YouVersion Logo
Search Icon

YEREMIYA 6

6
Achenjezedwa kuti adani adzamangira Yerusalemu misasa
1 # Yer. 1.14 Ananu a Benjamini, pulumukani pothawa pakati pa Yerusalemu, ombani lipenga m'Tekowa, kwezani chizindikiro m'Betehakeremu; pakuti chaoneka choipa chotuluka m'mpoto ndi kuononga kwakukulu. 2Ndidzachotsa mwana wamkazi wa Ziyoni mkazi wokoma ndi wololopoka. 3Abusa ndi nkhosa zao adzadza kwa iye; adzamanga mahema ao pomzinga iye; adzadya yense pokhala pake. 4Lalikirani nkhondo yakumenyana ndi iye; ukani, tikwere pakati pa usana. Tsoka kwa ife! Pakuti dzuwa lapendeka, mithunzi ya madzulo yatambasuka. 5Ukani, tiyende usiku, tipasule nyumba zake. 6Pakuti Yehova wa makamu atero, Dulani mitengo, unjikani nthumbira pomenyana ndi Yerusalemu; mudzi wakudzalangidwa ndi uwu; m'kati mwake modzala nsautso. 7#Yes. 57.20Monga kasupe atulutsa madzi ake, chomwecho atulutsa zoipa zake; chiwawa ndi kufunkha zimveka m'kati mwake; pamaso panga masiku onse pali kulira ndi mabala. 8Ulangizidwe, Yerusalemu, ungakuchokere moyo wanga, ndingakuyese iwe bwinja, dziko losakhalamo anthu.
9Yehova wa makamu atero, Adzakunkha otsalira a Israele monga mpesa; bweza dzanja lako monga wakutchera mphesa m'madengu ake. 10#Mac. 7.51Ndidzanena ndi yani, ndidzachita mboni kwa yani, kuti amve? Taona khutu lao lili losadulidwa, ndipo sangathe kumva; taona, mau a Yehova awatonzetsa iwo; sakondwera nao. 11Chifukwa chake ndadzala ndi ukali wa Yehova; ndalema ndi kudzikaniza; tsanulirani pa ana a pabwalo, ndi pa masonkhano a anyamata, pakuti ngakhale mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa, okalamba ndi iye amene achuluka masiku ake. 12#Deut. 28.30Nyumba zao zidzasanduka za ena, pamodzi ndi minda yao ndi akazi ao; pakuti ndidzatambasula dzanja langa pa okhala m'dziko, ati Yehova. 13#Yes. 56.11Pakuti kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu onse akhala akusirira; ndiponso kuyambira mneneri kufikira wansembe onse achita monyenga. 14#Ezk. 13.10Ndiponso apoletsa bala la anthu anga pang'onong'ono, ndi kuti, Mtendere, mtendere; koma palibe mtendere. 15#Yer. 3.3Kodi anakhala ndi manyazi pamene anachita chonyansa? Iai, sanakhale konse ndi manyazi, sanathe kunyala; chifukwa chake adzagwa mwa iwo akugwa; panthawi pamene ndidzafika kwa iwo, adzagwetsedwa, ati Yehova.
16 # Mala. 4.4; Mat. 11.29 Yehova atero, Imani m'njira ndi kuona, funsani za mayendedwe akale, m'menemo muli njira yabwino, muyende m'menemo, ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu; koma anati, Sitidzayendamo. 17#Ezk. 3.17Ndipo ndinaika alonda oyang'anira inu, ndi kuti, Mverani mau a lipenga; koma anati, Sitidzamvera. 18Chifukwa chake tamverani, amitundu inu, dziwani, msonkhano inu, chimene chili mwa iwo. 19#Miy. 1.31Tamva, dziko lapansi iwe; taona, Ine ndidzatengera choipa pa anthu awa, chipatso cha maganizo ao, pakuti sanamvere mau anga, kapena chilamulo changa, koma wachikana. 20#Yes. 1.11Lubani andifumiranji ku Sheba, ndi nzimbe ku dziko lakutali? Nsembe zopsereza zanu sizindisekeretsa, nsembe zophera zanu sizindikondweretsa Ine. 21Chifukwa chake atero Yehova, Taona, ndidzaikira anthuwa zophunthwitsa; ndipo atate ndi ana adzakhumudwa nazo pamodzi; munthu ndi mnzake adzatayika.
22 # Yer. 50.41-43 Yehova atero, Taona, mtundu wa anthu uchokera kumpoto; ndi mtundu waukulu adzaukitsidwa ku malekezero a dziko lapansi. 23Agwira uta ndi nthungo; ali ankharwe, alibe chifundo; mau ao aphokosera ngati nyanja, akwera pa akavalo; aguba monga anthu ofuna kumenyana nkhondo ndi iwe, mwana wamkazi wa Ziyoni. 24Tamva ife mbiri yake; manja athu alefuka, yatigwira nkhawa ndi zowawa ngati za mkazi wobala. 25Usatulukire kumunda, usayenda m'njira; pakuti lupanga la amaliwongo ndi mantha ali m'mbali zonse. 26#Est. 4.1Iwe mwana wamkazi wa anthu anga, udziveke ndi chiguduli, ndi kuvimvinika m'phulusa; ulire maliro ngati a mwana wamwamuna wa yekha, kulira kowawa koposa; pakuti wakufunkha adzatifikira ife motidzidzimutsa. 27Ndakuyesa iwe nsanja ndi linga mwa anthu anga, kuti udziwe ndi kuyesa njira yao. 28Onse ali opikisana ndithu, ayendayenda ndi maugogodi; ndiwo mkuwa ndi chitsulo; onsewa achita movunda; 29mvukuto yatenthedwa ndi moto; mtovu watha ndi moto wa ng'anjo; ayenga chabe; pakuti oipa sachotsedwa. 30#Ezk. 22.19-20Anthu adzawatcha nthale ya siliva, pakuti Yehova wakana iwo.

Currently Selected:

YEREMIYA 6: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for YEREMIYA 6