YouVersion Logo
Search Icon

MASALIMO 96

96
Onse a pansi pano ndi am'mwamba omwe alemekeze Mulungu
1 # Mas. 33.3 Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano;
muimbireni Yehova, inu, dziko lonse lapansi.
2Muimbireni Yehova, lemekezani dzina lake;
lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.
3Fotokozerani ulemerero wake mwa amitundu;
zodabwitsa zake mwa mitundu yonse ya anthu.
4 # Mas. 95.3 Pakuti Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu;
ayenera amuope koposa milungu yonse.
5Pakuti milungu yonse ya mitundu ya anthu ndiyo mafano,
koma Yehova analenga zakumwamba.
6 # Mas. 29.1-2 Pamaso pake pali ulemu ndi ukulu.
M'malo opatulika mwake muli mphamvu ndi zochititsa kaso.
7Mpatseni Yehova, inu, mafuko a mitundu ya anthu,
mpatseni Yehova ulemerero ndi mphamvu.
8Mpatseni Yehova ulemerero wa dzina lake;
bwerani nacho chopereka, ndipo fikani kumabwalo ake.
9 # Mas. 29.1-2 Gwadirani Yehova moyera ndi mokometsetsa,
njenjemerani pamaso pake, inu dziko lonse lapansi.
10 # Mas. 93.1 Nenani mwa amitundu, Yehova achita ufumu;
dziko lokhalamo anthu lomwe likhazikika kuti silingagwedezeke;
adzaweruza mitundu ya anthu molunjika.
11 # Mas. 69.34 Kumwamba kukondwere nilisekerere dziko lapansi;
nyanja ibume mwa kudzala kwake.
12Munda ukondwerere ndi zonse zili m'mwemo;
pamenepo mitengo yonse ya kunkhalango idzafuula mokondwera.
13 # Mas. 67.4 Pamaso pa Yehova, pakuti akudza;
pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi
Adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo,
ndi mitundu ya anthu ndi choonadi.

Currently Selected:

MASALIMO 96: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for MASALIMO 96