MATEYU 28
28
Yesu auka kwa akufa
(Mrk. 16.1-8; Luk. 24.1-12; Yoh. 20.1-18)
1 #
Mat. 27.56
Ndipo popita tsiku la Sabata, mbandakucha, tsiku lakuyamba la sabata, anadza Maria wa Magadala, ndi Maria winayo, kudzaona manda. 2Ndipo onani, panali chivomezi chachikulu; pakuti mngelo wa Ambuye anatsika Kumwamba, nafika kukunkhuniza mwalawo, nakhala pamwamba pake. 3Kuonekera kwake kunali ngati mphezi, ndi chovala chake choyeretsa ngati matalala; 4ndipo ndi kuopsa kwake alondawo ananthunthumira, nakhala ngati anthu akufa. 5Koma mngelo anayankha, nati kwa akaziwo, Musaope inu; pakuti ndidziwa inu mulikufuna Yesu, amene anapachikidwa. 6#Mat. 12.40; 16.21Iye mulibe muno iai; pakuti anauka, monga ananena. Idzani muno mudzaone malo m'mene anagonamo Ambuye. 7#Mat. 26.32; Mrk. 16.9Ndipo pitani msanga, muuze ophunzira ake, kuti, Wauka kwa akufa; ndipo onani, akutsogolerani ku Galileya; mudzamuona Iye komweko; onani, ndakuuzani inu. 8Ndipo iwo anachoka msanga kumanda, ndi mantha ndi kukondwera kwakukulu, nathamanga kukauza ophunzira ake. 9#Mrk. 16.7Ndipo onani, Yesu anakomana nao, nanena, Tikuoneni. Ndipo iwo anadza, namgwira Iye mapazi ake, namgwadira. 10#Aheb. 2.11Pomwepo Yesu ananena kwa iwo, Musaope; pitani, kauzeni abale anga kuti amuke ku Galileya, ndipo adzandiona Ine kumeneko.
Mau omveka mwa Ayuda
11Ndipo pamene iwo analikupita, onani, ena a alonda anafika kumzinda, nauza ansembe aakulu zonse zimene zinachitidwa. 12Ndipo pamene anasonkhana pamodzi ndi akulu, anakhala upo, napatsa asilikaliwo ndalama zambiri, 13nati, Kazinenani, kuti ophunzira ake anadza usiku, namuba Uja m'mene ife tinali m'tulo. 14Ndipo ngati ichi chidzamveka kwa kazembe, ife tidzamgwetsa mtima, ndipo tidzakukhalitsani opanda nkhawa. 15Ndipo iwo analandira ndalamazo, nachita monga anawalangiza: ndipo mbiri iyo inabuka mwa Ayuda, kufikira lero lomwe.
Yesu aoneka m'Galileya
16 #
Mat. 26.32; Mat. 28.7 Koma ophunzira khumi ndi mmodziwo anamuka ku Galileya, kuphiri kumene Yesu anawapangira. 17Ndipo pamene anamuona Iye, anamlambira; koma ena anakayika.
18 #
Luk. 10.22; Yoh. 3.35; 13.3; Aro. 14.9; Aef. 1.11, 21; Aheb. 1.2 Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pa dziko lapansi. 19#Yes. 52.10; Mrk. 16.15; Luk. 24.47; Mac. 2.38, 39; Akol. 1.23Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: 20ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.
Currently Selected:
MATEYU 28: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi