MALIRO 5
5
Adandaulira Yehova pa tsoka la ukapolo wao
1Yehova, kumbukirani chotigwerachi,
penyani nimuone chitonzo chathu.
2Cholowa chathu chasanduka cha alendo,
ndi nyumba zathu za achilendo.
3Ndife amasiye opanda atate,
amai athu akunga akazi amasiye.
4Tinamwa madzi athu ndi ndalama,
tiona nkhuni zathu pozigula.
5 #
Deut. 28.48
Otilondola atigwira pakhosi pathu,
tatopa osaona popumira.
6Tinagwira mwendo Ejipito
ndi Asiriya kuti tikhute zakudya.
7 #
Yer. 31.29
Atate athu anachimwa, kulibe iwo;
ndipo tanyamula mphulupulu zao.
8 #
Neh. 5.15
Akapolo atilamulira;
palibe wotipulumutsa m'dzanja lao.
9Timalowa m'zoopsa potenga zakudya zathu,
chifukwa cha lupanga la m'chipululu.
10Khungu lathu lapserera ngati pamoto
chifukwa cha kuwawa kwa njala.
11 #
Zek. 14.2
Anaipitsa akazi m'Ziyoni,
ndi anamwali m'midzi ya Yuda.
12Anawapachika akalonga manja ao;
sanalemekeze nkhope za akulu.
13Anyamata ananyamula mphero,
ana nakhumudwa posenza nkhuni.
14Akulu adatha kuzipata,
anyamata naleka nyimbo zao.
15Chimwemwe cha mtima wathu chalekeka,
masewera athu asanduka maliro.
16Korona wagwa pamutu pathu;
kalanga ife! Pakuti tinachimwa.
17Chifukwa cha ichi mtima wathu ufooka,
chifukwa cha izi maso athu achita chimbuuzi;
18pa phiri la Ziyoni lopasukalo
ankhandwe ayendapo.
19 #
Mas. 9.7; 45.6; Hab. 1.12 Inu, Yehova, mukhala chikhalire,
ndi mpando wanu wachifumu ku mibadwomibadwo.
20 #
Mas. 13.1
Bwanji mutiiwala chiiwalire,
ndi kutisiya masiku ambirimbiri.
21 #
Mas. 80.3, 7, 19 Mutitembenuzire kwa Inu, Yehova,
ndipo tidzatembenuzidwadi,
mukonzenso masiku athu ngati kale lija.
22Koma mwatikaniza konse,
mwatikwiyira kopambana.
Currently Selected:
MALIRO 5: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi