OWERUZA Mau Oyamba
Mau Oyamba
Bukuli likukamba zochitika zina ndi zina kuyambira nthawi imene Aisraele analowa m'dziko la Kanani kufikira nthawi yokhazikitsa ufumu. Pa nthawi yonseyo Aisraele anakhala akuzunzika kwambiri chifukwa chokhala pakati pa anthu a mitundu ina, anthu ofunkha ndi ankhanza, kotero kuti panali chisokonezo. Bukuli litchedwa Oweruza, kunena anthu angapo amene Yehova awaitana kuti azitsogolera Aisraele anzao pa nkhondo yomenyana ndi adani. Woweruza wina wodziwika kwambiri ndi Samisoni amene zochita zake zikukambidwa pa mutu 13 mpaka 16.
Phunziro lopezeka m'bukuli ndilo lakuti, Israele akakhala okhulupirika kwa Yehova, amakhala pa mtendere. Koma akafulatira Mulungu ndi kumamchimwira, amagwa m'mavuto aakulu. Komabe ngakhale iwo apandukira Yehova ndi kugwa m'mavuto, Mulungu ali wokonzeka kuwapulumutsa anthu akewo, ataona kuti atembenuka ndi kubwerera kwa Iyeyo.
Za mkatimu
Zochitika zina kufikira nthawi ya imfa ya Yoswa 1.1—2.10
Za oweruza ena ndi ena 2.11—16.31
Zochitika zinanso 17.1—21.25
Currently Selected:
OWERUZA Mau Oyamba: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi