YOHANE 15
15
Mpesa ndi nthambi zake
1Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate wanga ndiye wam'munda. 2#Mat. 15.13Nthambi iliyonse ya mwa Ine yosabala chipatso, aichotsa; ndi iliyonse yakubala chipatso, aisadza, kuti ikabale chipatso chochuluka. 3#Yoh. 17.17Mwakhala okonzeka tsopano inu chifukwa cha mau amene ndalankhula ndi inu. 4Khalani mwa Ine, ndi Ine mwa inu. Monga nthambi siingathe kubala chipatso pa yokha, ngati siikhala mwampesa; motere mulibe inunso ngati simukhala mwa Ine. 5#Afi. 1.11Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi zake: wakukhala mwa Ine, ndi Ine mwa iye, ameneyo abala chipatso chambiri; pakuti kopanda Ine simungathe kuchita kanthu. 6#Mat. 7.19Ngati wina sakhala mwa Ine, watayika kunja monga nthambi, nafota; ndipo azisonkhanitsa nazitaya kumoto, nazitentha. 7#Yoh. 14.13-14Ngati mukhala mwa Ine, ndi mau anga akhala mwa inu, pemphani chilichonse chimene muchifuna ndipo chidzachitika kwa inu. 8#Mat. 5.16Mwa ichi alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale chipatso chambiri; ndipo mudzakhala ophunzira anga. 9Monga momwe Atate wandikonda Ine, Inenso ndakonda inu; khalani m'chikondi changa. 10#Yoh. 14.15, 21, 23Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m'chikondi changa; monga Iye ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m'chikondi chake. 11#Yoh. 16.24Izi ndalankhula ndi inu, kuti chimwemwe changa chikhale mwa inu, ndi kuti chimwemwe chanu chidzale. 12#1Yoh. 3.11Lamulo langa ndi ili, kuti mukondane wina ndi mnzake, monga ndakonda inu. 13#Yoh. 10.11, 15Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake. 14Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulani inu.
Chiyanjano chatsopano
15 #
Mac. 20.27
Sinditchanso inu akapolo; chifukwa kapolo sadziwa chimene mbuye wake achita; koma ndatcha inu abwenzi; chifukwa zonse zimene ndazimva kwa Atate wanga ndakudziwitsani. 16#1Yoh. 4.10, 19; Yoh. 15.7Inu simunandisankha Ine, koma Ine ndinakusankhani inu, ndipo ndinakuikani, kuti mukamuke inu ndi kubala chipatso, ndi kuti chipatso chanu chikhale; kuti chimene chilichonse mukapempha Atate m'dzina langa akakupatseni inu. 17#1Yoh. 3.11Zinthu izi ndilamula inu, kuti mukondane wina ndi mnzake.
Wokhulupirira pokhala pa dziko lapansi
18 #
1Yoh. 3.1, 13 Ngati dziko lapansi lida inu, mudziwa kuti lidada Ine lisanayambe kuda inu. 19#Yoh. 17.14; 1Yoh. 4.5Mukadakhala a dziko lapansi, dziko lapansi likadakonda zake za lokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma Ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, chifukwa cha ichi likudani inu. 20#Mat. 10.24Kumbukirani mau amene Ine ndinanena kwa inu, Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake. Ngati anandilondalonda Ine, adzakulondalondani inunso; ngati anasunga mau anga, adzasunga anunso. 21#Mat. 10.22Koma izi zonse adzakuchitirani chifukwa cha dzina langa, chifukwa sadziwa wondituma Ine. 22#Yoh. 9.41Sindikadadza ndi kulankhula nao sakadakhala nalo tchimo; koma tsopano alibe chowiringula pa machimo ao. 23#1Yoh. 2.23Iye wondida Ine, adanso Atate wanga. 24#Yoh. 9.32Sindikadachita mwa iwo ntchito zosachita wina, sakadakhala nalo tchimo; koma tsopano anaona, nada Ine ndi Atate wanganso. 25#Mas. 69.4Koma chitero, kuti mau olembedwa m'chilamulo chao akwaniridwe, kuti, Anandida Ine kopanda chifukwa.
Mzimu Woyera ndi ophunzira omwe adzachita umboni
26 #
Yoh. 14.17, 26; 16.7, 13 Koma pamene wafika Nkhoswe, amene Ine ndidzamtuma kwa inu kuchokera kwa Atate, ndiye Mzimu wa choonadi, amene atuluka kwa Atate, Iyeyu adzandichitira Ine umboni. 27#Luk. 1.2; Mac. 1.8Ndipo inunso muchita umboni, pakuti muli ndi Ine kuyambira chiyambi.
Currently Selected:
YOHANE 15: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi