YOHANE 17
17
Yesu apempherera ophunzira ake
1 #
Yoh. 12.13
Zinthu izi analankhula Yesu; ndipo m'mene anakweza maso ake Kumwamba, anati, Atate, yafika nthawi; lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanu akulemekezeni Inu; 2#Mat. 11.27monga mwampatsa Iye ulamuliro pa thupi lililonse, kuti onse amene mwampatsa Iye, awapatse iwo moyo wosatha. 3#Yoh. 3.34; 1Yoh. 5.20Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Khristu amene munamtuma. 4#Yoh. 5.36; 9.3Ine ndalemekeza Inu pa dziko lapansi, m'mene ndinatsiriza ntchito imene munandipatsa ndichite. 5#Yoh. 1.1-2Ndipo tsopano, Atate Inu, lemekezani Ine ndi Inu nokha ndi ulemerero umene ndinali nao ndi Inu lisanakhale dziko lapansi. 6#Yoh. 17.2, 9, 11Ndalionetsera dzina lanu kwa anthu amene mwandipatsa Ine m'dziko lapansi; anali anu, ndipo mwandipatsa Ine iwo; ndipo adasunga mau anu. 7Azindikira tsopano kuti zinthu zilizonse zimene mwandipatsa Ine zichokera kwa Inu; 8#Yoh. 8.28; 16.27, 30chifukwa mau amene munandipatsa Ine ndinapatsa iwo; ndipo analandira, nazindikira koona kuti ndinatuluka kwa Inu, ndipo anakhulupirira kuti Inu munandituma Ine. 9Ine ndiwapempherera iwo; sindipempherera dziko lapansi, koma iwo amene mwandipatsa Ine, 10#Yoh. 16.15chifukwa ali anu: ndipo zanga zonse zili zanu, ndi zanu zili zanga; ndipo ndilemekezedwa mwa iwo. 11#1Pet. 1.5; Yud. 1Sindikhalanso m'dziko lapansi, koma iwo ali m'dziko lapansi, ndipo Ine ndidza kwa Inu. Atate Woyera, sungani awa m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine, kuti akhale mmodzi, monga Ife. 12#Yoh. 6.39, 70; 18.9; Mac. 1.20Pamene ndinakhala nao, Ine ndinalikuwasunga iwo m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine; ndipo ndinawasunga, ndipo sanatayika mmodzi yense wa iwo, koma mwana wa chitayiko, kuti lembo likwaniridwe. 13Koma tsopano ndidza kwa Inu; ndipo izi ndilankhula m'dziko lapansi, kuti akhale nacho chimwemwe changa chokwaniridwa mwa iwo okha. 14#Yoh. 15.18-19; 17.8Ine ndawapatsa iwo mau anu; ndipo dziko lapansi, linadana nao, chifukwa sakhala a dziko lapansi, monga Ine sindikhala wa dziko lapansi. 15#Mat. 6.13; Agal. 1.4Sindipempha kuti muwachotse iwo m'dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo. 16Siali a dziko lapansi monga Ine sindili wa dziko lapansi. 17#Aef. 5.26Patulani iwo m'choonadi; mau anu ndi choonadi. 18#Yoh. 20.21Monga momwe munandituma Ine kudziko lapansi, Inenso ndinatuma iwo kudziko lapansi. 19#1Ako. 1.2, 30Ndipo chifukwa cha iwo Ine ndidzipatula ndekha kuti iwonso akhale opatulidwa m'choonadi. 20Koma sindipempherera iwo okha, komanso iwo akukhulupirira Ine chifukwa cha mau ao; 21#Yoh. 10.16, 38; Aro. 12.5kuti onse akakhale amodzi, monga Inu Atate mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, kuti iwonso akakhale mwa Ife: kuti dziko lapansi likakhulupirire kuti Inu munandituma Ine. 22#1Yoh. 1.3Ndipo ulemerero umene mwandipatsa Ine ndapatsa iwo; kuti akhale amodzi, monga Ife tili mmodzi; 23#Akol. 3.14Ine mwa iwo, ndi Inu mwa Ine, kuti akhale angwiro mwa mmodzi; kuti dziko lapansi lizindikire kuti Inu munandituma Ine, nimunawakonda iwo, monga momwe munakonda Ine. 24#Yoh. 12.26; 14.3; 17.5; 1Ate. 4.17Atate, amene mwandipatsa Ine, ndifuna kuti, kumene ndili Ine, iwonso akhale pamodzi ndi Ine; kuti ayang'anire ulemerero wanga, umene mwandipatsa Ine; pakuti munandikonda Ine lisanakhazikike dziko lapansi. 25#Yoh. 7.29; 15.21; 16.27Atate wolungama, dziko lapansi silinadziwa Inu, koma Ine ndinadziwa Inu; ndipo iwo anazindikira kuti munandituma Ine; 26#Yoh. 15.9, 15ndipo ndinazindikiritsa iwo dzina lanu, ndipo ndidzalizindikiritsa; kuti chikondi chimene munandikonda nacho chikhale mwa iwo, ndi Ine mwa iwo.
Currently Selected:
YOHANE 17: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi