MALAKI 4
4
Oipa adzalangidwa, okoma adzadalitsidwa. Asamale chilamulo; adzafika Eliya
1 #
Yow. 2.31
Pakuti taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng'anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akuchita choipa. Adzakhala ngati chiputu; ndi tsiku lilinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi. 2#Luk. 1.78; Aef. 5.14Koma inu akuopa dzina langa, dzuwa la chilungamo lidzakutulukirani, muli kuchiritsa m'mapiko mwake; ndipo mudzatuluka ndi kutumphatumpha ngati anaang'ombe onenepa otuluka m'khola. 3Ndipo mudzapondereza oipa; pakuti adzakhala ngati mapulusa kumapazi anu, tsiku ndidzaikalo, ati Yehova wa makamu.
4 #
Eks. 20.3-17; Deut. 4.10 Kumbukirani chilamulo cha Mose mtumiki wanga, ndinamlamuliracho m'Horebu chikhale cha Israele lonse, ndicho malemba ndi maweruzo. 5#Yow. 2.31; Mat. 11.13-14; 17.11Taonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova. 6#Zek. 14.12Ndipo adzabwezera mitima ya atate kwa ana, ndi mitima ya ana kwa atate ao; kuti ndisafike ndi kukantha dziko lionongeke konse.
Currently Selected:
MALAKI 4: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi