YouVersion Logo
Search Icon

OWERUZA 3

3
Amitundu otsala akuyesa nao Aisraele
1Ndipo iyo ndiyo mitundu ya anthu anaisiyapo Yehova kuyesa nayo Israele, ndiwo onse amene sanadziwe nkhondo zonse za Kanani; 2chifukwa chake ndicho chokha chakuti adziwitse mibadwo ya ana a Israele ndi kuwaphunzitsa nkhondo, ngakhale iwo okhaokha osaidziwa konse kale; 3anasiya mafumu asanu a Afilisti ndi Akanani onse, ndi Asidoni, ndi Ahivi okhala m'phiri la Lebanoni, kuyambira phiri la Baala-Heremoni mpaka polowera ku Hamati. 4#Ower. 2.22Amenewo anakhala choyesera Israele kuti Yehova adziwe ngati adzamvere malamulo ake, amene analamulira makolo ao mwa dzanja la Mose. 5Ndipo ana a Israele anakhala pakati pa Akanani, Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi; 6#Eks. 34.16; Ezr. 9.12nakwatira ana akazi a iwowa, napereka ana ao akazi kwa ana amuna a iwowa natumikira milungu yao.
Otiniyeli alanditsa Aisraele m'dzanja la Kusani
7Ndipo ana a Israele anachita choipa pamaso pa Yehova, naiwala Yehova Mulungu wao, natumikira Abaala ndi zifanizo. 8Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele ndipo anawagulitsa m'dzanja la Kusani-Risataimu, mfumu ya Mesopotamiya; ndi ana a Israele anatumikira Kusani-Risataimu zaka zisanu ndi zitatu. 9#Ower. 1.13Ndipo pamene ana a Israele anafuula kwa Yehova, Yehova anaukitsira ana a Israele mpulumutsi amene anawapulumutsa, ndiye Otiniyele mwana wa Kenazi, mng'ono wake wa Kalebe. 10Ndipo unamdzera mzimu wa Yehova, iye naweruza Israele, natuluka kunkhondo; napereka Yehova Kusani-Risataimu mfumu ya Mesopotamiya m'dzanja lake; ndi dzanja lake linamlaka Kusani-Risataimu. 11Pamenepo dziko linapumula zaka makumi anai; ndi Otiniyele mwana wa Kenazi anafa.
Ehudi awalanditsa m'dzanja la Egiloni
12Koma ana a Israele anaonjezanso kuchita choipa pamaso pa Yehova; pamenepo Yehova analimbitsa Egiloni mfumu ya Mowabu pa Israele, popeza anachita choipa pamaso pa Yehova. 13#Ower. 1.16Ndipo anadzisonkhanitsira ana a Amoni ndi a Amaleke, namuka nakantha Israele, nalanda mudzi wa m'migwalangwa nakhalamo. 14Ndipo ana a Israele anatumikira Egiloni mfumu ya Mowabu zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu. 15Koma pamene ana a Israele anafuula kwa Yehova, Yehova anawaukitsira mpulumutsi, Ehudi mwana wa Gera, Mbenjamini, munthu wamanzere, ndipo ana a Israele anatumiza mtulo m'dzanja lake kwa Egiloni mfumu ya Mowabu. 16Ndipo Ehudi anadzisulira lupanga lakuthwa konsekonse utali wake mkono; nalimangirira pansi pa zovala zake pa ntchafu ya kulamanja. 17Ndipo anapereka mtulo kwa Egiloni, mfumu ya Mowabu; koma Egiloni ndiye munthu wonenepa ndithu. 18Ndipo atatha kupereka mtulowo, anauza anthu onyamula mtulo achoke. 19Koma iye mwini anabwerera pa mafano osema ali ku Giligala, nati, Ndili nao mau achinsinsi kwa inu, mfumu. Nati iye, Khalani chete. Ndipo anatuluka onse akuimapo. 20Ndipo Ehudi anamdzera alikukhala pa yekha m'chipinda chosanja chopitidwa mphepo. Nati Ehudi, Ndili nao mau a Mulungu akukuuzani. Nauka iye pa mpando wake. 21Ndipo Ehudi anatulutsa dzanja lake lamanzere nagwira lupanga ku ntchafu ya kulamanja nampyoza m'mimba mwake; 22ndi chigumbu chake chinalowa kutsata mpeni wake; ndi mafuta anaphimba mpeniwo, pakuti sanasolole lupanga m'mimba mwake; nilituluka kumbuyo. 23Pamenepo Ehudi anatuluka kukhonde namtsekera pamakomo pa chipinda chosanja nafungulira. 24Ndipo atatuluka iye, anadza akapolo ake; napenya, ndipo taonani pamakomo pa chipinda chosanja mpofungulira; nati iwo, Angophimba mapazi m'chipinda chake chosanja chopitidwa mphepo. 25Ndipo analindirira mpaka anachita manyazi; koma taonani, sanatsegule pamakomo pa chipinda chosanja. Pamenepo anatenga mfungulo natsegula; ndipo taonani, mbuye wao wagwa pansi, wafa. 26Ndipo Ehudi anapulumuka pakuchedwa iwo, napitirira pa mafano osema, napulumuka kufikira Seira. 27Ndipo kunali, pakufika iye anaomba lipenga ku mapiri a Efuremu; ndi ana a Israele anatsika naye kuchokera kumapiri, nawatsogolera iye. 28#Ower. 12.5; 1Sam. 17.47Ndipo ananena nao, Nditsateni ine, pakuti Yehova wapereka adani anu Amowabu m'manja mwanu. Ndipo anatsika ndi kumtsata, natsekereza Amowabu madooko a Yordani, osalola mmodzi aoloke. 29Ndipo anakantha Amowabu nyengo ija anthu zikwi khumi, onsewa anthu amoyo, ndi ngwazi; ndipo sanapulumuke ndi mmodzi yense. 30Motero anagonjetsa Mowabu tsiku lija pansi pa dzanja la Israele. Ndipo dziko linapumula zaka makumi asanu ndi atatu.
31Atapita iye kunali Samigara, mwana wa Anati amene anakantha Afilisti mazana asanu ndi limodzi ndi mtoso wa ng'ombe; nayenso anapulumutsa Israele.

Currently Selected:

OWERUZA 3: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for OWERUZA 3