YouVersion Logo
Search Icon

NEHEMIYA 1

1
Nehemiya apempherera ana a Israele kwa Mulungu
1 # Neh. 10.1 Mau a Nehemiya mwana wa Hakaliya. Kunali tsono mwezi wa Kisilevi, chaka cha makumi awiri, pokhala ine ku Susa kunyumba ya mfumu, 2anafika Hanani, mmodzi wa abale anga, iye ndi amuna ena a ku Yuda; ndipo ndinawafunsa za Ayuda adapulumukawo otsala andende, ndi za Yerusalemu. 3#2Maf. 25.10Nanena nane iwo, Otsalawo otsala andende uko kudzikoko akulukutika kwakukulu, nanyozedwa; ndi linga la Yerusalemu lapasuka, ndi zipata zake zatenthedwa ndi moto. 4Ndipo kunali, pakumva mau awa, ndinakhala pansi ndi kulira misozi, ndi kuchita maliro masiku ena, ndinasalanso, ndi kupemphera pamaso pa Mulungu wa Kumwamba, 5#Dan. 9.4ndi kuti, Ndikupembedzani Yehova, Mulungu wa Kumwamba, Mulungu wamkulu ndi woopsa, wakusunga pangano ndi chifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ake; 6#Dan. 9.5, 18-20mutchere khutu, ndi maso anu atseguke kumvera pemphero la kapolo wanu, ndilipempha pamaso panu tsopano apa msana ndi usiku, kupempherera ana a Israele akapolo anu, ndi kuwulula zoipa za ana a Israele zimene tachimwira nazo Inu; inde tachimwa, ine ndi nyumba ya atate wanga. 7#Deut. 28.15, 64Tachita mwamphulupulu pa Inu, osasunga malamulo, kapena malemba, kapena maweruzo, amene mudalamulira mtumiki wanu Mose. 8Mukumbukire mau mudalamulira mtumiki wanu Mose, ndi kuti, Mukalakwa, ndidzakubalalitsani mwa mitundu ya anthu; 9#Deut. 30.2-4koma mukabwerera kudza kwa Ine, ndi kusunga malamulo anga, ndi kuwachita, angakhale otayika anu anali ku malekezero a thambo, ndidzawasonkhanitsa kuchokera komweko, ndi kubwera nao kumalo ndinawasankha kukhalitsako dzina langa. 10#Deut. 9.29Ndipo awa ndi akapolo anu ndi anthu anu, amene munawaombola ndi mphamvu yanu yaikulu, ndi dzanja lanu lolimba. 11#Yes. 26.8; Aheb. 13.18Yehova, mutcherere khutu pemphero la kapolo wanu, ndi pemphero la akapolo anu okondwera nako kuopa dzina lanu; ndipo mupambanitse kapolo wanu lero lino, ndi kumuonetsera chifundo pamaso pa munthu uyu. Koma ndinali ine wothirira mfumu chakumwa chake.

Currently Selected:

NEHEMIYA 1: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in