EZEKIELE Mau Oyamba
Mau Oyamba
Mneneri Ezekiele anakhala ku ukapolo ku Babiloni kuyambira nthawi imene mzinda wa Yerusalemu unali usanalandidwe mpaka nthawi imene mzinda wa Yerusalemu unagwa m'manja mwa adani mu chaka cha 586 BC. Uthenga wake umapita kwa anthu amene anali ku ukapolo ku Babiloni komanso kwa anthu a mu Yerusalemu. Buku la Ezekiele lili ndi mfundo zisanu ndi imodzi zazikulu: (1) Mulungu aitana Ezekiele kuti akhale mneneri. (2) Machenjezo kwa anthu kuti Mulungu adzawaweruza komanso za kugwa ndi kupasuka kwa Yerusalemu. (3) Mauthenga ochokera kwa Yehova onena za chiweruzo chake pa maiko osiyanasiyana amene amazunza ndi kupotoza anthu ake; (4) Mau a chitonthozo kwa Israele kuti ngakhale mzinda wa Yerusalemu wapasuka, Yehova adzadalitsanso anthu ake; (5) Uneneri wolosera motsutsana ndi Gogi; (6) Kachisi wa Yehova adzamangidwanso ndi kukhala wa ulemerero kuposa kale, ndipo dziko lidzadalitsidwa.
Ezekiele anali munthu wa chikhulupiriro champhamvu komanso wa nzeru zakuthwa polongosola zimene adzaziwona m'masomphenya. Amapereka uthenga wake pogwiritsa ntchito zifanizo zochititsa chidwi ndi zachilendo. Phunziro lalikulu ndilo lakuti anthu atembenuke mtima ndi kusintha maganizo ao, popeza aliyense adzaweruzidwa chifukwa cha zolakwa zake. Choncho anthu asaleke kukhulupirira Yehova amene adzadzutsanso fuko lake la Israele. Ezekiele anali wansembe komanso mneneri, ndipo amakonda kunena za Kachisi wa Yehova ndi kufunika kwakuti anthu akhale oyera mtima pa ntchito yotumikira Mulungu.
Za mkatimu
Kuitanidwa kwa Ezekiele 1.1—3.27
Mauthenga achiweruzo onena za Yerusalemu 4.1—24.27
Chiweruzo cha Mulungu pa maiko 25.1—32.32
Lonjezo la Mulungu kwa anthu ake 33.1—37.28
Mau a Yehova otsutsa dziko la Gogi 38.1—39.29
Masomphenya a Kachisi komanso dziko lakutsogolo 40.1—48.35
Currently Selected:
EZEKIELE Mau Oyamba: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi