YouVersion Logo
Search Icon

NEHEMIYA 2

2
Arita-kisereksesi alola Nehemiya akamange linga la Yerusalemu
1 # Ezr. 7.1 Koma kunachitika mwezi wa Nisani, chaka cha makumi awiri cha Arita-kisereksesi mfumu pokhala vinyo pamaso pake, ndinatenga vinyoyo ndi kuipatsa mfumu. Koma sindidakhala wachisoni pamaso pake ndi kale lonse. 2#Miy. 15.13Ninena nane mfumu, Nkhope yako nja chisoni chifukwa ninji popeza sudwala? Ichi si chinthu china koma chisoni cha mtima. Pamenepo ndinachita mantha akulu. 3#1Maf. 1.31; Neh. 1.3Ndipo ndinati kwa mfumu, Mfumu ikhale ndi moyo kosatha; ilekerenji nkhope yanga kuchita chisoni, popeza pali bwinja kumudzi kuli manda a makolo anga, ndi zipata zake zopsereza ndi moto. 4Ndipo mfumu inati kwa ine, Ufunanji iwe? Pamenepo ndinapemphera Mulungu wa Kumwamba. 5Ndipo ndinati kwa mfumu, Chikakomera mfumu, ndi mtima wanu ukakomera kapolo wanu, munditumize ku Yuda kumudzi wa manda a makolo anga, kuti ndiumange. 6Ninena nane mfumu, ilikukhala pansi pamodzi ndi mkazi wake wamkulu, Ulendo wako ngwa nthawi yanji, udzabweranso liti? Ndipo kudakonda mfumu kunditumiza nditaitchula nthawi. 7Ndinanenanso kwa mfumu, Chikakomera mfumu, indipatse akalata kwa ziwanga za tsidya lija la mtsinje, andilole ndipitirire mpaka ndifikira ku Yuda; 8ndi kalata kwa Asafu wosunga misitu ya mfumu, kuti andipatse mitengo ya mitanda ya kuzipata za linga lili ku Kachisi, ndi ya linga la mudzi, ndi ya nyumba imene ndidzalowamo ine. Ndipo mfumu inandipatsa monga mwa dzanja lokoma la Mulungu londikhalira. 9Ndinafika tsono kwa ziwanga za tsidya lino la mtsinje, ndipo ndinawapatsa akalata a mfumu. Koma mfumu idatumiza apite nane akazembe a nkhondo, ndi apakavalo. 10Atamva Sanibalati Muhoroni, ndi Tobiya kapoloyo Mwamoni, chidawaipira kwakukulu, kuti wadza munthu kuwafunira ana a Israele chokoma. 11Motero ndinafika ku Yerusalemu, ndi kukhalako masiku atatu. 12Ndipo ndinauka usiku, ine ndi amuna owerengeka nane, osauza munthu yense ine choika Mulungu wanga m'mtima mwanga ndichitire Yerusalemu; panalibenso nyama ina nane, koma nyama imene ndinakhalapo. 13Ndipo ndinatuluka usiku pa Chipata cha ku Chigwa, kunka kuchitsime cha chinjoka, ndi ku Chipata cha Kudzala, ndi kuyang'ana malinga a Yerusalemu adapasukawo, ndi zipata zake zothedwa ndi moto. 14Ndipo ndinapitirira kunka ku Chipata cha Chitsime, ndi ku Dziwe la Mfumu; koma popita nyama ili pansi panga panaichepera. 15#2Sam. 15.23Ndipo ndinakwera usiku kumtsinje, ndi kuyang'ana lingali; ndinabwerera tsono ndi kulowa pa Chipata cha ku Chigwa, momwemo ndinabwereranso. 16Koma olamulira sanadziwe uko ndinamuka, kapena chochita ine; sindidauzenso kufikira pamenepo Ayuda, kapena ansembe, kapena aufulu, kapena olamulira, kapena otsala akuchita ntchitoyi. 17#Neh. 1.3Pamenepo ndinanena nao, Muona choipa m'mene tilimo, kuti Yerusalemu ali bwinja, ndi zipata zake zotentha ndi moto; tiyeni timange linga la Yerusalemu, tisakhalenso chotonzedwa. 18#2Sam. 2.7; Neh. 2.8Ndinawauzanso za dzanja la Mulungu wanga londikhalira mokoma, ndiponso za mau anandiuza mfumu. Nati iwo, Tinyamuke, timange. Chotero anandilimbitsira manja mokoma. 19#Ezr. 6.6; Mas. 44.13Koma Sanibalati Muhoroni, ndi Tobiya kapolo Mwamoniyo, ndi Gesemu Mwarabu, anamva natiseka pwepwete, natipeputsa, nati, Chiyani ichi muchichita? Mulikupandukira mfumu kodi? 20#Ezr. 4.3Koma ndinawabwezera mau, ndi kunena nao, Mulungu Wam'mwamba, Iye ndiye adzatilemeza; chifukwa chake ife akapolo ake tidzanyamuka ndi kumanga; koma inu mulibe gawo, kapena ulamuliro, kapena chikumbukiro, m'Yerusalemu.

Currently Selected:

NEHEMIYA 2: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in