MATEYU Mau Oyamba
Mau Oyamba
Buku la Mateyu limafotokoza za uthenga wabwino wakuti Yesu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja, amene kudzera mwa iye Mulungu anakwaniritsa malonjezano ake amene adanena kwa anthu ake mu Chipangano Chakale. Uthenga Wabwinowu si wa mtundu wa Ayuda okha ai, umene Yesu anabadwira ndi kukhala pakati pao, koma ndi wa dziko lonse.
Buku la Mateyu ndi lolembedwa mwadongosolo. Likuyamba ndi kubadwa kwa Yesu, kenaka ndi kulongosola za ubatizo ndi mayesero ake, komanso ndikudzanena za utumiki wake wolalikira, kuphunzitsa ndi kuchiritsa m'dera la Galileya. Zitatha izi, Uthengawu ukunena za ulendo wa Yesu kuchoka ku Galileya kupita ku Yerusalemu ndiponso zochitika mu sabata yomaliza ya utumiki wa Yesu, ndi kudzatsendera ndi kupachikidwa kwake pamtanda komanso kuukitsidwa kwake.
Bukuli likumuonetsa Yesu ngati Mphunzitsi wamkulu, amene ali ndi mphamvu zomasulira Malamulo a Mulungu ngati mwini wake, komanso amene amaphunzitsa za Ufumu wa Mulungu. Zambiri mwa ziphunzitso zake zimagawidwa m'magulu asanu: Choyamba ndi chiphunzitso cha paphiri, chimene chikunena za khalidwe labwino, maudindo, cholowa ndi matsiriziro ake a mzika za Ufumu wa Kumwamba (mutu 5 mpaka 7); Chachiwiri ndi malangizo kwa ophunzira ake 12 pa za utumiki wao (mutu 10); Chachitatu ndi mafanizo a Ufumu wa Kumwamba (mutu 13); Chachinai ndi chiphunzitso kuti kutsata Yesu kumanthauza chiyani (mutu 18) ndipo chachisanu ndi chiphunzitso cha chimaliziro cha nthawi ino komanso kubweranso kwa Ufumu wa Kumwamba (mutu 24 mpaka 25).
Za mkatimu
Kubadwa kwa Yesu Khristu ndi mbiri ya makolo ake 1.1—2.23
Utumiki wa Yohane Mbatizi 3.1-12
Yesu abatizidwa nayesedwa 3.13—4.11
Utumiki wa Yesu ku Galileya 4.12—18.35
Kuchokera ku Galileya kupita ku Yerusalemu 19.1—20.34
Sabata yomaliza mu Yerusalemu ndi madera oyandikira 1.1—27.66
Ambuye auka kwa akufa naonekera kwa anthu 28.1-20
Currently Selected:
MATEYU Mau Oyamba: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi