YouVersion Logo
Search Icon

OWERUZA 2

2
Mngelo wa Mulungu adzudzula Aisraele
1 # Gen. 17.7 Ndipo mthenga wa Yehova anakwera kuchokera ku Giligala kunka ku Bokimu. Ndipo anati, Ndinakukweretsani kuchokera ku Ejipito, ndi kulowetsa inu m'dziko limene ndinalumbirira makolo anu; ndipo ndinati, Sindidzathyola chipangano changa nanu ku nthawi yonse; 2#Deut. 7.2; 12.3ndipo inu, musamachita pangano ndi nzika za m'dziko ili; muzigamula maguwa ao a nsembe. Koma simunamvera mau anga; mwachichita ichi chifukwa ninji? 3#Num. 33.55Chifukwa chakenso ndinati, Sindidzawapirikitsa kuwachotsa pamaso panu; koma adzakhala ngati minga m'nthiti zanu, ndi milungu yao idzakhalira inu msampha. 4Ndipo kunali, pamene mthenga wa Yehova ananena mau awa kwa ana onse a Israele, anthuwo anakweza mau ao, nalira misozi. 5Potero analitcha dzina la malowo Bokimu: namphera Yehova nsembe pomwepo.
Aisraele alowerera atamwalira Yoswa
6Pamene Yoswa atawalola anthu amuke, ana a Israele anamuka, yense ku cholowa chake, dziko likhale laolao. 7Ndipo anthuwo anatumikira Yehova masiku onse a Yoswa, ndi masiku onse a akuluakulu otsala atafa Yoswa, amene adaona ntchito yaikulu yonse ya Yehova anaichitira Israele. 8Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Yehova anafa wa zaka zake zana ndi khumi. 9Ndipo anamuika m'malire a cholowa chake m'Timnati-Heresi, ku mapiri a Efuremu, kumpoto kwa phiri la Gaasi. 10#1Sam. 2.12; Agal. 4.8; 2Ate. 1.8Ndiponso mbadwo uwu wonse unasonkhanidwa kuikidwa kwa makolo ao; nuuka mbadwo wina pambuyo pao; wosadziwa Yehova kapena ntchitoyi adaichitira Israele.
11Ndipo ana a Israele anachita choipa pamaso pa Yehova, natumikira Abaala; 12#Deut. 31.16nasiya Yehova Mulungu wa makolo ao, amene adawatulutsa m'dziko la Ejipito, natsata milungu ina, milungu ya mitundu ya anthu okhala pozungulira pao, naigwadira; nautsa mkwiyo wa Yehova. 13Ndipo anasiya Yehova, natumikira Baala ndi Asitaroti. 14#Yos. 7.12Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele, ndipo anawapereka m'manja a ofunkha kuti awafunkhe; nawagulitsa m'dzanja la adani ao akuwazungulira osakhozanso iwowo kuima pamaso pa adani ao. 15Kuli konse anatuluka, dzanja la Yehova linawakhalira moipa, monga Yehova adanena, ndi monga Yehova adawalumbirira; nasautsika kwambiri iwowa. 16#1Sam. 12.11; Mac. 13.20Ndipo Yehova anautsa oweruza, amene anawapulumutsa m'dzanja la iwo akuwafunkha. 17#Eks. 34.15-16Koma sanamvere angakhale oweruza ao, pakuti anamuka kupembedza milungu ina, naigwadira; anapatuka msanga m'njira yoyendamo makolo ao, pomvera malamulo a Yehova; sanatero iwowa. 18#Deut. 32.36Ndipo pamene Yehova anawaukitsira oweruza, Yehova anakhala naye woweruzayo, nawapulumutsa m'dzanja la adani ao masiku onse a woweruzayo; pakuti Yehova anagwidwa chisoni pa kubuula kwao chifukwa cha iwo akuwapsinja ndi kuwatsendereza. 19Koma kunali atafa woweruzayo anabwerera m'mbuyo, naposa makolo ao ndi kuchita moipitsa, ndi kutsata milungu ina kuitumikira ndi kuigwadira, sanaleke kanthu ka machitidwe ao kapena ka njira yao yatcheni. 20#Yos. 23.16Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele; nati Iye, Popeza mtundu uwu unalakwira chipangano changa chimene ndinalamulira makolo ao, osamvera mau anga; 21Inenso sindionjeza kuingitsa pamaso pao a mitundu ina imene Yoswa adaisiya pakufa iyeyu; 22#Gen. 22.1; Deut. 8.2; Mas. 17.3kuti ndiyese nayo Israele ngati adzasunga njira ya Yehova kuyendamo monga anaisunga makolo ao, kapena iai. 23Motero Yehova analeka mitundu iyi osaiingitsa msanga, ndipo sadaipereka m'dzanja la Yoswa.

Currently Selected:

OWERUZA 2: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in