Tachita mwamphulupulu pa Inu, osasunga malamulo, kapena malemba, kapena maweruzo, amene mudalamulira mtumiki wanu Mose. Mukumbukire mau mudalamulira mtumiki wanu Mose, ndi kuti, Mukalakwa, ndidzakubalalitsani mwa mitundu ya anthu; koma mukabwerera kudza kwa Ine, ndi kusunga malamulo anga, ndi kuwachita, angakhale otayika anu anali ku malekezero a thambo, ndidzawasonkhanitsa kuchokera komweko, ndi kubwera nao kumalo ndinawasankha kukhalitsako dzina langa.