YouVersion Logo
Search Icon

MIKA 1

1
Mau akuchenjeza Israele ndi Yuda chifukwa cha machimo ao
1 # Yer. 26.18 Mau a Yehova amene anadza kwa Mika wa ku Moreseti masiku a Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda, amene adaona za Samariya ndi Yerusalemu.
2 # Mala. 3.5 Imvani, mitundu ya anthu, inu nonse; tamvera, dziko lapansi, ndi zonse zili m'mwemo; ndipo Ambuye Yehova akhale mboni yakutsutsa inu, Ambuye m'Kachisi wake wopatulika. 3Pakuti, taonani, Yehova alikutuluka m'malo mwake, nadzatsika, nadzaponda pa misanje ya dziko lapansi. 4#Mas. 97.5Ndi mapiri adzasungunuka pansi pa Iye, ndi zigwa zidzang'ambika, ngati sera pamoto, ngati madzi otsanulidwa potsetseremba. 5Chichitika ichi chonse chifukwa cha kulakwa kwa Yakobo, ndi machimo a nyumba ya Israele. Kulakwa kwa Yakobo nkotani? Si ndiko Samariya? Ndi misanje ya Yuda ndi iti? Si ndiyo Yerusalemu? 6Chifukwa chake ndidzaika Samariya ngati mulu wa miyala ya m'munda, ngati zooka m'munda wamphesa; ndipo ndidzataya miyala yake m'chigwa, ndi kufukula maziko ake. 7Ndi mafano ake osema onse adzaphwanyika, ndi mphotho zake zonse zidzatenthedwa ndi moto, ndi mafano ake onse ndidzawapasula; pakuti anazisonkhanitsa pa mphotho ya mkazi wachiwerewere, ndipo zidzabwerera kumphotho ya mkazi wachiwerewere. 8#Yes. 22.4Chifukwa cha ichi ndidzachita maliro, ndi kuchema, ndidzayenda wolandidwa ndi wamaliseche; ndidzalira ngati nkhandwe, ndi kubuma ngati nthiwatiwa. 9Pakuti mabala ake ndi osapola; pakuti afikira ku Yuda; afikira ku chipata cha anthu anga, ku Yerusalemu. 10#2Sam. 1.20Musachifotokoza m'Gati, musalira misozi konse; m'nyumba ya Afira ndinagubuduka m'fumbi. 11Pitiratu, wokhala m'Safiri iwe, wamaliseche ndi wamanyazi; wokhala m'Zanani sanatuluke; maliro a Betezele adzakulandani pokhala pake. 12#Amo. 3.6Pakuti wokhala m'Maroti alindira chokoma, popeza choipa chatsika kwa Yehova kunka kuchipata cha Yerusalemu. 13Manga galeta kukavalo waliwiro, wokhala m'Lakisi iwe, woyamba kuchimwitsa mwana wamkazi wa Ziyoni ndi iye; pakuti zolakwa za Israele zinapezedwa mwa iwe. 14Chifukwa chake pereka mphatso zolawirana kwa Moreseti-Gati; nyumba za Akizibu zidzakhala chinthu chabodza kwa mafumu a Israele. 15Ndidzakutengeranso wokhala m'Maresa iwe, iye amene adzakulandira ukhale cholowa chake; ulemerero wa Israele udzafikira ku Adulamu. 16Udziyeseze wadazi, udzimete wekha chifukwa cha ana ako okondwera nao; kuza dazi lako ngati la muimba; pakuti anakuchokera, nalowa ndende.

Currently Selected:

MIKA 1: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in