MIKA Mau Oyamba
Mau Oyamba
Mneneriyu adalalika mau ake ku Yuda panthawi ya mneneri Yesaya. Iye ankadziwiratu kuti ufumu wa Yuda nawonso udzawonongedwa. Monga muja Yehova adalangira ufumu wakumpoto chifukwa Aisraelewo ntchito zao zinali zopanda chilungamo, momwemonso adzalanga ndi Ayuda omwe chifukwa cha zochita zao zosalungama. Komabe pa mau ake Mika akuonetsa chikhulupiriro chakuti Mulungu adzakonzanso zinthu kutsogoloko kuti zidzakhale bwino.
Kutsogoloko Mulungu adzakhazikitsanso ufumu wake kudzera mwa mmodzi mwa zidzukulu za Davide, ndipo adzadzetsa mtendere ponseponse (5.2-4).
Mau ena ofunikira kwambiri amene akunena mwachidule zimene aneneri anali kulalikira ndi awa akuti, “Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.” (6.8)
Za mkatimu
Mau a Yehova otsutsa Aisraele ndi Ayuda 1.1—3.12
Mau ena a Yehova olonjeza zabwino 4.1—5.15
Mau ena a Yehova ochenjeza anthu, mau ena otsutsa chikhulupiriro 6.1—7.20
Currently Selected:
MIKA Mau Oyamba: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi