OWERUZA 1
1
Aisraele aonjeza kugonjetsa Akanani
1Ndipo atafa Yoswa, ana a Israele anafunsira kwa Yehova ndi kuti, Adzayamba ndani kutikwerera pa Akanani kuwathira nkhondo? 2#Gen. 49.8Ndipo Yehova anati, Akwere Yuda; taonani, ndapereka dzikoli m'dzanja lake. 3Ndipo Yuda ananena ndi Simeoni mkulu wake, Kwera nane ku gawo langa kuti tiwathire nkhondo Akanani; ndipo inenso ndidzamuka nawe ku gawo lako. Namuka naye Simeoni. 4Ndipo Yuda atakwera, Yehova anapereka Akanani ndi Aperizi m'dzanja lao, ndipo anakantha a iwowa anthu zikwi khumi ku Bezeki. 5Ndipo anapeza Adoni-Bezeki m'Bezeki, namthira nkhondo nakantha Akanani ndi Aperizi. 6Koma Adoni-Bezeki anathawa; ndipo anampirikitsa, namgwira, namdula zala zazikulu za m'manja ndi za m'mapazi. 7#1Sam. 15.33Pamenepo anati Adoni-Bezeki, Mafumu makumi asanu ndi awiri odulidwa zala zazikulu za m'manja ndi m'mapazi anaola kakudya kao pansi pa gome panga; monga ndinachita ine, momwemo Mulungu wandibwezera. Ndipo anadza naye ku Yerusalemu, nafa iye komweko.
8 #
Yos. 15.63
Ndipo ana a Yuda anachita nkhondo pa Yerusalemu, naulanda, naukantha ndi lupanga lakuthwa, natentha mudzi ndi moto. 9Ndipo atatero ana a Yuda anatsika kuthirana nao nkhondo Akanani akukhala kumapiri, ndi kumwera ndi kuchidikha. 10Ndipo Yuda anamuka kwa Akanani akukhala m'Hebroni; koma kale dzina la Hebroni ndilo mudzi wa Ariba; ndipo anakantha Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai. 11Pochoka pamenepo anamuka kwa nzika za ku Debiri, koma kale dzina la Debiri ndilo mudzi wa Kiriyati-Sefere. 12Ndipo Kalebe anati, Iye amene akantha mudzi wa Kiriyati-Sefere, naulanda, yemweyo ndidzampatsa Akisa mwana wanga wamkazi akhale mkazi wake. 13#Ower. 3.9Ndipo Otiniyele, mwana wa Kenazi mng'ono wa Kalebe anaulanda, ndipo anampatsa Akisa mwana wake wamkazi akhale mkazi wake. 14Ndipo kunali, m'mene anamdzera, anamkakamiza mwamuna wake kuti apemphe atate wake ampatse munda; natsika pa bulu wake; ndipo Kalebe ananena naye, Ufunanji? 15Ndipo anati kwa iye, Mundipatse dalitso; popeza mwandipatsa dziko la kumwera, ndipatsenso zitsime za madzi. Pamenepo Kalebe anampatsa zitsime za kumtunda ndi zitsime za kunsi.
16 #
Deut. 34.3; 1Sam. 15.6; 1Mbi. 2.55; Yer. 35.2 Ndipo ana a Mkeni mlamu wake wa Mose, anakwera kutuluka m'mudzi wa m'migwalangwa pamodzi ndi ana a Yuda, nalowa m'chipululu cha Yuda chokhala kumwera kwa Aradi; namuka iwo nakhala ndi anthuwo. 17Ndipo Yuda anamuka ndi Simeoni mkulu wake, nakantha Akanani akukhala m'Zefati, nauononga konse. Koma dzina la mudziwo analitcha Horoma. 18Yuda analandanso Gaza ndi malire ake, ndi Asikeloni ndi malire ake ndi Ekeroni ndi malire ake. 19#2Maf. 18.7Ndipo Yehova anali ndi Yuda, iye nawaingitsa a kumapiri, osaingitsa nzika za kuchigwa, popeza zinali nao magaleta achitsulo. 20#Yos. 14.13Ndipo anapatsa Kalebe Hebroni monga Mose adanena; iye nawaingitsa komweko ana amuna atatu a Anaki. 21#Yos. 15.63Koma ana a Benjamini sanaingitse Ayebusi okhala m'Yerusalemu; koma Ayebusi anakhala m'Yerusalemu pamodzi ndi ana a Benjamini, mpaka lero lino.
22 #
Yak. 2.13; Ower. 1.19 Ndipo anakwera iwo a m'nyumba ya Yosefe, naonso kunka ku Betele; ndipo Yehova anakhala nao. 23#Gen. 28.19Ndipo iwo a m'nyumba ya Yosefe anatumiza ozonda ku Betele. Koma kale dzina la mudziwo ndilo Luzi. 24#Yos. 2.12, 14Ndipo alonda anaona munthu alikutuluka m'mudzi, nanena naye, Utionetsetu polowera m'mudzi, ndipo tidzakuchitira chifundo. 25Nawaonetsa polowera m'mudzi iye, naukantha mudzi iwowa ndi lupanga lakuthwa; koma analola munthuyo ndi banja lake lonse amuke. 26Ndipo munthuyo anamuka ku dziko la Ahiti, namanga mudzi, nautcha dzina lake Luzi; ndilo dzina lake mpaka lero lino.
Aisraele aleka kugonjetsa Akanani ena
27Koma Manase sanaingitse a ku Beteseani ndi midzi yake kapena a Taanaki ndi midzi yake, kapena nzika za ku Dori ndi midzi yake, kapena nzika za ku Ibleamu ndi midzi yake, kapena nzika za ku Megido ndi midzi yake; koma Akanani anakhumba kukhala m'dziko muja. 28Ndipo kunali, atakula mphamvu Israele, anasonkhetsa Akanani, osawaingitsa onse.
29Ndipo Efuremu sanaingitse Akanani okhala m'Gezere; koma Akanani anakhala m'Gezere pakati pao.
30Zebuloni sanaingitse nzika za ku Kitironi, kapena za ku Nahaloli; koma Akanani anakhala pakati pao, nawasonkhera.
31Asere sanaingitse nzika za ku Ako, kapena nzika za ku Sidoni, kapena a Alabu, kapena a Akizibu, kapena a Heliba, kapena a Afiki, kapena a Rehobu; 32koma Asere anakhala pakati pa Akanani nzika za kudziko; pakuti sanawaingitse.
33Nafutali sanaingitse nzika za ku Betesemesi, kapena nzika za ku Betanati; koma anakhala pakati pa Akanani, nzika za kudziko; koma nzika za ku Betesemesi, ndi a ku Betanati zinawasonkhera.
34Ndipo Aamori anakankha ana a Dani akhale kumapiri pakuti sanawalole atsikire kuchigwa; 35Aamori anakhumbanso kukhala kuphiri la Heresi, ku Ayaloni, ndi ku Saalibimu; koma dzanja la a m'nyumba ya Yosefe linawalaka, nakhala iwo akupereka msonkho. 36Ndipo malire a Aamori anayambira pokwerera pa Akarabimu, pathanthwe ku Sela, ndi pokwererapo.
Currently Selected:
OWERUZA 1: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi