YOHANE 16
16
Awachenjeza za kuzunzidwa
(Mat. 24.9-10; Luk. 21.16-19)
1 #
Mat. 11.6
Izi ndalankhula ndi inu kuti mungakhumudwitsidwe. 2#Yoh. 12.42; Mac. 8.1; 9.1Adzakutulutsani m'masunagoge, koma ikudza nthawi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikira Mulungu. 3#Yoh. 15.21Ndipo izi adzachita, chifukwa sanadziwa Atate, kapena Ine. 4#Yoh. 14.28Koma zinthu izi ndalankhula ndi inu kuti ikadza nthawi yao, mukakumbukire kuti ndinakuuzani. Koma izi sindinanena kwa inu kuyambira pachiyambi, chifukwa ndinali pamodzi ndi inu. 5#Yoh. 14.28Koma tsopano ndimuka kwa Iye wondituma Ine; ndipo palibe wina mwa inu andifunsa Ine, Munka kuti? 6#Yoh. 14.1Koma chifukwa ndalankhula izi ndi inu chisoni chadzala mumtima mwanu.
Chomwe Mzimu Woyera adzachitira anthu
7 #
Mac. 2.33
Koma ndinena Ine choonadi ndi inu; kuyenera kwa inu kuti ndichoke Ine; pakuti ngati sindichoka, Nkhosweyo sadzadza kwa inu; koma ngati ndipita ndidzamtuma Iye kwa inu. 8Ndipo atadza Iyeyo, adzatsutsa dziko lapansi za machimo, ndi za chilungamo, ndi za chiweruziro; 9za machimo, chifukwa sakhulupirira Ine; 10za chilungamo, chifukwa ndinka kwa Atate, ndipo simundionanso; 11za chiweruzo, chifukwa mkulu wa dziko ili lapansi waweruzidwa. 12Ndili nazo zambirinso zakunena kwa inu, koma simungathe kuzisenza tsopano lino. 13#Yoh. 14.26; 1Yoh. 2.20, 27Koma atadza Iyeyo, Mzimu wa choonadi, adzatsogolera inu m'choonadi chonse; pakuti sadzalankhula za Iye mwini; koma zinthu zilizonse adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zilinkudza adzakulalikirani. 14Iyeyo adzalemekeza Ine; chifukwa adzatenga za mwa Ine, nadzalalikira kwa inu. 15#Mat. 11.27Zinthu zilizonse Atate ali nazo ndi zanga; chifukwa chake ndinati, kuti atenga za mwa Ine, nadzalalikira kwa inu.
Yesu anena za imfa, kuuka, ndikubwera kwake
16 #
Yoh. 13.3, 33 Katsala kanthawi, ndipo simundionanso Ine, ndipo kanthawinso, ndipo mudzandiona Ine. 17Mwa ophunzira ake tsono anati wina ndi mnzake, Ichi nchiyani chimene anena ndi ife, Kanthawi ndipo simundiona; ndiponso kanthawi, ndipo mudzandiona; ndipo, chifukwa ndimuka kwa Atate? 18Chifukwa chake ananena. Ichi nchiyani chimene anena, Kanthawi? Sitidziwa chimene alankhula. 19Yesu anazindikira kuti analikufuna kumfunsa Iye, ndipo anati kwa iwo, Kodi mulikufunsana wina ndi mnzake za ichi, kuti ndinati, Kanthawi ndipo simundiona Ine, ndiponso kanthawi nimudzandiona Ine? 20Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mudzalira ndi kubuma maliro inu, koma dziko lapansi lidzakondwera; mudzachita chisoni inu, koma chisoni chanu chidzasandulika chimwemwe. 21Mkazi pamene akuti abale ali nacho chisoni, chifukwa yafika nthawi yake; koma pamene wabala mwana, sakumbukiranso kusaukako, chifukwa cha chimwemwe kuti wabadwa munthu kudziko lapansi. 22#Luk. 24.41, 45Ndipo inu tsono muli nacho chisoni tsopano lino, koma ndidzakuonaninso, ndipo mtima wanu udzakondwera, ndipo palibe wina adzachotsa kwa inu chimwemwe chanu. 23#Yoh. 15.16Ndipo tsiku limenelo simudzandifunsa kanthu. Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Ngati mudzapempha Atate kanthu, adzakupatsani inu m'dzina langa. 24#Yoh. 15.11Kufikira tsopano simunapempha kanthu m'dzina langa; pemphani, ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikwaniridwe.
25Zinthu izi ndalankhula ndi inu m'mafanizo; ikudza nthawi imene sindidzalankhula ndi inu m'mafanizo, koma ndidzakulalikirani inu m'mafanizo, koma ndidzakulalikirani inu momveka za Atate. 26#Yoh. 16.23Tsiku limenelo mudzapempha m'dzina langa; ndipo sindinena kwa inu kuti Ine ndidzafunsira inu kwa Atate; 27#Yoh. 14.21, 23; 17.8pakuti Atate yekha akonda inu, chifukwa inu mwandikonda Ine, ndi kukhulupirira kuti Ine ndinatuluka kwa Atate. 28#Yoh. 13.3Ndinatuluka mwa Atate, ndipo ndadza kudziko lapansi: ndilisiyanso dziko lapansi, ndipo ndipita kwa Atate. 29Ophunzira ake ananena, Onani, tsopano mulankhula zomveka, ndipo mulibe kunena chiphiphiritso. 30#Yoh. 21.17Tsopano tidziwa kuti mudziwa zonse, ndipo mulibe kusowa kuti wina akafunse Inu; mwa ichi tikhulupirira kuti munatuluka kwa Mulungu. 31Yesu anayankha iwo, Kodi mukhulupirira tsopano? 32#Mat. 26.13; Mrk. 14.50; Yoh. 8.29Onani ikudza nthawi, ndipo yafika, imene mudzabalalitsidwa, yense ku zake za yekha, ndipo mudzandisiya Ine pa ndekha. Ndipo sindikhala pa ndekha, chifukwa Atate ali pamodzi ndi Ine, 33#Yes. 9.6; Yoh. 15.18-21; Aro. 8.37; Akol. 1.20; 1Yoh. 4.4Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalingonjetsa dziko lapansi Ine.
Currently Selected:
YOHANE 16: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi