NEHEMIYA 4
4
Adani ayesa kuwaletsa kumanga malinga
1 #
Neh. 2.10, 19 Ndipo kunali, atamva Sanibalati kuti tinalikumanga lingali, kudamuipira, nakwiya kwakukulu, naseka Ayuda pwepwete. 2Nanena iye pamaso pa abale ake ndi ankhondo a ku Samariya, nati, Alikuchitanji Ayuda ofookawa? Adzimangire linga kodi? Adzapereka nsembe kodi? Adzatsiriza tsiku limodzi kodi? Adzakometsanso miyala ya ku miunda yotenthedwa? 3Ndipo Tobiya Mwamoni anali naye, nati, Chinkana ichi achimanga, ikakwerako nkhandwe, idzagamula linga lao lamiyala. 4#Mas. 123.3-4; 79.12Imvani, Mulungu wathu, popeza tanyozeka ife; muwabwezere chitonzo chao pamtu pao, ndi kuwapereka akhale chofunkhidwa m'dziko la ndende; 5#Mas. 69.27-28ndipo musakwirira mphulupulu yao, ndi kulakwa kwao kusafafanizike pamaso panu; pakuti anautsa mkwiyo wanu pamaso pa omanga linga. 6Koma tinamanga lingali, ndi linga lonse linalumikizana kufikira pakatimpakati; popeza mitima ya anthu inalunjika kuntchito.
7 #
Neh. 4.1
Koma kunali, atamva Sanibalati, ndi Tobiya, ndi Aarabu, ndi Aamoni, ndi Aasidodi, kuti makonzedwe a malinga a Yerusalemu anakula, ndi kuti mopasuka mwake munayamba kutsekeka, chidawaipira kwambiri; 8#Mas. 83.3-5napangana chiwembu iwo onse pamodzi, kudzathira nkhondo ku Yerusalemu, ndi kuchita chisokonezo m'menemo. 9#Mas. 50.15Koma tinapemphera kwa Mulungu wathu, ndi kuwaikira olindirira usana ndi usiku, chifukwa cha iwowa. 10Ndipo Ayuda anati, Mphamvu ya osenza akatundu yatha, ndi dothi lichuluka, motero sitidzakhoza kumanga lingali. 11Nati adani athu, Sadzadziwa kapena kuona mpaka talowa pakati pao, ndi kuwapha, ndi kuleketsa ntchitoyi. 12Ndipo kunali, atafika Ayuda okhala pafupi pao ochokera pamalo ponse, anatiuza ife kakhumi, Bwererani kwa ife.
Ankhondo atchinjiriza antchito
13Chifukwa chake ndinawaika potera m'kati mwa linga, popenyeka; inde ndinaika anthu monga mwa mabanja ao, akhale nao malupanga ao, nthungo zao, ndi mauta ao. 14#Num. 14.9; 2Sam. 10.12Ndipo ndinapenya, ndinanyamuka, ndinanena kwa aufulu, ndi olamulira, ndi anthu otsala, Musamawaopa iwo; kumbukirani Yehova wamkulu ndi woopsa, ndi kuponyera nkhondo abale anu, ana anu aamuna ndi aakazi, akazi anu, ndi nyumba zanu. 15#Yob. 5.12-13Ndipo kunali, pakumva adani athu kuti chinadziwika nafe, ndi kuti Mulungu adapititsa pachabe uphungu wao, tinabwera tonse kunka kulinga, yense kuntchito yake. 16Ndipo kuyambira pamenepo gawo lina la anyamata anga anagwira ntchito, ndi gawo lina linagwira nthungo, zikopa, ndi mauta, ndi malaya achitsulo; ndi akulu anali m'mbuyo mwa nyumba yonse ya Yuda. 17Iwo omanga linga, ndi iwo osenza katundu, posenza, anachita aliyense ndi dzanja lake lina logwira ntchito, ndi lina logwira chida; 18ndi omanga linga aliyense anamangirira lupanga lake m'chuuno mwake, nagwira ntchito motero. Ndipo woomba lipenga anali ndi ine. 19Ndipo ndinati kwa aufulu, ndi olamulira, ndi anthu otsala, Ntchito ndiyo yochuluka ndi yachitando, ndi ife tili palakepalake palingapo, yense atalikizana ndi mnzake; 20#Eks. 14.14, 25paliponse mukumva mau a lipenga, musonkhanire komweko kwa ife; Mulungu wathu adzatigwirira nkhondo. 21Momwemo tinalikugwira ntchito; gawo lina la iwo linagwira nthungo kuyambira mbandakucha mpaka zatuluka nyenyezi. 22Ndinanenanso kwa anthu nthawi yomweyi, Aliyense agone m'Yerusalemu pamodzi ndi mnyamata wake, kuti atilindirire usiku, ndi kugwira ntchito usana. 23Ndipo ine, ndi abale anga, ndi anyamata anga, angakhale amuna olindirira onditsata ine, nnena mmodzi yense wa ife anavula zovala zake, yense anapita ndi chida chake kumadzi.
Currently Selected:
NEHEMIYA 4: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi