YouVersion Logo
Search Icon

MATEYU 15

15
Miyambo ya makolo
(Mrk. 7.1-23)
1 # Mrk. 7.1 Pomwepo anadza kwa Yesu Afarisi ndi alembi, ochokera ku Yerusalemu, nati, 2#Mrk. 7.5; Akol. 2.8Ophunzira anu alumphiranji miyambo ya makolo? Pakuti sasamba manja pakudya. 3Ndipo Iye anayankha, nati kwa iwo, Inunso mulumphiranji lamulo la Mulungu chifukwa cha miyambo yanu? 4#Eks. 20.12; 21.17; Miy. 23.22Pakuti Mulungu anati,
Lemekeza atate wako ndi amai ako; ndipo,
Wakunenera atate wake ndi amake zoipa, afe ndithu.
5 # Mrk. 7.11-12 Koma inu munena, Amene aliyense anena kwa atate wake kapena kwa amake, Icho ukanathandizidwa nacho, nchoperekedwa kwa Mulungu; 6iyeyo sadzalemekeza atate wake. Ndipo inu mupeputsa mau a Mulungu chifukwa cha miyambo yanu. 7#Mrk. 7.6Onyenga inu! Yesaya ananenera bwino za inu, ndi kuti,
8 # Yes. 29.13 Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao;
koma mtima wao uli kutali ndi Ine.
9 # Yes. 29.13 Koma andilambira Ine kwachabe,
ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.
10Ndipo Iye anaitana makamuwo nati kwa iwo, Imvani, nimudziwitse; 11#Aro. 14.14, 17, 20si chimene chilowa m'kamwa mwake chiipitsa munthu; koma chimene chituluka m'kamwa mwake, ndicho chiipitsa munthu.
12Pomwepo anadza ophunzira, nanena kwa Iye, Mudziwa kodi kuti Afarisi anakhumudwa pakumva chonenacho? 13#Yes. 60.21Koma Iye anayankha nati, Mmera wonse, umene Atate wanga wa Kumwamba sanaubzale, udzazulidwa. 14#Yes. 9.16; Luk. 6.39Kawalekeni iwo, ali atsogoleri akhungu. Ndipo ngati wakhungu amtsogolera wakhungu, onse awiri adzagwa m'mbuna. 15Ndipo Petro anayankha nati kwa Iye, Mutifotokozere ife fanizoli. 16Ndipo Iye anati, Kodi inunso mukhala chipulukirire? 17Simudziwa kodi kuti zonse zakulowa m'kamwa zipita m'mimba, ndipo zitayidwa kuthengo? 18#Yak. 3.6Koma zakutuluka m'kamwa zichokera mumtima; ndizo ziipitsa munthu. 19#Yer. 17.9; Mrk. 7.21Pakuti mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano; 20izi ndizo ziipitsa munthu, koma kudya osasamba manja sikuipitsa munthu ai.
Mkazi wa ku Kanani
(Mrk. 7.24-30)
21 # Mrk. 7.24 Ndipo Yesu anatulukapo napatukira kumbali za Tiro ndi Sidoni. 22Ndipo onani, mkazi wa ku Kanani anatuluka m'malire, nafuula, nati, Mundichitire ine chifundo Ambuye, mwana wa Davide; mwana wanga wamkazi wagwidwa koopsa ndi chiwanda. 23Koma Iye sanamyankhe mau amodzi. Ndipo ophunzira ake anadza, nampempha, nati, Mumuuze amuke; pakuti afuula pambuyo pathu. 24#Mat. 10.5-6; Aro. 15.8Ndipo Iye anayankha, nati, Sindinatumidwa kwa ena koma kwa nkhosa zotayika za banja la Israele. 25Koma iye anadza, namgwadira Iye, nanena, Ambuye, ndithangateni ine. 26#Mat. 7.6Ndipo Iye anayankha, nati, Sichabwino kutenga mkate wa ana, ndi kuuponyera tiagalu. 27Koma iye anati, Etu, Ambuye, pakutinso tiagalu timadya nyenyeswa zakugwa pagome pa ambuye ao. 28Pomwepo Yesu anayankha, nati kwa iye, Mkaziwe, chikhulupiriro chako ndi chachikulu; chikhale kwa iwe monga momwe wafunira. Ndipo mwana wake anachira nthawi yomweyo.
Yesu achulukitsa mikate pachiwiri paja
(Mrk. 8.1-10)
29Ndipo Yesu anachoka kumeneko, nadza kunyanja ya Galileya, nakwera m'phiri, nakhala pansi pamenepo. 30#Yes. 35.5-6; Luk. 7.22Ndipo makamu ambiri a anthu anadza kwa Iye, ali nao opunduka miyendo, akhungu, osalankhula, opunduka ziwalo, ndi ena ambiri, nawakhazika pansi pa mapazi ake: ndipo Iye anawachiritsa; 31kotero kuti khamulo linazizwa, pakupenya osalankhula nalankhula, opunduka ziwalo nachira, ndi opunduka miyendo nayenda, ndi akhungu napenya, ndipo iwo analemekeza Mulungu wa Israele.
32 # Mrk. 8.1 Ndipo Yesu anaitana ophunzira ake, nati, Mtima wanga uchitira chifundo khamu la anthuwa, pakuti ali chikhalire ndi Ine masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya, ndipo sindifuna kuwauza iwo amuke osadya, kuti angaziye panjira. 33#2Maf. 4.42-44Ndipo ophunzira ananena kwa Iye, Tiione kuti mikate yotere m'chipululu yakukhutitsa unyinji wotere wa anthu? 34Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Muli nayo mikate ingati? Ndipo iwo anati, Isanu ndi iwiri, ndi tinsomba pang'ono. 35Ndipo Iye analamulira anthuwo akhale pansi onse; 36#Mat. 14.19natenga mikateyo isanu ndi iwiri ndi nsombazo; nayamika Mulungu, nanyema, napatsa kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa anthu. 37Ndipo onsewa anadya, nakhuta: ndipo anatola makombo otsala madengu asanu ndi awiri odzala. 38Ndipo anadyawo anali amuna zikwi zinai kuwaleka akazi ndi ana.
39 # Mrk. 8.10 Ndipo m'mene Iye anauza makamuwo amuke, analowa m'ngalawa, nafika m'malire a Magadani.

Currently Selected:

MATEYU 15: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in