YouVersion Logo
Search Icon

YOSWA 3

3
Aisraele aoloka Yordani
1Ndipo Yoswa analawirira mamawa, kuchoka ku Sitimu, nafika ku Yordani, iye ndi ana onse a Israele; nagona komweko, asanaoloke. 2Ndipo kunali atapita masiku atatu, akapitao anapita pakati pa chigono; 3nalamulira anthu, ndi kuti, Mukadzaona likasa la chipangano la Yehova Mulungu wanu, ndi ansembe Aleviwo atalisenza, pamenepo muchoke kwanu ndi kulitsata. 4#Eks. 19.12Koma pakhale dera pakati pa inu ndi ilo, monga mikono zikwi ziwiri poliyesa; musaliyandikire, kuti mudziwe njira imene muziyendamo; popeza simunapita njirayi kufikira lero. 5#Eks. 19.10, 14; Yow. 2.16Ndipo Yoswa ananena kwa anthu, Mudzipatule, pakuti mawa Yehova adzachita zodabwitsa pakati pa inu. 6Ndipo Yoswa anati kwa ansembe, Senzani likasa la chipangano, nimuoloke pamaso pa anthu. Nasenza iwo likasa la chipangano, natsogolera anthu. 7#Yos. 4.14; 2Mbi. 1.1Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Lero lino ndidzayamba kukukuza pamaso pa Aisraele onse, kuti adziwe, kuti monga momwe ndinakhalira ndi Mose, momwemo ndidzakhala ndi iwe. 8#Yos. 3.17Ndipo uzilamulira ansembe akunyamula likasa la chipangano, ndi kuti, Pamene mufika kumphepete kwa madzi a Yordani muziima m'Yordani.
9Ndipo Yoswa anati kwa ana a Israele, Idzani kuno, mumve mau a Yehova Mulungu wanu. 10#Deut. 5.26; 1Sam. 17.26; Mat. 16.16; 1Ate. 1.9Nati Yoswa, Ndi ichi mudzadziwa kuti Mulungu wamoyo ali pakati pa inu, ndi kuti adzapirikitsa ndithu pamaso panu Akanani, ndi Ahiti, ndi Ahivi, ndi Aperizi, ndi Agirigasi, ndi Aamori, ndi Ayebusi. 11Taonani, likasa la chipangano la Ambuye wa dziko lonse lapansi lioloka Yordani pamaso panu. 12Ndipo tsono, mudzitengere amuna khumi ndi awiri mwa mafuko a Israele, fuko limodzi mwamuna mmodzi. 13#Zek. 4.14Ndipo kudzakhala, akaima mapazi a ansembe akusenza likasa la Yehova Ambuye wa dziko lonse, m'madzi a Yordani, adzadulidwa madziwo, ndiwo madzi ochokera kumagwero, nadzaima mulu umodzi. 14#Mac. 7.44-45Ndipo kunali pochoka anthu ku mahema ao kukaoloka Yordani, ansembe anasenza likasa la chipangano pamaso pa anthu. 15Ndipo pamene iwo akusenza likasa anafika ku Yordani, nathibika m'mphepete mwa madzi mapazi a ansembe akusenza likasa, pakuti Yordani asefuka m'magombe ake onse, nyengo yonse ya masika, 16pamenepo madzi ochokera kumagwero anaima, nauka ngati mulu, kutalitu ku Adama, ndiwo mudzi wa ku mbali ya Zaretani; koma madzi akutsikira kunka ku nyanja ya chidikha, ndiyo Nyanja ya Mchere, anadulidwa konse; ndipo anthu anaoloka pandunji pa Yeriko. 17#Eks. 14.29Ndipo ansembe akulisenza likasa la chipangano la Yehova, anaima pouma pakati pa Yordani, ndi Aisraele onse anaoloka pouma mpaka mtundu wonse unatha kuoloka Yordani.

Currently Selected:

YOSWA 3: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in