YouVersion Logo
Search Icon

YOSWA 2

2
Yoswa atuma anthu awiri azonde Yeriko
1 # Aheb. 11.31 Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, ali ku Sitimu, anatuma amuna awiri mosadziwika kukazonda, ndi kuti, Mukani, mulipenye dzikolo, ndi ku Yeriko. Ndipo anamuka nalowa m'nyumba ya mkazi wadama, dzina lake Rahabi, nagona momwemo. 2Ndipo wina anaiuza mfumu ya Yeriko, kuti, Taonani, usiku uno alowa muno amuna a ana a Israele, kulizonda dziko. 3Ndipo mfumu ya Yeriko inatuma wina kwa Rahabi, ndi kuti, Tulutsa amunawo anafika kwanu, amene analowa m'nyumba mwako; popeza anadzera kulizonda dziko lonse. 4Koma mkaziyo anatenga amuna awiriwo, nawabisa; natero, Inde, amunawo anandifikira; koma sindinadziwa uko afuma; 5ndipo m'mene akadati atseke pachipata, kutada, anatuluka amunawo; uko anamuka amunawo osakudziwa ine; muwalondole msanga, pakuti mudzawapeza. 6Koma adawakweretsa patsindwi, nawabisa ndi mitengo yanthamza yoyanika patsindwi. 7Ndipo amunawo anawalondola pa njira ya ku Yordani yonka kudooko; ndipo atatuluka akuwalondola, anatseka pachipata. 8Koma asanagone iwo, anawakwerera patsindwi iye, 9#Gen. 35.5; Eks. 23.27nati kwa amunawo, Ndidziwa kuti Yehova wakupatsani dzikoli, ndi kuti kuopsa kwanu kwatigwera, ndi kuti okhala m'dziko onse asungunuka pamaso panu. 10#Eks. 14.21; Num. 21.24-35Popeza tidamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a m'Nyanja Yofiira pamaso panu, muja mudatuluka m'Ejipito; ndi chija munachitira mafumu awiri a Aamori okhala tsidya la Yordani, ndiwo Sihoni ndi Ogi, amene mudawaononga konse. 11#Deut. 4.39Ndipo titamva ichi mitima yathu inasungunuka; analibenso mtima ndi mmodzi yense, chifukwa cha inu; pakuti Yehova Mulungu wanu, ndiye Mulungu wa m'mwamba umo, ndi pa dziko lapansi. 12Ndipo tsopano, mundilumbiriretu kwa Yehova, popeza ndakuchitirani chifundo, kuti inunso mudzachitira chifundo a m'nyumba ya atate wanga ndi kundipatsa chizindikiro choona, 13kuti mudzawasunga ndi moyo atate wanga ndi mai wanga, ndi alongo anga ndi abale anga, ndi zonse ali nazo, ndi kupulumutsa miyoyo yathu kuimfa. 14#Ower. 1.24Ndipo amunawo anati kwa iye, Moyo wathu ndiwo moyo wanu, mukapanda kuwulula chodzera ife; ndipo kudzakhala kuti, pakutipatsa ife dziko ili Yehova, tidzakuchitira chifundo ndi choonadi. 15#Mac. 9.25Pamenepo anawatsitsa pazenera ndi chingwe; popeza nyumba yake inali pa linga la mudzi, nakhala iye palingapo. 16Ndipo anati kwa iwo, Mukani kuphiri, olondola angakupezeni; mubisale kumeneko masiku atatu, mpaka atabwerera olondolawo, pamenepo muyende ulendo wanu. 17Ndipo amunawo anati kwa iye, Sitidzachimwira lumbiro lako ili watilumbiritsali. 18#Yos. 6.23Taona, tikadzalowa m'dzikomo ife, uzimanga chingwe ichi chofiira pazenera pamene watitsitsira; ndipo udzasonkhanitsa m'nyumbamo atate wako ndi mai wako ndi abale ako ndi a m'nyumba onse a atate wako. 19#Mat. 27.25Ndipo kudzakhala kuti aliyense akadzatuluka pa khomo la nyumba yako kubwalo, imfa imeneyi ndi yake, tilibe kupalamula ife; koma aliyense adzakhala ndi iwe m'nyumba, likamfikira dzanja, imfa imeneyi ndi yathu. 20Koma ukawulula chodzera ifecho tidzamasukira lumbiro lako watilumbiritsali. 21Nati iye, Momwemo, monga mwa mau anu. Ndipo anawauza amuke, iwo namuka; namanga iye chingwe chofiiracho pazenera. 22Ndipo anayenda iwo, nafika kuphiri, nakhalako masiku atatu mpaka atabwerera olondolawo; popeza olondolawo anawafunafuna panjira ponse, osawapeza. 23Pamenepo amuna awiriwo anabwerera, natsika m'phirimo naoloka, nafika kwa Yoswa mwana wa Nuni, namfotokozera zonse zidawagwera. 24#Eks. 23.31Ndipo anati kwa Yoswa, Zoonadi, Yehova wapereka dziko lonse m'manja mwathu; ndiponso nzika zonse zasungunuka pamaso pathu.

Currently Selected:

YOSWA 2: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in