YouVersion Logo
Search Icon

NYIMBO YA SOLOMONI 6

6
1Bwenzi lako wapita kuti,
mkaziwe woposa kukongola?
Bwenzi lako wapatukira kuti,
tikamfunefune pamodzi nawe?
2Bwenzi langa watsikira kumunda kwake,
kuzitipula za mphoka,
kukadya kumunda kwake, ndi kutchera akakombo.
3 # Nyi. 2.16; Yes. 62.5; Mat. 9.15 Ndine wake wa wokondedwa wanga,
wokondedwa wanganso ndiye wa ine;
aweta zake pakati pa akakombo.
Mkwati ndi mkwatibwi alemekezana
4Wakongola, bwenzi langa, namwaliwe ngati Tiriza,
wokoma ngati Yerusalemu,
woopsa ngati nkhondo ndi mbendera.
5Undipambutsire maso ako,
pakuti andiopetsa.
Tsitsi lako likunga gulu la mbuzi,
zigona pambali pa Giliyadi.
6Mano ako akunga gulu la nkhosa zazikazi,
zikwera kuchokera kosamba;
yonse ili ndi ana awiri,
palibe imodzi yopoloza.
7Palitsipa pako pakunga phande la khangaza
paseli pa chophimba chako.
8Alipo akazi akulu a mfumu makumi asanu ndi limodzi,
kudza akazi aang'ono makumi asanu ndi atatu,
ndi anamwali osawerengeka.
9Nkhunda yanga, wangwiro wangayu, ndiye mmodzi;
ndiye wobadwa yekha wa amake;
ndiye wosankhika wa wombala.
Ana akazi anamuona, namutcha wodala;
ngakhale akazi akulu a mfumu,
ndi akazi aang'ono namtamanda.
10Nati, Ndaniyo atuluka ngati mbandakucha,
wokongola ngati mwezi,
woyera ngati dzuwa,
woopsa ngati nkhondo ndi mbendera?
11Ndinatsikira kumunda wa mtedza,
kukapenya msipu wa m'chigwa,
kukapenya ngati pamipesa paphuka,
ngati pamakangaza patuwa maluwa.
12Ndisanazindikire, moyo wanga unandiimika
pakati pa magaleta a anthu anga aufulu.
13Anati, Bwera, bwera, Msulamiwe;
bwera, bwera, tiyang'ane pa iwe.
Muyang'aniranji pa Msulami,
ngati pa masewero akuguba?

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in