YONA 4
4
Kudandaula kwa Yona, kumdzudzula kwa Mulungu
1Koma sikudakomera Yona konse, ndipo anapsa mtima. 2#Eks. 34.6; Mas. 86.5; Yow. 2.13Ndipo anapemphera kwa Yehova, nati, Ha, Yehova! Si ndiwo mau anga ndikali m'dziko langa? Chifukwa chake ndinafulumira kuthawira ku Tarisisi, pakuti ndinadziwa kuti Inu ndinu Mulungu wachisomo ndi wodzala chifundo, wolekerera ndi wokoma mtima mochuluka, ndi woleka choipacho. 3#1Maf. 19.4Ndipo tsopano, Yehova, mundichotseretu moyo wanga, kundikomera ine kufa, osakhala ndi moyo ai. 4Ndipo Yehova anati, Uyenera kupsa mtima kodi? 5Pamenepo Yona anatuluka m'mudzi, nakhala pansi kum'mawa kwa mudzi, nadzimangira komweko thandala, nakhala pansi pake mumthunzi mpaka adzaona chochitikira mudzi. 6Ndipo Yehova Mulungu anaikiratu msatsi, naumeretsera Yona, uchite mthunzi pamutu pake, kumlanditsa m'nsautso yake. Ndipo Yona anakondwera kwambiri chifukwa cha msatsiwo. 7Koma Mulungu anauikira mphanzi pakucha m'mawa mwake, ndiyo inadya msatsi, nufota. 8Ndipo kunali, potuluka dzuwa Mulungu anaika mphepo ya kum'mawa yotentha, ndipo dzuwa linatentha mutu wake wa Yona, nalefuka iye, nadzipempherera kuti afe; nati, Kundikomera ine kufa, kukhala ndi moyo ai. 9Ndipo Mulungu anati kwa Yona, Uyenera kodi kupsa mtima chifukwa cha msatsiwo? Nati iye, Ee, kundiyenera ine kupsa mtima mpaka imfa. 10Ndipo Yehova anati, Unachitira chifundo msatsiwo umene sunagwirapo ntchito, kapena kuumeretsa, umene unamera usiku, nutha usiku; 11ndipo sindiyenera Ine kodi kuchitira chifundo Ninive mudzi waukulu uwu; m'mene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi awiri osadziwa kusiyanitsa pakati pa dzanja lao lamanja ndi lamanzere, ndi zoweta zambiri zomwe?
Currently Selected:
YONA 4: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi