YouVersion Logo
Search Icon

MALAKI 3

3
Za mthenga wokonzeratu njira ya Ambuye
1 # Yes. 63.9; Mat. 11.10 Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu. 2#Yes. 4.4; Mala. 4.1; Mat. 3.10-12Koma ndani adzapirira tsiku la kudza kwake? Ndipo adzaima ndani pooneka Iye? Pakuti adzanga moto wa woyenga, ndi sopo wa otsuka; 3#Zek. 13.9ndipo adzakhala pansi ndi kuyenga ndi kuyeretsa siliva, nadzayeretsa ana a Levi, nadzawayengetsa ngati golide ndi siliva; pamenepo iwo adzapereka kwa Yehova zopereka m'chilungamo. 4Pamenepo chopereka cha Yuda ndi Yerusalemu chidzakomera Yehova, ngati masiku a kale lija, ndi ngati zaka zoyamba zija. 5#Zek. 5.4; Yak. 5.4, 12Ndipo ndidzayandikiza kwa inu kuti ndiweruze; ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi achigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa ntchito pa kulipira kwake, akazi amasiye, ndi ana amasiye, ndi wakuipsa mlandu wa mlendo, osandiopa Ine, ati Yehova wa makamu. 6#Num. 23.19; Aro. 11.29Pakuti Ine Yehova sindisinthika, chifukwa chake inu ana a Yakobo simunathedwa.
Za kusalanda za Mulungu ndi madalitso atsatapo
7 # Zek. 1.3 Kuyambira masiku a makolo anu mwapatuka kuleka malemba anga osawasunga. Bwererani kudza kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu, ati Yehova wa makamu. Koma inu mukuti, Tibwerere motani? 8#Neh. 13.10, 12Kodi munthu adzalanda za Mulungu? Ndipo inu mundilanda Ine. Koma mukuti, Takulandani zotani? Limodzilimodzi la magawo khumi, ndi zopereka. 9Mutembereredwa ndi temberero; pakuti mundilanda Ine, ndinu mtundu uwu wonse. 10#2Mbi. 31.10; Miy. 3.9-10; 2Ako. 9.6-8Mubwere nalo limodzilimodzi lonse la khumi, kunyumba yosungiramo, kuti m'nyumba mwanga mukhale chakudya; ndipo mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira. 11#Amo. 4.9Ndipo ndidzadzudzula zolusa chifukwa cha inu, kuti zisakuonongereni zipatso za nthaka yanu; ngakhale mpesa wanu sudzayoyoka zipatso zake, zosacha m'munda, ati Yehova wa makamu. 12Ndipo amitundu onse adzatcha inu odala; pakuti mudzakhala dziko lokondweretsa, ati Yehova wa makamu.
13Mau anu andilimbira, ati Yehova. Koma inu mukuti, Tanena motsutsana nanu ndi chiyani? 14#Mas. 73.13Mwanena, Kutumikira Mulungu nkwa chabe; ndipo tapindulanji ndi kusunga udikiro wake, ndi kuyenda ovala zamaliro pamaso pa Yehova wa makamu? 15#Mas. 73.12Ndipo tsopano tiwatcha odzikuza odala, inde iwo ochita zoipa amangidwa ngati nyumba; inde, ayesa Mulungu, napulumuka. 16#Mas. 56.8; Aheb. 3.13Pamenepo iwo akuopa Yehova analankhulana wina ndi mnzake; ndipo Yehova anawatchera khutu namva, ndi buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuopa Yehova, nakumbukira dzina lake. 17#Eks. 19.5; Mas. 103.13; Tit. 2.14Ndipo adzakhala angaanga, ati Yehova wa makamu, tsiku ndidzaikalo, ndipo ndidzawaleka monga munthu aleka mwana wake womtumikira. 18#Mas. 58.11Pamenepo mudzabwera ndi kuzindikira pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosamtumikira.

Currently Selected:

MALAKI 3: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for MALAKI 3