YouVersion Logo
Search Icon

MATEYU 16

16
Afarisi ndi Asaduki afuna chizindikiro
(Mrk. 8.11-13)
1 # Mat. 12.38-39; Mrk. 8.11 Ndipo Afarisi ndi Asaduki anadza, namuyesa, namfunsa Iye awaonetse chizindikiro cha Kumwamba. 2Koma Iye anayankha, nati kwa iwo, Madzulo munena, Kudzakhala ngwee; popeza thambo lili lacheza. 3Ndipo m'mawa, Lero nkwa mphepo: popeza thambo lili la cheza chodera. Mudziwa kuzindikira za pa nkhope ya thambo; koma zizindikiro za nyengo yino, simungathe kuzindikira. 4#Mat. 12.38-39Obadwa oipa ndi achigololo afunafuna chizindikiro; ndipo sadzalandira chizindikiro china, koma chizindikiro cha Yona. Ndipo Iye anawasiya, nachokapo.
5Ndipo ophunzira anadza kutsidya linalo, naiwala kutenga mikate. 6#Luk. 12.1Ndipo Yesu anati kwa iwo, Yang'anirani mupewe chotupitsa mkate cha Afarisi ndi Asaduki. 7Ndipo iwo anafunsana wina ndi mnzake, nati, Sitinatenga mikate. 8Koma Yesu, m'mene anadziwa, anati, Ha, inu okhulupirira pang'ono, mufunsana chifukwa ninji wina ndi mnzake, kuti simunatenga mikate? 9#Mat. 14.17Kodi chikhalire simudziwa, ndipo simukumbukira mikate isanu ija ya anthu aja zikwi zisanu, ndi madengu angati munawatola? 10#Mat. 15.34Penanso mikate isanu ndi iwiri ija ya anthu zikwi zinai, ndi madengu angati munawatola? 11Bwanji nanga simudziwa kuti sindinanena kwa inu za mikate? Koma pewani chotupitsa cha Afarisi ndi Asaduki. 12Pomwepo anadziwitsa kuti sanawauze kupeza chotupitsa cha mikate, koma chiphunzitso cha Afarisi ndi Asaduki.
Chivomerezo cha Petro
(Mrk. 8.27-33; Luk. 9.18-22; Yoh. 6.66-69)
13 # Mrk. 8.27 Ndipo Yesu, pamene anadza ku dziko la ku Kesareya-Filipi, anafunsa ophunzira ake, kuti, Anthu anena kuti Mwana wa Munthu ndiye yani? 14Ndipo iwo anati, Ena ati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndipo enanso Yeremiya, kapena mmodzi wa aneneri. 15Iye ananena kwa iwo, Koma inu mutani kuti Ine ndine yani? 16#Mat. 14.33; Mrk. 8.38; Luk. 9.20; Yoh. 6.39Ndipo Simoni Petro anayankha nati, Inu ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo. 17#1Ako. 2.10Ndipo Yesu anayankha iye, nati, Ndiwe wodala, Simoni Bara-Yona: pakuti thupi ndi mwazi sizinakuululira ichi, koma Atate wanga wa Kumwamba. 18#Yoh. 1.42; Aef. 2.20Ndiponso Ine ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe ili ndidzakhazika Mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la akufa sadzagonjetsa uwo. 19#Mat. 18.18; Yoh. 20.23Ndidzakupatsa mafungulo a Ufumu wa Kumwamba; ndipo chimene ukamanga pa dziko lapansi chidzakhala chomangidwa Kumwamba: ndipo chimene ukachimasula pa dziko lapansi, chidzakhala chomasulidwa Kumwamba. 20#Mat. 12.16; 17.9; Mrk. 8.30Pamenepo analamulira ophunzira kuti asauze munthu kuti Iye ndiye Khristu.
21 # Mat. 20.17-19; Mrk. 8.31 Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kuwalangiza ophunzira ake, kuti kuyenera Iye amuke ku Yerusalemu, kukazunzidwa zambiri ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi; ndi kukaphedwa, ndi tsiku lachitatu kuuka kwa akufa. 22Ndipo Petro anamtenga Iye, nayamba kumdzudzula, kuti, Dzichitireni chifundo, Ambuye; sichidzatero kwa Inu ai. 23#Aro. 8.5-7Koma Iye anapotoloka, nati kwa Petro, Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; ndiwe chondikhumudwitsa Ine; chifukwa sumasamalira za Mulungu, koma za anthu.
Za kusenza mtanda wake
(Mrk. 8.34; 9.1; Luk. 9.23, 27)
24 # Mat. 10.38; Mrk. 8.34; Mac. 14.22 Pomwepo Yesu anati kwa ophunzira ake, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wake, nanditsate Ine. 25#Mat. 10.39; Luk. 17.33; Yoh. 12.25Pakuti iye amene afuna kupulumutsa moyo wake adzautaya: koma iye amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine, adzaupeza. 26#Mas. 49.7-8Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake? Kapena munthu adzaperekanji chosintha ndi moyo wake?
27 # Mas. 62.12; Mat. 26.64; Mrk. 8.38; Aro. 2.6 Pakuti Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate wake, pamodzi ndi angelo ake; ndipo pomwepo Iye adzabwezera kwa anthu onse monga machitidwe ao. 28#Mrk. 9.1; Aheb. 2.9Indetu ndinena kwa inu, kuti alipo ena a iwo aima pano sadzalawa ndithu imfa, kufikira adzaona Mwana wa Munthu atadza mu ufumu wake.

Currently Selected:

MATEYU 16: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in