MASALIMO 95
95
Adandaulira anthu alemekeze namvere Mulungu wao wamkulu
1 #
Mas. 100.1
Tiyeni tiimbire Yehova mokondwera;
tifuule kwa thanthwe la chipulumutso chathu.
2Tidze nacho chiyamiko pamaso pake,
timfuulire Iye mokondwera ndi nyimbo.
3 #
2Mbi. 2.5; Mas. 96.4 Pakuti Yehova ndiye Mulungu wamkulu;
ndi mfumu yaikulu yoposa milungu yonse.
4Malo ozama a dziko lapansi ali m'dzanja lake;
chuma cha m'mapiri chomwe ndi chake.
5 #
Gen. 1.9-10; Yon. 1.9 Nyanja ndi yake, anailenga;
ndipo manja ake anaumba dziko louma.
6Tiyeni, tipembedze tiwerame;
tigwade pamaso pa Yehova, amene anatilenga.
7 #
Mas. 80.1; 100.3; Aheb. 3.7-11 Pakuti Iye ndiye Mulungu wathu,
ndipo ife ndife anthu a pabusa pake,
ndi nkhosa za m'dzanja mwake.
Lero, mukamva mau ake!
8 #
Eks. 17.2, 7 Musaumitse mitima yanu, ngati ku Meriba,
ngati tsiku la ku Masa m'chipululu.
9 #
1Ako. 10.9
Pamene makolo anu anandisuntha,
anandiyesa, anapenyanso chochita Ine.
10Zaka makumi anai mbadwo uwu unandimvetsa chisoni,
ndipo ndinati, Iwo ndiwo anthu osokerera mtima,
ndipo sadziwa njira zanga.
11 #
Num. 14.23, 28, 30 Chifukwa chake ndinalumbira mu mkwiyo wanga,
ngati adzalowa mpumulo wanga.
Currently Selected:
MASALIMO 95: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi