YouVersion Logo
Search Icon

MATEYU 17

17
Mawalitsidwe a Yesu paphiri
(Mrk. 9.2-13; Luk. 9.28-36)
1 # Mrk. 9.2 Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu anatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane mbale wake, napita nao pa okha pa phiri lalitali; 2ndipo Iye anasandulika pamaso pao; ndipo nkhope yake inawala monga dzuwa, ndi zovala zake zinakhala zoyera mbu monga kuwala. 3Ndipo onani, Mose ndi Eliya anaonekera kwa iwo, alinkulankhula ndi Iye. 4Ndipo Petro anayankha, nati kwa Yesu, Ambuye, kuli bwino kuti ife tikhale pano; ngati mulola ndidzamanga pano misasa itatu; umodzi wa Inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya. 5#Yes. 42.1; Mat. 3.17; Mac. 3.22-23Akali chilankhulire, onani, mtambo wowala unawaphimba iwo: ndipo onani, mau ali kunena mumtambo, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani Iye. 6Ndipo pamene ophunzira anamva, anagwa nkhope zao pansi, naopa kwakukulu. 7Ndipo Yesu anadza, nawakhudza nati, Ukani, musaopa. 8Ndipo iwo, pokweza maso ao sanaone munthu, koma Yesu yekha.
9 # Mat. 16.20; Mrk. 9.9 Ndipo pamene anali kutsika paphiri, Yesu anawalamula iwo kuti, Musakauze munthu choonekacho, kufikira Mwana wa Munthu adadzauka kwa akufa. 10Ndipo ophunzira ake anamfunsa, nanena, Ndipo bwanji alembi amanena kuti Eliya ndiye atsogole kudza? 11#Mala. 4.5-6; Luk. 1.16-17Ndipo Iye anayankha, nati, Eliya akudzatu, nadzabwezera zinthu zonse; 12#Mat. 14.3, 10; Mrk. 9.12-13koma ndinena kwa inu, kuti Eliya anadza kale, ndipo iwo sanamdziwe iye, koma anamchitira zonse zimene anazifuna iwo. Ndipo chonchonso Mwana wa Munthu adzazunzidwa ndi iwo. 13Pomwepo ophunzira anazindikira kuti analankhula nao za Yohane Mbatizi.
Yesu achiritsa wodwala khunyu
(Mrk. 9.14-32; Luk. 9.37-45)
14 # Mrk. 9.14 Ndipo pamene iwo anadza kukhamu la anthu, kunafika kwa Iye munthu, namgwadira Iye, nati, 15Ambuye, chitirani mwana wanga chifundo; chifukwa adwala nkhunyu, kuzunzika koipa: pakuti amagwa kawirikawiri pamoto, ndi kawirikawiri m'madzi. 16Ndipo ndinadza naye kwa ophunzira anu, koma iwo sanathe kumchiritsa. 17Ndipo Yesu anayankha nati, Ha, obadwa osakhulupirira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji? Ndidzalekerera inu nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine kuno. 18Ndipo Yesu anamdzudzula; ndipo chiwanda chinatuluka mwa iye; ndipo mnyamatayo anachira kuyambira nthawi yomweyo. 19Pamenepo ophunzira anadza kwa Yesu, ali pa yekha, nati, Nanga ife sitinakhoza bwanji kuchitulutsa? 20#Mat. 21.21Ndipo Iye ananena kwa iwo, Chifukwa chikhulupiriro chanu nchaching'ono: pakuti indetu ndinena kwa inu, Mukakhala nacho chikhulupiriro monga kambeu kampiru, mudzati ndi phiri ili, Senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakukanikani. #17.20 Mabuku ena akale amaonjezerapo vesi 21 Koma mzimu ngati uwu mungautulutse pokhapokha mutapemphera ndi kusala kudya.
22 # Mat. 16.21; Luk. 9.44 Ndipo m'mene anali kutsotsa m'Galileya, Yesu ananena nao, Mwana wa Munthu adzaperekedwa m'manja a anthu; 23ndipo adzamupha Iye, ndipo Iye adzauka tsiku lachitatu. Ndipo iwo anali ndi chisoni chachikulu.
Yesu apereka msonkho
24Ndipo pofika ku Kapernao amene aja akulandira ndalama za ku Kachisi anadza kwa Petro nati, Kodi Mphunzitsi wanu sapereka rupiyalo? 25Iye anavomera, Apereka. Ndipo polowa iye m'nyumba, Yesu anatsogola kunena naye, nati, Simoni, uganiza bwanji? Mafumu a dziko lapansi alandira msonkho kwa yani? Kwa ana ao kodi, kapena kwa akunja? 26Ndipo m'mene iye anati, Kwa akunja, Yesu ananena kwa iye, Chifukwa chake anawo ali aufulu. 27Koma kuti ife tisawakhumudwitse, pita iwe kunyanja, ukaponye mbedza, nuitole nsomba yoyamba kuwedza; ndipo ukaikanula pakamwa pake udzapezamo rupiya; tatenga limeneli, nuwapatse ilo pamtu pa iwe ndi Ine.

Currently Selected:

MATEYU 17: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in