YouVersion Logo
Search Icon

MATEYU 27

27
Yudasi adzipachika yekha
(Mac. 1.16-19)
1 # Mas. 2.2; Mrk. 15.1 Ndipo pakudza mamawa, ansembe aakulu ndi akulu a anthu onse anakhala upo wakumchitira Yesu, kuti amuphe; 2#Mat. 20.19; Mac. 3.13ndipo anammanga Iye, namuka naye, nampereka Iye kwa Pilato kazembeyo.
3 # Mat. 26.14-15 Pamenepo Yudasi yemwe anampereka Iye, poona kuti Iye anatsutsidwa kuti afe, analapa, nabweza ndalama zija zasiliva makumi atatu kwa ansembe aakulu ndi akulu, 4nanena, Ndinachita koipa ine, pakupereka mwazi wosalakwa. Koma iwo anati, Tili nacho chiyani ife? Udzionere wekha. 5#2Maf. 17.23; Mac. 1.18-19Ndipo iye anataya pansi ndalamazo pa Kachisi, nachokapo, nadzipachika yekha pakhosi. 6Ndipo ansembe aakulu anatenga ndalamazo, nati, Sikuloledwa kuziika m'chosonkhera ndalama za Mulungu, chifukwa ndizo mtengo wa mwazi. 7Koma anapangana, nazigula munda wa woumba mbiya, ukhale manda a alendo. 8#2Sam. 17.23; Mac. 1.18-19Chifukwa chake munda umenewu anautcha, Munda-wa-mwazi, kufikira lero lino. 9#Zek. 11.12-13Pamenepo chinakwaniridwa chonenedwa ndi Yeremiya mneneri, ndi kuti,
Ndipo iwo anatenga ndalamazo zasiliva makumi atatu,
mtengo wa uja wowerengedwa mtengo wake,
amene iwo a ana a Israele anawerenga mtengo wake;
10ndipo anazipereka kugula munda wa woumba mbiya,
monga anandilamulira ine Ambuye.
Yesu kwa Pilato
(Mrk. 15.1-20; Luk. 23.1-25; Yoh. 18.28—19.16)
11Ndipo Yesu anaimirira pamaso pa kazembe, ndipo kazembeyo anamfunsa Iye kuti, Kodi Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo Yesu anati kwa iye, Mwatero. 12#Mat. 26.63Ndipo pakumnenera Iye ansembe aakulu ndi akulu, Iye sanayankhe kanthu. 13Pomwepo Pilato ananena kwa Iye, Sukumva kodi zinthu zambiri zotere akunenera Iwe? 14#Mat. 26.63Ndipo sanayankhe Iye, ngakhale mau amodzi, kotero kuti kazembe anazizwa ndithu. 15#Mrk. 15.6Ndipo pa chikondwerero kazembe adazolowera kumasulira anthu mmodzi wandende, amene iwo anafuna. 16Ndipo pa nthawi yomweyo anali ndi wandende wodziwika, dzina lake Barabasi. 17Chifukwa chake pamene anasonkhana, Pilato ananena kwa iwo, Mufuna kuti ndikumasulireni yani? Barabasi kodi, kapena Yesu, wotchedwa Khristu? 18Pakuti anadziwa kuti anampereka Iye mwanjiru. 19Ndipo pamene Pilato analikukhala pa mpando wakuweruza, mkazi wake anatumiza mau kwa iye, kunena, Musachite kanthu ndi munthu wolungamayo; pakuti lero m'kulota ine ndasauka kwambiri chifukwa cha Iye. 20#Mrk. 15.11; Mac. 3.14Koma ansembe aakulu ndi akulu anapangira anthu kuti apemphe Barabasi, koma kuti aononge Yesu. 21Koma kazembe anati kwa iwo, Mufuna kuti ndikumasulireni uti wa awa awiri? Ndipo iwo anati, Barabasi. 22Pilato ananena kwa iwo, Nanga ndidzachita chiyani ndi Yesu, wotchedwa Khristu? Onse anati, Apachikidwe pamtanda. 23Ndipo iye anati, Chifukwa ninji? Anachita choipa chotani? Koma iwo anafuulitsa kopambana, Apachikidwe pamtanda. 24#Deut. 21.6Koma Pilato poona kuti sanafitse, koma kuti linapambana phokoso, anatenga madzi, nasamba manja pamaso pa khamulo, nati, Ine ndilibe kuchimwira mwazi wa munthu uyu wolungama, mudzionere nokha. 25#Deut. 19.10; 2Sam. 1.16; Mac. 5.28Ndipo anthu onse anavomereza, ndi kuti, Mwazi wake uli pa ife ndi pa ana athu. 26#Yes. 53.5; Mrk. 15.15Pomwepo iye anamasulira iwo Barabasi, koma anakwapula Yesu, nampereka Iye kuti akampachike pamtanda.
27 # Mrk. 15.15 Pomwepo asilikali a kazembe anamuka naye Yesu kubwalo la milandu, nasonkhanitsa kwa Iye khamu lao lonse. 28Ndipo anavula malaya ake, namveka malaya ofiira achifumu. 29Ndipo analuka korona waminga, namveka pamutu pake, namgwiritsa bango m'dzanja lamanja lake; ndipo anagwada pansi pamaso pake, namchitira chipongwe, nati, Tikuoneni, mfumu ya Ayuda! 30#Yes. 50.6Namthira malovu, natenga bango, nampanda Iye pamutu. 31Ndipo pamene anatha kumchitira Iye chipongwe, anavula malaya aja, namveka Iye malaya ake, natsogoza Iye kukampachika pamtanda.
Ampachika Yesu
(Mrk. 15.21-41; Luk. 23.26-49; Yoh. 19.17-37)
32 # Num. 15.35-36; Mrk. 15.21; Mac. 7.58; Aheb. 13.12 Ndipo pakutuluka pao anapeza munthu wa ku Kirene, dzina lake Simoni, namkakamiza iye kuti anyamule mtanda wake. 33#Mrk. 15.22Ndipo pamene anadza kumalo dzina lake Gologota, ndiko kunena kuti, Malo a Bade, 34#Mas. 69.21anamwetsa Iye vinyo wosanganiza ndi ndulu; ndipo Iye, m'mene analawa, sanafune kumwa. 35#Mas. 22.18; Mrk. 15.24Ndipo pamene anampachika Iye, anagawana zovala zake ndi kulota maere: 36#Mat. 27.54nakhala iwo pansi, namdikira kumeneko. 37#Mrk. 15.26Ndipo anaika pamwamba pamutu pake mlandu wake wolembedwa: UYU NDI YESU MFUMU YA AYUDA. 38#Yes. 53.12; Mrk. 15.27Pamenepo anapachika pamodzi ndi Iye achifwamba awiri, mmodzi kudzanja lamanja, ndi wina kulamanzere. 39#Mas. 22.7; Mrk. 15.29Ndipo anthu akupitirirapo anamchitira mwano Iye ndi kupukusa mitu yao, 40#Mat. 26.63; Yoh. 2.19nati, Nanga Iwe, wopasula Kachisi, ndi kummanganso masiku atatu, tadzipulumutsa wekha; ngati uli Mwana wa Mulungu, tatsika pamtandapo. 41Chomwechonso ansembe aakulu, pamodzi ndi alembi ndi akulu anamchitira chipongwe, nati, 42Anapulumutsa ena, sangathe kudzipulumutsa yekha. Ndiye mfumu ya Aisraele; atsike tsopano pamtandapo, ndipo tidzamkhulupirira Iye. 43#Mas. 22.8Amakhulupirira Mulungu; Iye ampulumutse tsopano, ngati amfuna; pakuti anati, Ine ndine Mwana wa Mulungu. 44#Mrk. 15.32Ndiponso achifwambawo opachikidwa pamodzi ndi Iye, anamlalatira Iye mau amodzimodzi. 45#Amo. 8.9; Mrk. 15.33Ndipo ora lachisanu ndi chimodzi panali mdima pa dziko lonse, kufikira ora lachisanu ndi chinai. 46#Mas. 22.1; Aheb. 5.7Ndipo poyandikira ora lachisanu ndi chinai, Yesu anafuula ndi mau akulu, kunena, Eli, Eli, lama sabakitani? ndiko kunena kuti, Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine? 47Ndipo ena a iwo akuimirira komweko, pamene anamva, ananena, Uyo aitana Eliya. 48#Mat. 27.34; Mrk. 15.36Ndipo pomwepa mmodzi wa iwo anathamanga, natenga chinkhupule, nachidzaza ndi vinyo wosasa, nachiika pabango, namwetsa Iye. 49Koma ena anati, Taleka, tione ngati Eliya adzafika kudzampulumutsa. 50#Mrk. 15.37Ndipo Yesu, pamene anafuula ndi mau akulu, anapereka mzimu wake. 51#Eks. 26.31; Mrk. 15.37Ndipo onani, chinsalu chotchinga cha m'Kachisi chinang'ambika pakati, kuchokera kumwamba kufikira pansi; ndipo dziko linagwedezeka, ndi miyala inang'ambika; 52ndi manda anatseguka, ndi mitembo yambiri ya anthu oyera mtima, akugona kale, inauka; 53ndipo anatuluka m'manda mwao pambuyo pa kuuka kwake, nalowa m'mzinda woyera, naonekera kwa anthu ambiri. 54#Mat. 27.36; Mrk. 15.39Ndipo anali naye akudikira Yesu, anaona chivomezi, ndi zinthu zimene zinachitidwa, anaopa kwambiri, nanena, Indedi Uyu ndiye Mwana wa Mulungu.
55 # Luk. 8.2-3 Ndipo anali pomwepo akazi ambiri, akuyang'anira patali, omwe anatsata Yesu kuchokera ku Galileya, namatumikira Iye; 56#Mrk. 15.40mwa iwo amene munali Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi wa Yosefe, ndi amake wa ana a Zebedeo.
Amuika Yesu kumanda
(Mrk. 15.42-47; Luk. 23.50-56; Yoh. 19.38-42)
57Ndipo pamene panali madzulo, anadza munthu wachuma wa ku Arimatea, dzina lake Yosefe, amene analinso wophunzira wa Yesu; 58yemweyo anapita kwa Pilato, napempha mtembo wa Yesu. Pomwepo Pilato analamula kuti uperekedwe. 59Ndipo Yosefe anatenga mtembo, naukulunga m'nsalu yabafuta yoyeretsa, 60#Yes. 53.9nauika m'manda ake atsopano, osemedwa m'mwala, nakunkhunizira mwala waukulu pakhomo pa manda, nachokapo. 61Ndipo Maria wa Magadala anali pamenepo, ndi Maria winayo, anakhala pansi popenyana ndi mandawo.
62Ndipo m'mawa mwake, ndilo dzuwa lotsatana ndi tsiku lokonzera, ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhanira kwa Pilato, 63#Mat. 16.21; Mrk. 8.31; Luk. 9.22nanena, Mfumu, takumbukira ife kuti wonyenga uja anati, pamene anali ndi moyo, Ndidzauka pofika masiku atatu. 64Chifukwa chake mulamule kuti asindikize pamandapo, kufikira tsiku lachitatulo, kuti kapena ophunzira ake angadze, nadzamuba Iye, nadzanena kwa anthu, kuti Iye anauka kwa akufa: ndipo chinyengo chomaliza chidzaposa choyambacho. 65Pilato anati kwa iwo, Tengani alonda; mukani, kasungeni monga mudziwa. 66#Dan. 6.17Ndipo iwo anamuka, nasunga manda, nasindikizapo chizindikiro pamwalapo, iwo pamodzi ndi alondawo.

Currently Selected:

MATEYU 27: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in