YEREMIYA 7
7
Mneneri alikuima pa chipata cha Kachisi, atchula mau akulonjeza ndi akuopsa
1Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, kuti, 2#Yer. 26.2Ima m'chipata cha nyumba ya Yehova, lalikira m'menemo mau awa, ndi kuti, Tamvani mau a Yehova, inu nonse a Yuda, amene alowa m'zipata izi kuti mugwadire Yehova. 3#Yer. 26.13Yehova wa makamu atero, Mulungu wa Israele, Konzani njira zanu ndi machitidwe anu, ndipo ndidzakukhalitsani inu m'malo ano. 4#Mik. 3.11Musakhulupirire mau onama, kuti, Kachisi wa Yehova, Kachisi wa Yehova, Kachisi wa Yehova ndi awa. 5#Yer. 22.3Pakuti mukakonzatu njira zanu ndi machitidwe anu; ndi kuweruzatu milandu ya munthu ndi mnansi wake; 6ndi kuleka kutsendereza mlendo, ndi wamasiye, ndi mkazi wamasiye, osakhetsa mwazi wosachimwa m'malo muno, osatsata milungu ina ndi kudziipitsa nayo; 7#Deut. 4.40ndipo ndidzakukhazikani inu m'malo muno, m'dziko limene ndinapatsa makolo anu, kuyambira kale lomwe kufikira muyaya. 8#Yer. 7.4Taonani, mukhulupirira mau onama, osapindulitsa. 9#1Maf. 18.21Kodi mudzapha, ndi kuba, ndi kuchita chigololo, ndi kulumbira zonama, ndi kupereka nsembe kwa Baala, ndi kutsata milungu ina imene simunaidziwa, 10#Ezk. 23.39ndi kudza ndi kuima pamaso panga m'nyumba yino, imene itchedwa dzina langa, ndi kuti, Talanditsidwa; kuti muchite zonyansa izi? 11#Yes. 56.7; Mat. 21.13Kodi nyumba yino, imene itchedwa dzina langa, ikhala phanga la okwatula pamaso panu? Taona, Ine ndachiona, ati Yehova. 12#1Sam. 4.3-12Koma pitani tsopano kumalo anga amene anali m'Silo, m'mene ndinaikamo dzina langa poyamba paja, ndi kuona chimene ndinachitira chifukwa cha zoipa za anthu anga Israele. 13#Miy. 1.24Ndipo tsopano, chifukwa munachita ntchito zonsezi, ati Yehova, ndipo ndinanena kwa inu, ndi kuuka mamawa ndi kunena, koma simunamva; ndipo ndinakuitanani inu, koma simunayankha; 14#1Sam. 4.3-12chifukwa chake ndidzaichitira nyumba iyi, imene itchedwa dzina langa, imene mukhulupirirayi, ndipo ndidzachitira malo amene ndinakupatsani inu ndi makolo anu, monga ndinachitira Silo. 15#2Maf. 17.23Ndipo ndidzakuchotsani inu pamaso panga, monga ndinachotsa abale anu onse, mbeu zonse za Efuremu.
16 #
Eks. 32.10; Yer. 15.1 Chifukwa chake iwe usapempherere anthu awa, usawakwezere iwo mfuu kapena pemphero, usandipembedze; pakuti Ine sindidzakumvera iwe. 17Kodi suona iwe chimene achichita m'midzi ya Yuda ndi m'miseu ya Yerusalemu? 18#Yer. 4.17, 19Ana atola nkhuni, atate akoleza moto, akazi akanyanga ufa, kuti aumbe mikate ya mfumu yaikazi ya kumwamba, athirire milungu ina nsembe yothira, kuti autse mkwiyo wanga. 19#Deut. 32.16, 21Kodi autsa mkwiyo wanga? Ati Yehova; kodi sadziutsira okha manyazi a nkhope zao? 20Chifukwa chake, ati Ambuye Mulungu, Taonani, mkwiyo wanga ndi ukali wanga udzathiridwa pa malo ano, pa anthu, ndi pa nyama, ndi pa mitengo ya m'munda, ndi pa zipatso zapansi; ndipo udzatentha osazima.
21 #
Yer. 6.20
Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele; Ikani zopereka zopsereza zanu pa nsembe zophera zanu, nimudye nyama. 22#1Sam. 15.22; Mas. 51.16-17Pakuti sindinanena kwa makolo anu, tsiku lija ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito, ngakhale kuwauza nsembe zopsereza kapena zophera; 23#Deut. 6.3koma chinthu ichi ndinawauza, kuti, Mverani mau anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga; nimuyende m'njira yonse imene ndakuuzani inu, kuti chikukomereni. 24#Mas. 81.11-12Koma sanamvere, sanatchere khutu, koma anayenda m'upo ndi m'kuuma kwa mtima wao woipa, nabwerera chambuyo osayenda m'tsogolo. 25#Yer. 29.19Chiyambire tsiku limene makolo anu anatuluka m'dziko la Ejipito kufikira lero lino, ndatumiza kwa inu atumiki anga onse, aneneri, tsiku ndi tsiku, kuuka mamawa ndi kuwatumiza iwo; 26#Mas. 81.11-12koma sanandimvere Ine sanatchera khutu lao, koma anaumitsa khosi lao; anaipa koposa makolo ao.
27 #
Ezk. 2.7
Ndipo uzinena kwa iwo mau awa onse, koma sadzakumvera iwe; ndipo udzawaitananso; koma sadzakuyankha iwe. 28Ndipo udzati kwa iwo, Umene ndi mtundu wosamvera mau a Yehova Mulungu wao, wosalola kulangizidwa, choonadi chatha, chadulidwa pakamwa pao.
Zoopsa za Tofeti
29 #
Mik. 1.16
Meta tsitsi lako, iwe Yerusalemu, nulitaye, nukweze maliro pa mapiri oti see; pakuti Yehova wakana ndi kusiya mbadwo umene aukwiyira. 30#2Maf. 21.4, 7Pakuti ana a Yuda anachita choipa pamaso panga, ati Yehova; naika zonyansa zao m'nyumba yotchedwa dzina langa, kuti alipitse. 31#2Maf. 23.10Namanga akachisi a ku Tofeti, kuli m'chigwa cha mwana wa Hinomu, kuti atenthe m'moto ana ao aamuna ndi aakazi; chimene sindinauza iwo, sichinalowa m'mtima mwanga. 32#Yer. 19.6Chifukwa chake, taonani, masiku alikudza, ati Yehova, ndipo sadzatchedwanso Tofeti, kapena Chigwa cha mwana wa Hinomu, koma Chigwa cha Kuphera; pakuti adzataya m'Tofeti, kufikira malo akuikamo adzasowa. 33#Deut. 28.26Ndipo mitembo ya anthu awa idzakhala zakudya za mbalame za mlengalenga, ndi za zilombo za dziko lapansi; palibe amene adzaziopsa. 34#Lev. 26.31-33; Ezk. 26.13; Chiv. 18.23Ndipo ndidzaletsa m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, mau akukondwa ndi mau akusekera, ndi mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi; pakuti dziko lidzasanduka bwinja.
Currently Selected:
YEREMIYA 7: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi