,
pakuti ndadwala ndi chikondi.
6Dzanja lake lamanzere anditsamiritse kumutu,
dzanja lake lamanja ndi kundifungatira.
7Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu,
pali mphoyo, ndi mbawala za kuthengo,
kuti musautse, ngakhale kugalamutsa chikondi,
mpaka chikafuna mwini.
8Mau a wokondedwa wanga mnyamatayo! Taona, adza,
alikulumpha pamapiri, alikujidimuka pazitunda.
9Wokondedwa wanga akunga mphoyo,
pena mwana wa mbawala:
Taona, aima patseri pakhoma lathu.
Apenyera pazenera,
nasuzumira pamade.
10Wokondedwa wanga analankhula, nati kwa ine,
tauka, bwenzi langa, wokongola wanga, tiye.
11Pakuti, taona, chisanu chatha,
mvula yapita yaleka;
12maluwa aoneka pansi;
nthawi yoimba mbalame yafika,
mau a njiwa namveka m'dziko lathu.
13Mkuyu utchetsa nkhuyu zake zosakhwima,
mipesa niphuka,
inunkhira bwino.
Tauka, bwenzi langa, wokongola wangawe, tiyetu.
14Nkhunda yangawe, yokhala m'ming'alu ya thanthwe,
mobisika motsetsereka,
ndipenye nkhope yako, ndimve mau ako;
pakuti mau ako ngokoma, nkhope yako ndi kukongola.
15 #
1Ako. 5.6
Mutigwirire ankhandwe, ngakhale ang'ono,
amene akuononga minda yamipesa;
pakuti m'minda yathu yamipesa muphuka biriwiri.
16 #
Nyi. 6.3
Wokondedwa wanga ndi wa ine, ine ndine wake:
aweta zake pakati akakombo.
17Mpaka dzuwa litapepa, mithunzi ndi kutanimpha,
bwera, bwenzi langawe, nukhale ngati mphoyo
pena mwana wa mbawala
pa mapiri a mipata.
Currently Selected:
NYIMBO YA SOLOMONI 2: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi