YouVersion Logo
Search Icon

NEHEMIYA Mau Oyamba

Mau Oyamba
Buku la Nehemiya tingathe kuligawa mu magawo anai: Gawo loyamba ndi pamene Nehemiya akubwerera ku Yerusalemu, atatumizidwa ndi mfumu ya ku Persiya kuti akakhale bwanamkubwa wa dziko la Yuda. Gawo lachiwiri ndi pamene akumanganso malinga a Yerusalemu. Lachitatu ndi pamene Ezara akuwerenga Malamulo a Mulungu anthuwo nalapa machimo. Gawo lachinai ndi ntchito zina zimene Nehemiya anazichita pokhala bwanamkubwa wa ku Yuda.
Chinthu chodziwika bwino mu bukuli ndi mbiri ya moyo wa Nehemiya wodalira pa Mulungu komanso kukonda kupemphera.
Za mkatimu
Nehemiya abwerera ku Yerusalemu 1.1—2.20
Kumangidwanso kwa makoma a Yerusalemu 3.1—7.73
Lamulo liwerengedwa, ndipo anthu akonzanso mapangano ao 8.1—10.39
Ntchito zina za Nehemiya 11.1—13.31

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in