YouVersion Logo
Search Icon

YOSWA 24

24
Yoswa akumbutsa anthu zowachitira Mulungu
1Ndipo Yoswa anasonkhanitsa mafuko onse a Israele ku Sekemu, naitana akuluakulu a Israele ndi akulu ao, ndi oweruza ao, ndi akapitao ao; ndipo anadzilangiza pamaso pa Mulungu. 2#Gen. 11.27-32Ndipo Yoswa ananena ndi anthu onse, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Kale lija makolo anu anakhala tsidya lija la mtsinje, ndiye Tera, atate wa Abrahamu ndi atate wa Nahori; natumikira milungu ina iwowa. 3#Gen. 12.1-2, 5Ndipo ndinamtenga kholo lanu Abrahamu tsidya lija la mtsinje, ndi kumuyendetsa m'dziko lonse la Kanani ndi kuchulukitsa mbeu zake ndi kumpatsa Isaki. 4#Gen. 25.21-26; 36.8; 46.1-6Ndi kwa Isaki ndinapatsa Yakobo ndi Esau, ndipo ndinampatsa Esau phiri la Seiri likhale lakelake; koma Yakobo ndi ana ake anatsikira kunka ku Ejipito. 5#Eks. 3.10; 7.1—12.51Pamenepo ndinatuma Mose ndi Aroni, ndipo ndinasautsa Aejipito, monga ndinachita pakati pake; ndipo nditatero ndinakutulutsani. 6#Eks. 12.37, 51; 14.9Ndipo ndinatulutsa atate anu m'Ejipito; ndipo munadza kunyanja; koma Aejipito analondola atate anu ndi magaleta ndi apakavalo mpaka ku Nyanja Yofiira. 7#Eks. 14.20, 27-28Ndipo pamene anafuula kwa Yehova, anaika mdima pakati pa inu ndi Aejipito nawatengera nyanja, nawamiza; ndi maso anu anapenya chochita Ine m'Ejipito; ndipo munakhala m'chipululu masiku ambiri. 8#Num. 21.21-35Pamenepo ndinakulowetsani inu m'dziko la Aamori okhala tsidya lija la Yordani; nagwirana nanu iwowa; ndipo ndinawapereka m'dzanja lanu, nimunalandira dziko lao likhale lanulanu; ndipo ndinawaononga pamaso panu. 9#Num. 22—24Pamenepo Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu, anauka naponyana ndi Israele; natuma naitana Balamu mwana wa Beori atemberere inu; 10koma sindinafuna kumvera Balamu, potero anakudalitsani chidalitsire, ndipo ndinakulanditsani m'dzanja lake. 11#Yos. 3.14Pamenepo munaoloka Yordani, ndi kufika ku Yeriko; ndi eni ake a ku Yeriko anaponyana nanu nkhondo, Aamori, ndi Aperizi, ndi Akanani, ndi Ahiti, ndi Agirigasi, Ahivi, ndi Ayebusi; ndipo ndinawapereka m'dzanja lanu. 12Ndipo ndinatuma mavu atsogolere inu, amene anawaingitsa pamaso panu, ndiwo mafumu awiri a Aamori; osati ndi lupanga lako, kapena ndi uta wako ai. 13Ndipo ndinakupatsani dziko limene simunagwiramo ntchito, ndi midzi simunaimanga, ndipo mukhala m'mwemo; mukudya za m'minda yamphesa, ndi minda ya azitona imene simunaioka.
Yoswa abwereza kuchita pangano pakati pa Mulungu ndi anthu
14 # 1Sam. 12.24; 2Ako. 1.12 Ndipo tsopano, opani Yehova ndi kumtumikira ndi mtima wangwiro ndi woona; nimuchotse milungu imene makolo anu anaitumikira tsidya lija la mtsinje, ndi m'Ejipito; nimutumikire Yehova. 15#Gen. 18.19; 1Maf. 18.21; Yoh. 6.67Ndipo ngati kutumikira Yehova kukuipirani mudzisankhire lero amene mudzamtumikira, kapena milungu imene anaitumikira makolo anu okhala tsidya lija la mtsinje, kapena milungu ya Aamori amene mukhala m'dziko lao; koma ine, ndi a m'nyumba yanga, tidzatumikira Yehova. 16Ndipo anthu anayankha, nati, Sikungatheke kuti timsiye Yehova, ndi kutumikira milungu ina; 17pakuti Yehova Mulungu wathu ndi Iye amene anatikweza kutitulutsa m'dziko la Ejipito kunyumba ya akapolo, nachita zodabwitsa zazikuluzo pamaso pathu, natisunga m'njira monse tidayendamo, ndi pakati pa anthu onse amene tinapita pakati pao; 18ndipo Yehova anaingitsa pamaso pathu anthu awa onse, ngakhale Aamori okhala m'dzikomo; chifukwa chake ifenso tidzatumikira Yehova, pakuti ndiye Mulungu wathu. 19#1Sam. 6.20; Yes. 5.16Ndipo Yoswa anati kwa anthu, Simukhoza inu kutumikira Yehova pakuti ndiye Mulungu woyera, ndi Mulungu wansanje; sadzalekerera zolakwa zanu, kapena zochimwa zanu. 20#1Mbi. 28.9Mukasiya Yehova, ndi kutumikira milungu yachilendo, adzatembenuka ndi kukuchitirani choipa, ndi kukuthani, angakhale anakuchitirani chokoma. 21Ndipo anthu anati kwa Yoswa, Iaitu, koma tidzatumikira Yehova. 22#Yos. 24.15; Mas. 119.173Ndipo Yoswa ananena ndi anthu, Inu mwadzichitira mboni inu nokha kuti mwadzisankhira Yehova kumtumikira Iye. Ndipo anati, Ndife mboni. 23#1Sam. 7.3Ndipo tsopano, chotsani milungu yachilendo ili pakati pa inu, ndi kulozetsa mitima yanu kwa Yehova, Mulungu wa Israele. 24Ndipo anthu anati kwa Yoswa, Tidzamtumikira Yehova Mulungu wathu ndi kumvera mau ake. 25#2Maf. 11.17Motero Yoswa anachita pangano ndi anthu tsiku lija, nawaikira lemba ndi chiweruzo m'Sekemu.
26 # Deut. 31.24 Ndipo Yoswa analembera mau awa m'buku la chilamulo cha Mulungu; natenga mwala waukulu, nauimitsa apo patsinde pa thundu wokhala pa malo opatulika a Yehova. 27Ndipo Yoswa anati kwa anthu onse, Taonani, mwala uwu udzakhala mboni yotitsutsa; pakuti udamva mau onse a Yehova amene ananena kwa ife; ndipo udzakhala mboni yotsutsa inu, mungakanize Mulungu wanu. 28Pamenepo Yoswa anauza anthu amuke, yense ku cholowa chake.
Amwalira Yoswa ndi Eleazara
29Ndipo kunali, zitatha izi, Yoswa mwana wa Nuni mtumiki wa Yehova, adafa, wa zaka zana ndi khumi. 30Ndipo anamuika m'malire a cholowa chake m'Timnati-Sera, ndiwo ku mapiri a Efuremu kumpoto kwa phiri la Gaasi. 31Ndipo Israele anatumikira Yehova masiku onse a Yoswa, ndi masiku onse a akuluakulu otsala atafa Yoswa, amene anadziwa ntchito yonse ya Yehova anaichitira Israele. 32#Gen. 33.19; 50.25Ndipo mafupa a Yosefe amene ana a Israele anakwera nao kuchokera ku Ejipito anawaika ku Sekemu, pa kadziko kamene adakagula Yakobo kwa ana a Hamori atate wa Sekemu ndi kuwapatsa ndalama zana; ndipo anakhala cholowa cha ana a Yosefe. 33Eleazaranso mwana wa Aroni anafa; ndipo anamuika pa phiri la Finehasi mwana wake, limene adampatsa ku mapiri a Efuremu.

Currently Selected:

YOSWA 24: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in