NEHEMIYA 5
5
Nehemiya atchinjiriza aumphawi opsinjika
1 #
Lev. 25.35-37; Yes. 5.7 Pamenepo panamveka kulira kwakukulu kwa anthu ndi akazi ao kudandaula pa abale ao Ayuda. 2Popeza panali ena akuti, Ife, ana athu aamuna ndi aakazi, ndife ambiri; talandira tirigu, kuti tidye tikhale ndi moyo. 3Panali enanso akuti, Tili kupereka chikole minda yathu, ndi minda yathu yampesa ndi nyumba zathu; kuti tilandire tirigu chifukwa cha njalayi. 4Panali enanso akuti, Takongola ndalama za msonkho wa mfumu; taperekapo chikole minda yathu, ndi minda yathu yampesa. 5#Eks. 21.7; Lev. 25.39; Yes. 58.7Koma tsopano thupi lathu likunga thupi la abale athu, ana athu akunga ana ao; ndipo taonani, titengetsa ana athu aamuna ndi aakazi akhale akapolo, ndi ana athu akazi ena tawatengetsa kale; ndipo tilibe ife mphamvu ya kuchitapo kanthu; ndi minda yathu, ndi minda yathu yampesa, nja ena. 6Ndipo pakumva kulira kwao, ndi mau ao, kunandiipira kwambiri. 7#Ezk. 22.12Pamenepo mtima wanga unandipangira; ndipo ndinatsutsana nao aufulu ndi olamulira, ndi kunena nao, Mukongoletsa mwa phindu yense kwa mbale wake. Ndipo ndinasonkhanitsa msonkhano waukulu wakuwatsutsa. 8#Lev. 25.48Ndipo ndinanena nao, Ife monga umo tinakhoza, tinaombola abale athu Ayuda ogulitsidwa kwa amitundu; ndipo kodi inu mukuti mugulitse abale anu, kapena tiwagule ndi ife? Pamenepo anakhala duu, nasowa ponena. 9#2Sam. 12.14; Aro. 2.24Ndinatinso, Chinthu muchitachi si chokoma ai; simuyenera kodi kuyenda m'kuopa Mulungu wathu, chifukwa cha mnyozo wa amitundu, ndiwo adani athu? 10Kodi ine, ndi abale anga, ndi anyamata anga, tiwakongoletsa ndalama ndi tirigu mwa phindu? Ndikupemphani, tileke phindu ili. 11Abwezereni lero lomwe minda yao, minda yao yampesa, minda yao ya azitona, ndi nyumba zao, ndi limodzi la magawo zana limodzi la ndalama, ndi tirigu, vinyo, ndi mafuta, limene muwalipitsa. 12#Ezr. 10.5; Yer. 34.8-9Pamenepo anati, Tidzawabwezera osawalipitsa kanthu, tidzachita monga momwe mwanena. Pamenepo ndinaitana ansembe, ndi kuwalumbiritsa, kuti adzachita monga mwa mau awa. 13#Mat. 10.14; Mac. 18.6Ndinakutumulanso malaya anga, ndi kuti, Mulungu akutumule momwemo munthu yense wosasunga mau awa, kunyumba yake, ndi kuntchito yake; inde amkutumule momwemo, namtayire zake zonse. Ndi msonkhano wonse unati, Amen, nalemekeza Yehova. Ndipo anthu anachita monga mwa mau awa. 14#Neh. 13.6; 1Ako. 9.4, 15Ndipo chiyambire tsiku lija anandiika ndikhale kazembe wao m'dziko la Yuda; kuyambira chaka cha makumi awiri kufikira chaka cha makumi atatu mphambu ziwiri cha Arita-kisereksesi mfumu, ndizo zaka khumi ndi ziwiri, ine ndi abale anga sitinadya chakudya cha kazembe. 15#Neh. 5.9; 2Ako. 11.9; 12.13Koma akazembe akale ndisanakhale ine, analemetsa anthu, nadzitengera kwa iwo mkate, ndi vinyo, pamodzi ndi siliva masekeli makumi anai; angakhale anyamata ao anachita ufumu pa anthu; koma sindinatero ine, chifukwa cha kuopa Mulungu. 16Ndiponso ndinalimbikira ntchito ya linga ili, ngakhale dziko sitinaligula, ndi anyamata anga onse anasonkhanira ntchito komweko. 17#2Sam. 9.7; 1Maf. 18.19Panalinso podyera ine Ayuda ndi olamulira amuna zana limodzi mphambu makumi asanu, pamodzi ndi iwo akutidzera kuchokera kwa amitundu otizinga. 18#1Maf. 4.22-23Zokonzekeratu tsiku limodzi tsono ndizo ng'ombe imodzi, ndi nkhosa zonenepa zisanu ndi imodzi, anandikonzeratunso nkhuku, ndi kamodzi atapita masiku khumi vinyo wambiri wa mitundumitundu; chinkana chonsechi sindinafunsira chakudya cha kazembe, popeza ukapolo unalemerera anthuwo. 19#Neh. 13.14, 22Mundikumbukire Mulungu, zindikomere zonse ndinachitira anthu awa.
Currently Selected:
NEHEMIYA 5: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi