YOSWA 23
23
Yoswa achenjeza anthu asunge Malamulo a Mulungu
1Ndipo atapita masiku ambiri, Yehova atapumulitsa Israele kwa adani ao onse akuwazungulira, ndipo Yoswa adakalamba nakhala wa zaka zambiri; 2#Deut. 31.28Yoswa anaitana Aisraele onse, akuluakulu ao, ndi akulu ao, ndi oweruza ao, ndi akapitao ao, nanena nao, Ndakalamba, ndine wa zaka zambiri; 3#Eks. 14.14ndipo munapenya zonse Yehova Mulungu anachitira mitundu iyi yonse ya anthu chifukwa cha inu; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye anakuthirirani nkhondo. 4Taonani, ndakugawirani mitundu ya anthu iyi yotsala ikhale cholowa cha mafuko anu, kuyambira ku Yordani, ndi mitundu yonse ya anthu ndinaipasula, mpaka ku Nyanja Yaikulu ku malowero a dzuwa. 5#Num. 33.53Ndipo Yehova Mulungu wanu Iyeyu adzawapirikitsa pamaso panu, ndi kulanda dziko lao kuwachotsa pamaso panu, ndipo mudzalandira dziko lao likhale cholowa chanu; monga Yehova Mulungu wanu ananena ndi inu. 6#Num. 31.27Koma mulimbike mtima kwambiri kusunga ndi kuchita zonse zolembedwa m'buku la chilamulo cha Mose, osachipatukira kulamanja kapena kulamanzere; 7osalowa pakati pa amitundu awa otsala mwa inu; kapena kutchula dzina la milungu yao; osalumbiritsa nalo, kapena kuitumikira, kapena kuigwadira; 8#Deut. 10.20koma muumirire Yehova Mulungu wanu, monga munachita mpaka lero lino. 9#Yos. 1.5Pakuti Yehova anaingitsa pamaso panu mitundu yaikulu ndi yamphamvu; koma inu, palibe munthu anaima pamaso panu mpaka lero lino. 10#Deut. 32.30Munthu mmodzi wa inu adzapirikitsa anthu chikwi chimodzi; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye amathirira inu nkhondo monga ananena ndi inu. 11Potero mudzisamalire ndithu kuti mukonde Yehova Mulungu wanu. 12Koma, mukadzabwerera m'mbuyo pang'ono pokha ndi kuumirira otsala a mitundu awa, ndiwo akutsala pakati pa inu, ndi kukwatitsana nao, ndi kulowana nao, naonso kulowana nanu; 13#Ower. 2.3dziwani ndithu kuti Yehova Mulungu wanu sadzalandanso dziko la amitundu awa kuwachotsa pamaso panu; koma adzakhala kwa inu deka ndi msampha ndi mkwapulo m'nthiti mwanu, ndi minga m'maso mwanu, mpaka mudzatayika m'dziko lokoma ili anakupatsani Yehova Mulungu wanu. 14#Yos. 21.45; 1Maf. 2.2; Luk. 21.33Ndipo taonani, lero lino ndilikumuka njira ya dziko lonse lapansi; ndipo mudziwa m'mitima yanu yonse, ndi m'moyo mwa inu nonse, kuti pa mau okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwe padera mau amodzi; onse anachitikira inu, sanasowepo mau amodzi. 15#Lev. 26.16Ndipo kudzakhala kuti monga zakugwerani zokoma zonse anakunenerani Yehova Mulungu wanu, momwemo Yehova adzakutengerani zoipa zonse mpaka atakuonongani kukuchotsani m'dziko lokoma ili anakupatsani Yehova Mulungu wanu. 16Mukalakwira chipangano cha Yehova Mulungu wanu chimene analamulira inu ndi kumuka ndi kutumikira milungu ina ndi kuigwadira, mkwiyo wa Mulungu udzayakira inu, nimudzatayika msanga m'dziko lokomali anakupatsani.
Currently Selected:
YOSWA 23: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi