YouVersion Logo
Search Icon

NEHEMIYA 3

3
Mamangidwe a malinga ndi zipata za Yerusalemu
1 # Yoh. 5.2 Pamenepo Eliyasibu mkulu wa ansembe ananyamuka pamodzi ndi abale ake ansembe, namanga chipata chankhosa; anachipatula, naika zitseko zake, inde anachipatula mpaka Nsanja ya Zana, mpaka nsanja ya Hananele. 2Ndi pambali pake anamanga amuna a ku Yeriko. Ndi pambali pao anamanga Zakuri mwana wa Imuri. 3#Zef. 1.10Ndi chipata chansomba anachimanga ana a Hasena; anamanga mitanda yake, ndi kuika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipingiridzo yake. 4Ndi pambali pao anakonza Meremoti mwana wa Uriya, mwana wa Hakozi. Ndi pambali pao anakonza Mesulamu mwana wa Berekiya, mwana wa Mesezabele. Ndi pambali pao anakonza Zadoki mwana wa Baana. 5#Ower. 5.23Ndi pambali pao anakonza Atekowa; koma omveka ao sanapereke makosi ao kuntchito ya Mbuye wao. 6#Neh. 12.39Ndi chipata chakale anachikonza Yoyada mwana wa Paseya; ndi Mesulamu mwana wa Besodeiya anamanga mitanda yake, ndi kuika zitseko zake, ndi zokowera zake, ndi mipingiridzo yake. 7Ndi pambali pao anakonza Melatiya Mgibeoni, ndi Yadoni Mmeronoti, ndi amuna a ku Gibiyoni, ndi a ku Mizipa, wa ulamuliro wa chiwanga tsidya lino la mtsinje. 8#Neh. 12.38Pambali pake anakonza Uziyele mwana wa Haraya, wa iwo osula golide. Ndi padzanja pake anakonza Hananiya, wa iwo osanganiza zonunkhira; nalimbikitsa Yerusalemu mpaka linga lachitando. 9Ndi pambali pao anakonza Refaya mwana wa Huri, ndiye mkulu wa dera lina la dziko la Yerusalemu. 10Ndi pambali pao anakonza Yedaya mwana wa Harumafa, pandunji pa nyumba yake. Ndi pambali pake anakonza Hatusi mwana wa Hasabineya. 11Malikiya mwana wa Harimu, ndi Hasubu mwana wa Pahatimowabu, anakonza gawo lina, ndi Nsanja ya Ng'anjo. 12Ndi pambali pake anakonza Salumu mwana wa Halohesi, mkulu wa dera lina la dziko la Yerusalemu, iye ndi ana ake akazi. 13#Neh. 2.13Chipata cha ku Chigwa anachikonza Hanuni; ndi okhala m'Zanowa anachimanga, naika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipiringidzo yake; ndiponso mikono chikwi chimodzi cha lingalo mpaka ku Chipata cha Kudzala. 14Ndi Chipata cha Kudzala anachikonza Malikiya mwana wa Rekabu, mkulu wa dziko la Betehakeremu; anachimanga, naika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipiringidzo yake. 15#Neh. 2.14; Yoh. 9.7Ndi chipata cha kukasupe anachikonza Salumu mwana wa Kolihoze mkulu wa dziko la Mizipa anachimanga, nachikomaniza pamwamba pake, naika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipiringidzo yake; ndiponso linga la dziwe la Sela pa munda wa mfumu, ndi kufikira kumakwerero otsikira kumudzi wa Davide. 16#2Maf. 20.20Potsatizana naye anakonza Nehemiya mwana wa Azibuki, mkulu wa dera lake lina la dziko la Betezuri, mpaka malo a pandunji pa manda a Davide, ndi ku dziwe adalikumba, ndi kunyumba ya amphamvu aja. 17Potsatizana naye anakonza Alevi, Rehumu mwana wa Bani. Pambali pake anakonza Hasabiya mkulu wa dera lina la dziko la Keila, kukonzera dziko lake. 18Potsatizana naye anakonza abale ao, Bavai mwana wa Henadadi, mkulu wa dera lina la dziko la Keila. 19#2Mbi. 26.9Ndi pa mbali pake Ezere mwana wa Yesuwa, mkulu wa Mizipa, anakonza gawo lina, pandunji pokwerera kunyumba yosungamo zida za nkhondo, popindirira linga. 20Potsatizana naye Baruki mwana wa Zabai anafulumira kukonza gawo lina kuyambira popindirira mpaka kukhomo la nyumba ya Eliyasibu mkulu wa ansembe. 21Potsatizana naye Meremoti mwana wa Uriya mwana wa Hakozi anakonza gawo lina, kuyambira kukhomo la nyumba ya Eliyasibu kufikira malekezero ake a nyumba ya Eliyasibu. 22Ndi potsatizana naye anakonza ansembe okhala kuchidikha. 23Potsatizana nao anakonza Benjamini ndi Hasubu pandunji pa nyumba pao. Potsatizana nao anakonza Azariya mwana wa Maaseiya mwana wa Ananiya pafupi pa nyumba yake. 24Potsatizana naye Binuyi mwana wa Henadadi anakonza gawo lina, kuyambira kunyumba ya Azariya kufikira popindirira kufikira kungodya. 25#Yer. 32.2Palali mwana wa Uzai anakonza pandunji popindirira, ndi nsanja yosomphoka pa nyumba ya mfumu ya kumtunda, imene ili kubwalo la kaidi. Potsatizana naye anakonza Pedaya mwana wa Parosi. 26#Neh. 8.1, 3Koma Anetini okhala m'Ofele anakonza kufikira kumalo a pandunji pa Chipata cha Madzi kum'mawa, ndi nsanja yosomphokayo. 27Potsatizana nao Atekowa anakonza gawo lina, pandunji pa nsanja yaikulu yosomphoka ndi kulinga la Ofele. 28#2Maf. 11.16Kumtunda kwa chipata cha akavalo anakonza ansembe, yense pandunji pa nyumba yake. 29Potsatizana nao anakonza Zadoki mwana wa Imeri pandunji pa nyumba yake. Ndi potsatizana naye anakonza Semaya mwana wa Sekaniya, wosunga chipata cha kum'mawa. 30Potsatizana naye Hananiya mwana wa Selemiya, ndi Hanuni mwana wachisanu ndi chimodzi wa Zalafi, anakonza gawo lina. Potsatizana naye anakonza Mesulamu mwana wa Berekiya pandunji pa chipinda chake. 31Potsatizana naye anakonza Malikiya wina wa osula golide kufikira kunyumba ya Anetini, ndi ya ochita malonda, pandunji pa chipata cha Hamifikadi, ndi kuchipinda chosanja cha kungodya. 32Ndi pakati pa chipinda chosanja cha kungodya ndi chipata chankhosa anakonza osula golide ndi ochita malonda.

Currently Selected:

NEHEMIYA 3: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in